Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Kuukitsidwa kwa Yesu Kumatanthauza Ciani kwa Ife?

Kodi Kuukitsidwa kwa Yesu Kumatanthauza Ciani kwa Ife?

“Wauka kwa akufa.”—MAT. 28:6.

1, 2. (a) Kodi atsogoleli acipembedzo anali kufuna kudziŵa ciani? Nanga Petulo anayankha motani? (Onani cithunzi pamwamba.) (b) N’cifukwa ciani Petulo analimba mtima panthawiyo?

MASIKU ocepa Yesu ataphedwa, mtumwi Petulo anakumana ndi gulu la mphamvu la anthu otsutsa. Iwo anali atsogoleli acipembedzo Aciyuda amene anacititsa kuti Yesu aphedwe. Pambuyo pakuti Petulo wacilitsa munthu amene anabadwa wolemala, amunawo anafuna kuti Petulo afotokoze kuti anacita zimenezo ndi ulamulilo uti kapena m’dzina la ndani. Molimba mtima, mtumwiyo anayankha kuti: “M’dzina la Yesu Kristu Mnazareti uja, amene inu munam’pacika pamtengo, koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kudzela mwa iyeyo, munthu uyu waimilila pamaso panu atacila bwinobwino.”—Mac. 4:5-10.

2 Izi zisanacitike, Petulo anali atakana Yesu katatu cifukwa ca mantha. (Maliko 14:66-72) Nanga n’cifukwa ciani analimba mtima pamaso pa atsogoleli acipembedzo? Mzimu woyela unam’thandiza, ndipo nayenso anatsimikiza kuti Yesu anaukadi. N’cifukwa ciani mtumwi ameneyu anali wotsimikiza kuti Yesu ali moyo? Nanga n’cifukwa ciani nafenso ndife otsimikiza?

3, 4. (a) Ndi anthu ati amene anaukitsidwa atumwi a Yesu anasabadwe? (b) Nanga ndi anthu ati amene Yesu anaukitsa?

 3 Nkhani ya kuuka kwa akufa sinali yacilendo kwa atumwi a Yesu, cifukwa anthu ena anaukitsidwapo io asanabadwe. Iwo anali kudziŵa kuti Mulungu anathandiza mneneli Eliya ndi Elisa kucita zozizwitsa zimenezo. (1 Maf. 17:17-24; 2 Maf. 4:32-37) Ndipo nthawi ina munthu wina anauka pamene thupi lake linaponyedwa m’manda ndi kukhudza mafupa a Elisa. (2 Maf. 13:20, 21) Akristu oyambilila anali kukhulupilila nkhani za m’Malemba zimenezi, monga mmene ife timakhulupilila kuti Mau a Mulungu ndi oona.

4 Mwacionekele, tonse timakhudzika mtima tikaŵelenga nkhani za anthu amene Yesu anaukitsa. Pamene iye anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wa masiye, mai ameneyu ayenela kuti anadabwa kwambili. (Luka 7:11-15) Panthawi ina Yesu anaukitsa kamtsikana ka zaka 12. Ganizilani cimwemwe cimene makolo ake anakhala naco pamene anaona kuti mwana wao alinso ndi moyo. (Luka 8:49-56) Ndiponso ziyenela kuti zinali zokondweletsa kwambili kwa khamu la anthu, limene linaona Lazaro akutuluka m’manda wamoyo, ndipo ali bwinobwino.—Yoh. 11:38-44.

CIFUKWA CAKE KUUKA KWA YESU KUNALI KWAPADELA

5. Kuukitsidwa kwa Yesu kunasiyana motani ndi kuukitsidwa kwa anthu ena m’mbuyomo?

5 Atumwi anadziŵa kuti kuuka kwa Yesu kunali kosiyana ndi kwa anthu akale amene anaukitsidwapo. Anthu amenewo anaukitsidwa ndi matupi aumunthu, ndiyeno pambuyo pake anafanso. Koma Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu limene silingafe. (Ŵelengani Machitidwe 13:34.) Petulo analemba kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” Tsopano “iye ali kudzanja lamanja la Mulungu, pakuti anapita kumwamba, ndipo angelo, maulamulilo, ndi mphamvu zinakhala pansi pake.” (1 Pet. 3:18-22) Ziukililo zoyamba zinali zocititsa cidwi, koma siziposa ciukililo capadela cimeneci.

