Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ikani Maganizo Anu pa Zinthu Zakumwamba”

“Ikani Maganizo Anu pa Zinthu Zakumwamba”

“Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko.”—AKOL. 3:2.

1, 2. (a) N’ciani cionetsa kuti mpingo wa m’nthawi ya atumwi ku Kolose unali pa mavuto? (b) Ndi malangizo ati amene anathandiza abale a ku Kolose kukhalabe olimba?

MPINGO wacikristu wa m’nthawi ya atumwi ku Kolose unali pa mavuto. Ena mumpingo anayambitsa magaŵano mwa kulimbikitsa anthu kutsatila Cilamulo ca Mose. Ndipo ena anali kulimbikitsa ciphunzitso cakuti kucitako zosangulutsa paumoyo ndi kulakwa. Potsutsa ziphunzitso zabodza zimenezi, mtumwi Paulo analemba kalata yolimbikitsa, pocenjeza abale a ku Kolose kuti: “Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Kristu.”—Akol. 2:8.

2 Ngati Akristu odzozedwa amenewo anali kuika maganizo ao pa “mfundo zimene ndi maziko a moyo wa m’dzikoli,” zikanaonetsa kuti anakana njila ya Yehova yopulumutsila anthu. (Akol. 2:20-23) Kuti Paulo awathandize kuteteza ubale wao wamtengo wapatali ndi Mulungu, anawalimbikitsa kuti: “Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko.” (Akol. 3:2) Ndithudi, abale a Kristu anafunikila kuika  m’maganizo coloŵa cao cosaonongeka cimene ‘anawasungila kumwamba.’—Akol. 1:4, 5.

3. (a) Ndi ciyembekezo cotani cimene Akristu odzozedwa amaika m’maganizo? (b) Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

3 Masiku ano, Akristu odzozedwa naonso amaika maganizo ao pa Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndi pa ciyembekezo cao codzakhala “olandila coloŵa anzake a Kristu.” (Aroma 8:14-17) Nanga bwanji za anthu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi? Kodi mau a Paulo amawakhudza bwanji? Nanga a “nkhosa zina” angaike motani maganizo ao pa “zinthu zakumwamba”? (Yoh. 10:16) Abulahamu ndi Mose anaika maganizo ao pa zinthu zakumwamba, ngakhale panthawi zovuta. Nanga tingatsatile bwanji citsanzo cao?

ZIMENE KUIKA MAGANIZO ATHU PA ZINTHU ZAKUMWAMBA KUMATANTHAUZA

4. Kodi a nkhosa zina angacite ciani kuti aike maganizo ao pa zinthu zakumwamba?

4 Ngakhale kuti a nkhosa zina alibe ciyembekezo ca kumwamba, naonso angaike maganizo ao pa zinthu zakumwamba. Angacite bwanji zimenezo? Angacite zimenezo mwa kuika Yehova Mulungu ndi Ufumu wake patsogolo mu umoyo wao. (Luka 10:25-27) Ndiye cifukwa cake, timatsatila citsanzo ca Kristu. (1 Pet. 2:21) Mofanana ndi Akristu a m’nthawi ya atumwi, nafenso tingakhudzidwe ndi maganizo onama, nzelu zadziko, ndi kukonda cuma m’dongosolo ili la Satana. (Ŵelengani 2 Akorinto 10:5.) Pokhala otsatila a Yesu, tiyenela kukhala maso kuti tiziteteze ku misampha imene ingationonge mwa kuuzimu.

5. Tingacitenji kuti tidziŵe ngati timakondetsetsa cuma?

5 Kodi mzimu wa dziko wokonda cuma watiyambukila? Nthawi zambili, zimene timakonda zimaonetsa zimene zili mumtima ndi m’maganizo mwathu. Yesu anati: “Kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:21) Kuti tidziŵe zimene zili mumtima mwathu, ndi bwino kudzifufuza nthawi zonse. Tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi zonse zoganiza zanga zimakhala pa ndalama? Kapena ndimangoganizila zamalonda ndi kupeza umoyo wabwino? Kodi ndimayesetsa kukhala ndi diso lolunjika pa zinthu za kuuzimu?’ (Mat. 6:22) Yesu anaonetsa kuti anthu amene amafunitsitsa “kudziunjikila cuma padziko,” amaononga ubale wao ndi Mulungu.—Mat. 6:19, 20, 24.

