NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA March 2015

M’magazini iyi muli nkhani zophunzila mlungu wa May 4 mpaka May 31, 2015.

MBILI YANGA

Tinapeza Nchito Yopindulitsa Kwambili

David ndi Gwen Cartwright anali kuvinila limodzi kale, koma masiku ano akugwilila limodzi nchito yopindulitsa.

“Munavomeleza Kuti Zimenezi Zicitike”

N’cifukwa ciani zofalitsa zathu zaposacedwapa zakhala zikufotoza nkhani za m’Baibulo m’njila yosavuta ndi yomveka bwino?

Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?

Ŵelengani kuti mudziŵe kamvedwe katsopano ka fanizo la Yesu la anamwali 10 lokhala ndi uthenga wosavuta kumva ndi wofunika kwambili.

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kale zofalitsa zathu zinali kakamba kwambili tanthauzo la zocitika zina zochulidwa m’Baibulo, koma m’zaka za posachedwapa, sizikutelo. N’cifukwa ciani zili conco?

Zimene Tiphunzilapo pa Fanizo la Matalente

Nkhani iyi isintha kamvedwe kathu ka fanizo la matalente.

Kuthandiza Abale a Kristu Mokhulupilika

Kodi anthu amene Kristu adzaweluza kuti ndi nkhosa amathandiza motani abale ake?

Kodi Kukwatiwa “Mwa Ambuye” N’kofunikabe?

Anthu amene ndi ofunitsitsa kutsatila malangizo a Mulungu amakondweletsa mtima wake, ndipo amalandila madalitso a kuuzimu.