6. Kodi kuukitsidwa kwa Yesu kunawakhudza bwanji ophunzila ake?

6 Kuukitsidwa kwa Yesu kunawakhudza kwambili ophunzila ake. Iye sanali wakufa monga mmene adani ake anali kuganizila. Yesu anali ndi moyo monga colengedwa cauzimu camphamvu cimene munthu sangaphe. Ciukililo cake cinali umboni wakuti iye analidi Mwana wa Mulungu. Cifukwa ophunzila ake anadziŵa kuti iye ali moyo, io sanakhalenso ndi cisoni kapena kucita mantha. Koma anakhala acangu ndi olimba mtima. Ngati Yesu sanaukitsidwe, cifuno ca Mulungu cikanalephela ndipo uthenga wabwino umene io anali kulalikila ukanakhala wopanda phindu.

7. Kodi Yesu akucita ciani tsopano? Nanga pamenepa pabuka mafunso otani?

7 Pokhala atumiki a Yehova, timadziŵa kuti Yesu anali munthu wapadela kwambili. Iye ali moyo ndipo akutsogolela pa nchito imene imakhudza munthu aliyense padziko lapansi. Popeza Yesu Kristu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu wa kumwamba, posacedwapa adzacotsa zoipa zonse padziko lapansi. Ndipo adzasandutsa dziko kukhala paladaiso kuti anthu akakhalemo kwamuyaya. (Luka 23:43) Ngati Yesu sanaukitsidwe, zonsezi sizikanatheka. Kodi pali zifukwa zotani zokhulupilila kuti iye anaukitsidwa kwa akufa? Nanga kuukitsidwa kwake kuli ndi tanthauzo lotani kwa ife?

YEHOVA ANAGONJETSA IMFA

8, 9. (a) N’cifukwa ciani atsogoleli Aciyuda anapempha kuti akhwimitse citetezo pa manda a Yesu? (b) Nanga n’ciani cinacitika pamene akazi anafika kumanda?

8 Yesu ataphedwa, ansembe aakulu ndi  Afarisi anapita kwa Pilato ndi kunena kuti: “Bwana, ife takumbukila kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapita masiku atatu ndidzauka.’ Conco lamulani kuti akhwimitse citetezo pamandapo kufikila tsiku lacitatu, kuti ophunzila ake asabwele kudzamuba ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti cinyengo cotsilizaci cidzakhala coipa kwambili kuposa coyamba cija.” Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nao asilikali olondela. Pitani kakhwimitseni citetezo monga mmene mukudziŵila.” Iwo anacitadi zimenezo.—Mat. 27:62-66.

9 Thupi la Yesu linaikidwa m’manda osemedwa m’thanthwe, ndipo anatseka khomo la manda amenewo ndi cimwala cacikulu. Atsogoleli acipembedzo Aciyuda, anafuna kuti Yesu akhalebe wakufa m’manda mmenemo kwamuyaya. Koma Yehova anali ndi maganizo osiyana. Patsiku lacitatu pamene Mariya Mmagadala ndi Mariya wina uja anabwela kudzaona manda, anapeza kuti mngelo wagubuduza cimwala ndipo wakhalapo. Mngeloyo anauza akazi amenewo kuloŵa mkati kuti atsimikizile kuti munalibe munthu. Mngelo anawauza kuti, “Iye sali pano cifukwa wauka kwa akufa.” (Mat. 28:1-6) Yesu anali wamoyo.

10. Ndi umboni wotani umene Paulo anapeleka ponena za kuuka kwa Yesu?

10 Zinthu zimene zinacitika masiku 40 pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, zinapeleka umboni wotsimikizilika. Pofotokoza mwacidule za umboni umenewo, mtumwi Paulo analembela Akristu a ku Korinto kuti: “Mwa zinthu zofunika kwambili zimene ndinakupatsilani zija, zimenenso ineyo ndinalandila, panali zonena kuti, Kristu anafela macimo athu, malinga ndi Malemba. Ndiponso kuti anaikidwa m’manda, kenako anaukitsidwa tsiku lacitatu, mogwilizana ndi Malemba. Panalinso zoti anaonekela kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja. Ndiyeno anaonekelanso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambili a io akali ndi moyo mpaka lelo, koma ena anagona mu imfa. Kenako anaonekela kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizila pake anaonekela kwa ine, ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.”— 1 Akor. 15:3-8.