6. Tingapambane bwanji pankhondo yolimbana ndi zilakolako zathupi?

6 Kupanda ungwilo kwathu kungatisonkhezele kucita zinthu zoipa. (Ŵelengani Aroma 7:21-25.) Ngati tilibe thandizo la mzimu woyela wa Mulungu, tingagonje ku “nchito za mdima.” Zimenezi ziphatikizapo “maphwando aphokoso ndi kumwa mwaucidakwa . . . ciwelewele ndi khalidwe lotailila.” (Aroma 13:12, 13) Kuti tipambane pankhondo yolimbana ndi “zinthu zapadziko,” zimene ndi zilakolako zathupi, tifunikila kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba. Kucita zimenezi kumafuna khama, ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anati: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolela ngati kapolo.” (1 Akor. 9:27) Motelo, kuti tikhalebe pa mpikisano wokalandila moyo, tiyenela kusamala ndi zimene timacita. Tsopano, tiyeni tikambilane zimene amuna aŵili okhulupilika akale anacita kuti ‘akondweletse Mulungu.’—Aheb. 11:6.

ABULAHAMU “ANAKHULUPILILA MWA YEHOVA”

7, 8. (a) Abulahamu ndi Sara anakumana ndi mavuto otani? (b) Nanga Abulahamu anaika maganizo ake pa ciani?

7 Pamene Yehova anauza Abulahamu ndi banja lake kuti acoke ndi kupita  ku Kanani, iye anamvela ndi mtima wonse. Cifukwa cakuti Abulahamu anali wokhulupilika ndi womvela, Yehova anacita naye pangano pamene anati: “Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa.” (Gen. 12:2) Panapita zaka zambili, koma Abulahamu ndi mkazi wake, Sara, anali asanakhale ndi mwana. Kodi Yehova anaiŵala zimene analonjeza Abulahamu? Ndipo panthawi imeneyo, umoyo unali wovuta ku Kanani. Abulahamu ndi banja lake anasiya nyumba yao ndi acibale ao ena ku Uri, mzinda wotukuka wa ku Mesopotamiya. Kuti afike ku Kanani, io anayenda mtunda wa makilomita 1,600. Kumeneko anali kukhala m’matenti, anapilila ndi njala, ndipo anakumana ndi acifwamba. (Gen. 12:5, 10; 13:18; 14:10-16) Ngakhale n’conco, io sanaganize zobwelela ku umoyo wabwino ku Uri.—Ŵelengani Aheberi 11:8-12, 15.

8 M’malo moika maganizo ake pa “zinthu zapadziko,” Abulahamu “anakhulupilila mwa Yehova.” (Gen. 15:6) Iye anaika maganizo ake pa zinthu zakumwamba mwa njila yakuti anali kuganizila za malonjezo a Mulungu. Zotsatilapo zake n’zakuti Mulungu Wam’mwambamwamba anam’dalitsa. Iye anaonekela kwa Abulahamu ndi kumuuza kuti: “‘Kweza maso ako kumwamba, uŵelenge nyenyezizo ngati ungathe kuziŵelenga.’ Ndipo anamuuzanso kuti: ‘Umu ndi mmene mbeu yako idzakhalile.’” (Gen. 15:5) Zimenezo ziyenela kuti zinam’limbikitsa kwambili. Nthawi zonse Abulahamu akayang’ana nyenyezi kumwamba, anali kukumbukila lonjezo la Yehova lakuti adzaculukitsa mbeu yake. Panthawi yake, Mulungu anapatsa Abulahamu mwana monga mmene anam’lonjezela.—Gen. 21:1, 2.

9. Kutsatila citsanzo ca Abulahamu kungatithandize bwanji kupitilizabe kutumikila Mulungu?

9 Mofanana ndi Abulahamu, nafenso tiyembekezela kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Mulungu. (2 Pet. 3:13) Ngati sitiika maganizo athu pa zinthu zakumwamba, tingaone monga kuti malonjezo akucedwa kukwanilitsika. Ndipo zingacititse kuti tibwelele m’mbuyo kuuzimu. Mwacitsanzo, kodi m’mbuyomu munasintha zinthu zina kuti muyambe upainiya kapena kuti muonjezele utumiki wanu? Ngati n’conco, tikuyamikilani kwambili. Nanga mucita bwanji tsopano? Musaiŵale kuti Abulahamu anaika maganizo ake pa “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:10) Iye “anakhulupilila mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”—Aroma 4:3.

