NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA February 2015

M’magazini ino muli nkhani zophunzila mlungu wa April 6 mpaka May 3, 2015.

Mphatso Yosangalatsa ya Anthu a ku Japan

Buku latsopano lakuti ‘The Bible—The Gospel According to Matthew’ linatulutsidwa ku Japan. Kodi linalembedwa bwanji? Nanga n’cifukwa ciani linalembedwa?

Khalani Wodzicepetsa ndi Wacifundo Monga Yesu

Lemba la 1 Petulo 2:21 limatilimbikitsa kutsatila mapazi a Yesu mosamala kwambili. Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, kodi tingakhale bwanji odzicepetsa ndi acifundo monga Yesu?

Khalani Wolimba Mtima ndi Wozindikila Monga Yesu

Mwa kuphunzila zimene zinalembedwa m’Baibulo timadziŵa mmene Yesu analili. Phunzilani mmene tingatsatilile mapazi ake mwa kukhala wolimba mtima ndi wozindikila.

Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki

Tikudziŵa kuti kulengeza uthenga wabwino ndi nchito yofunika kwambili imene tiyenela kucita masiku ano. N’ciani cingatithandize kuonjezela cangu cathu mu utumiki wacikristu?

Kukonzekeletsa Anthu ‘Kuphunzila Zokhudza Yehova’

Kodi nchito yolalikila inawayendela bwanji Akristu oyambilila? N’ciani cinathandiza kuti nchito yolalikila ikhale yosavuta m’nthawi ya atumwi kuposa nthawi ina iliyonse m’mbili ya anthu?

Yehova Akutsogolela Nchito Yathu Yophunzitsa Padziko Lonse

N’zinthu zotani zimene zacitika zimene zathandiza atumiki a Yehova kulalikila uthenga wabwino mogwila mtima padziko lapansi?

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Tingaonetse bwanji kuti timaganizila abale ndi alongo amene amadwala akamva fungo la pelefyumu? Ndi pacocitika citi pamene mlongo afunika kuvala cakumutu?

ZA M'NKHOKWE YATHU

“Nyengo Yabwino Koposa”

Magazini ya Zion’s Watch Tower inacha cikumbutso ca imfa ya Kristu kuti “nyengo yabwino koposa,” ndipo inalimbikitsa anthu onse amene anali kuiŵelenga kuti ayenela kucita mwambo umenewo. Kodi Cikumbutso cinali kucitidwa bwanji m’zaka za m’mbuyomu