CIFUKWA CAKE TIMAKHULUPILILA KUTI YESU ANAUKITSIDWA

11. Zinatheka bwanji kuti kuuka kwa Yesu kucitike “malinga ndi Malemba”?

11 Cifukwa coyamba cimene timakhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’cakuti kuuka kwake kunacitika “malinga ndi Malemba.” Mau a Mulungu anakambilatu za kuuka kwake. Mwacitsanzo, Davide analemba kuti “wokhulupilika” wamkulu wa Mulungu sadzasiidwa m’Manda. (Ŵelengani Salimo 16:10.) Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., mtumwi Petulo anakamba kuti mau amenewa anali kukamba za Yesu pamene anati: “[Davide] anaonelatu zapatsogolo ndi kunenelatu za kuuka kwa Kristu. Ananenelatu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.”—Mac. 2:23-27, 31.

12. Ndani anaona Yesu woukitsidwayo?

12 Cifukwa caciŵili cimene timakhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’cakuti tili ndi umboni wa anthu ambili. Kwa masiku 40, Yesu woukitsidwayo anaonekela kwa ophunzila ake m’munda umene unali pafupi ndi manda ake. Anaonekelanso kwa ophunzila ena panjila ya ku Emau ndi kumalo ena. (Luka 24:13-15) Pa zocitika zimenezo, iye anakamba ndi aliyense payekha kuphatikizapo Petulo, ndipo pambuyo pake anakamba ndi gulu la anthu. Kamodzi iye anaonekela kwa khamu la anthu oposa 500. Sitingakane umboni wakuti anthu ambili anaona Yesu woukitsidwayo.

13. Kodi cangu ca ophunzila a Yesu cinaonetsa bwanji kuti anali otsimikiza kuti Yesu anaukitsidwa?

 13 Cifukwa cacitatu cimene timakhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’cakuti ophunzila ake analalikila mwacangu za kuuka kwake. Ngati nkhani ya kuukitsidwa kwa Yesu inali yopanda umboni, n’cifukwa ciani Petulo anaika moyo wake paciswe? N’cifukwa ciani iye analengeza za kuukitsidwa kwa Kristu kwa atsogoleli acipembedzo amene anazonda Yesu ndi kucititsa kuti aphedwe? Cinali cifukwa cakuti Petulo ndi ophunzila ena anali otsimikiza kuti Yesu anali moyo, ndi kuti anali kutsogolela nchito imene Mulungu anafuna kuti icitike. Ndiponso, ciukililo ca Yesu cinapeleka ciyembekezo kwa otsatila ake kuti naonso adzaukitsidwa. Mwacitsanzo, Sitefano anafa ali ndi cikhulupililo cakuti akufa adzauka.—Mac. 7:55-60.

14. N’cifukwa ciani timakhulupilila kuti Yesu ali moyo?

14 Cifukwa cacinai cimene timakhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’cakuti tili ndi umboni wakuti iye akulamulila monga Mfumu, ndipo akutumikila monga Mutu wa mpingo wacikristu. Zotsatilapo n’zakuti Akristu oona aonjezeka. Kodi izi zikanacitika ngati Yesu sanaukitsidwe kwa akufa? Ngati sanaukitsidwe sitikanamva za iye. Koma tili ndi zifukwa zomveka zokhulupilila kuti Yesu ali moyo, ndi kuti tsopano akutitsogolela pamene tilengeza uthenga wabwino padziko lonse.

ZIMENE KUUKITSIDWA KWA YESU KUMATANTHAUZA KWA IFE

15. N’cifukwa ciani kuuka kwa Yesu kumatithandiza kuti tizilalikila molimba mtima?

15 Kuuka kwa Kristu kumatithandiza kuti tizilalikila molimba mtima. Kwa zaka 2,000, adani a Mulungu ayesa kuti alepheletse kulengezedwa kwa uthenga wabwino. Iwo amagwilitsila nchito mpatuko, citsutso, anthu aciwawa, ziletso, cizunzo, ndi kupha. Komabe, palibe ‘cida cimene cingapangidwe’ cimene cidzalepheletsa nchito yolalikila za Ufumu ndi kupanga ophunzila. (Yes. 54:17) Sitimamuopa Satana ndi anthu ake. Monga mmene Yesu analonjezela, iye ali nafe kuti atithandize. (Mat. 28:20) Tili ndi cidalilo cakuti, kaya adani athu acite zotani sangatiletse kulalikila.

Kuuka kwa Yesu kumatithandiza kulalikila molimba mtima (Onani ndime 15)

16, 17. (a) Kodi ciukililo cimatsimikizila bwanji kuti zimene Yesu anaphunzitsa n’zoona? (b) Malinga ndi Yohane 11:25, ndi mphamvu zotani zimene Mulungu anapatsa Yesu?

16 Kuuka kwa Yesu kumatsimikizila kuti zimene anaphunzitsa n’zoona. Paulo analemba kuti ngati Kristu sanaukitsidwe, ndiye kuti cikhulupililo ca Akristu ndi zimene amalalikila n’zopanda phindu. Katswili wina wa Baibulo analemba kuti: “Ngati Kristu sanaukitsidwe, . . . ndiye kuti Akristu ndi anthu opusa kwambili amene amakhulupilila cinyengo cacikulu.” Ngati Yesu sanaukitsidwe, ndiye kuti Uthenga wabwino wonena za munthu wabwino ndi wanzelu, amene anaphedwa ndi adani ake ndi wopanda phindu. Koma Kristu anaukitsidwa, ndipo zimenezi zinatsimikizila kuti zimene anaphunzitsa ndi zimene anakamba ponena za mtsogolo n’zoona.—Ŵelengani 1 Akorinto 15:14, 15, 20.

17 Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupilila mwa ine, ngakhale amwalile, adzakhalanso ndi moyo.” (Yoh. 11:25) Lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwa. Yehova wapatsa Yesu mphamvu zoukitsa anthu amene ali ndi ciyembekezo cakumwamba. Ndipo adzaukitsanso mabiliyoni a anthu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi. Nsembe ya Yesu ndi kuuka kwake zimatsimikizila kuti imfa idzatha. Conco, kudziŵa zimenezi kungatithandize kupilila mayeselo alionse ndi kusaopa imfa.

18. Kodi kuuka kwa Yesu kumatsimikizila ciani?

18 Kuuka kwa Yesu kumatitsimikizila  kuti anthu amene adzakhala padziko lapansi adzaweluzidwa mogwilizana ndi miyezo yacikondi ya Yehova. Pokamba ndi anthu a ku Atene wakale, Paulo anati: “[Mulungu] wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweluza m’cilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzela mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapeleka citsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa kwa akufa.” (Mac. 17:31) Mulungu anasankha Yesu kukhala Woweluza wathu, ndipo tili ndi cidalilo cakuti adzaweluza mwacilungamo ndi mwacikondi.—Ŵelengani Yesaya 11:2-4.

19. Kodi kukhulupilila kuti Kristu anauka kumatikhudza bwanji?

19 Kukhulupilila kuti Yesu anauka kumatilimbikitsa kucita cifunilo ca Mulungu. Ngati Yesu sanafe ndi kuuka, sitikanamasulidwa ku cilango ca ucimo ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Ngati Yesu sanauke, nafenso tingakambe kuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti maŵa tifa.” (1 Akor. 15:32) Sitimaika maganizo athu pa zosangulutsa, m’malo mwake timayamikila ciyembekezo ca ciukililo. Ndipo tili ndi zifukwa zomveka zotsatilila malangizo a Yehova paumoyo wathu wonse.

20. Kuuka kwa Yesu kumaonetsa bwanji kuti Mulungu ali ndi mphamvu?

20 Kuuka kwa Kristu kumapeleka umboni wosatsutsika wakuti Yehova ndi wamphamvu, ndipo “amapeleka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Yehova anagwilitsila nchito mphamvu ndi nzelu kuti aukitse Yesu ku moyo wosafa wa kumwamba. Ndiponso, Mulungu anaonetsa kuti ali ndi mphamvu zokwanilitsa malonjezo ake onse. Zimenezi ziphatikizapo ulosi wonena za lonjezo lakuti “mbeu” yapadela idzathetsa nkhani ya ulamulilo wa cilengedwe conse. Koma kuti lonjezo limeneli likwanilitsidwe, Yesu anafunikila kufa ndi kuukitsidwa.—Gen. 3:15.

21. Kodi ciyembekezo ca ciukililo cili ndi tanthauzo lotani kwa inu?

21 Timayamikila Yehova cifukwa cotipatsa ciyembekezo cakuti tidzauka. Baibulo limalonjeza kuti: “Taonani! Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nao, ndipo io adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nao. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Lonjezo lokondweletsa limeneli linapelekedwa kwa mtumwi wokhulupilika Yohane, amene anauzidwa kuti: “Lemba, pakuti mau awa ndi odalilika ndi oona.” (Chiv. 1:1; 21:3-5) Ndani anauza Yohane kulemba mau amenewa? Ndi Yesu Kristu woukitsidwayo.Chiv. 1:1; 21:3-5.