MOSE ANAONA “WOSAONEKAYO”

10. Kodi Mose anali ndi umoyo wotani ali mnyamata?

10 Munthu wina amene anaika maganizo ake pa zinthu zakumwamba ndi Mose. Ali mnyamata, iye “anaphunzila nzelu zonse za Aiguputo.” Amenewa sanali maphunzilo wamba. Iye analeledwa m’banja lacifumu la Aiguputo, pamene Iguputo unali ulamulilo wamphamvu koposa padziko lonse. Maphunzilo apamwamba amenewo anacititsa Mose kukhala “wamphamvu m’mau ndi m’zocita zake.” (Mac. 7:22) Ganizilani mwai umene Mose akanakhala nao. Ngakhale n’conco, iye anaika maganizo ake pa zinthu zofunika kwambili, zimene ndi kucita cifunilo ca Mulungu.

11, 12. Ndi maphunzilo otani amene Mose anaona kuti ndi apamwamba? Nanga tidziŵa bwanji?

11 Pamene Mose anali mwana, amai ake a Yokebedi, anam’phunzitsa za Mulungu wa Aheberi. Mose anaona kuti kudziŵa Yehova kunali kofunika kwambili kuposa cuma ciliconse. Conco, iye anakana udindo ndi mwai umene akanakhala nao cifukwa cokhala m’banja la Farao. (Ŵelengani Aheberi 11:24-27.) Ndithudi, maphunzilo  a kuuzimu ndi kukhulupilila Yehova, zinam’thandiza kuika maganizo ake pa zinthu zakumwamba.

12 Mose analandila maphunzilo akuthupi apamwamba kwambili amene analipo panthawiyo. Koma kodi anawagwilitsila nchito kuti achuke mu Iguputo, adzipangile dzina, kapena kupeza cuma cakuthupi? Iyai. Baibulo limati iye “anakana kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mocita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zaucimo.” Mosapita m’mbali, Mose anagwilitsila nchito maphunzilo a kuuzimu kupititsa patsogolo cifunilo ca Yehova.

13, 14. (a) N’ciani cinathandiza Mose kuti ayenelele nchito imene Yehova anam’patsa? (b) Mofanana ndi Mose, kodi tiyenela kucita ciani?

13 Mose anali kuganizila kwambili za Yehova ndi anthu ake. Atafika zaka 40, iye anaona kuti angakwanitse kumasula anthu a Mulungu ku ukapolo mu Iguputo. (Mac. 7:23-25) Komabe, Yehova asanam’patse nchito imeneyo, Mose anafunikila kuphunzila zambili. Anafunikila kukulitsa makhalidwe monga kudzicepetsa, kuleza mtima, kufatsa, ndi kudziletsa. (Miy. 15:33) Mose anafunikila kuphunzila kuti akonzekele mavuto amtsogolo. Zaka 40 zimene iye anali m’busa, zinam’thandiza kukulitsa makhalidwe amenewa.

14 Kodi kukhala m’busa kunali ndi zotsatilapo zabwino kwa Mose? Inde. Mau a Mulungu amati iye anakhala “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Anakulitsa khalidwe la kudzicepetsa, limene linam’thandiza kucita zinthu modekha ndi anthu osiyanasiyana, ndiponso pa nkhani zovuta. (Eks. 18:26) Nafenso tiyenela kukulitsa makhalidwe a kuuzimu kuti tikapulumuke ‘cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:14) Kodi timagwilizana ndi anthu onse, kuphatikizapo aja amene timaona kuti ndi a mtima wapacala? Mau a mtumwi Petulo angatithandize pankhaniyi. Iye anati: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale.”—1 Pet. 2:17.

KUIKABE MAGANIZO ATHU PA ZINTHU ZAKUMWAMBA

15, 16. (a) N’cifukwa ciani kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba n’kofunika? (b) Nanga n’cifukwa ciani kukhala ndi khalidwe labwino n’kofunika kwa Akristu?

15 Tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta.’ (2 Tim. 3:1) Conco, kuti tikhalebe maso kuuzimu tifunika kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba. (1 Ates. 5:6-9) Tiyeni tikambilane njila zitatu za mmene tingacitile zimenezi.

16 Khalidwe lathu: Petulo anazindikila kuti khalidwe labwino n’lofunika kwambili. Iye anati: “Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti . . . pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zocita zanu zabwino, adzatamande Mulungu.” (1 Pet. 2:12) Kaya tili pa nyumba, ku nchito, kusukulu, pa zosangulutsa kapena mu ulaliki, tiyenela kuyesetsa kulemekeza Yehova ndi khalidwe lathu labwino. N’zoona, pokhala anthu opanda ungwilo, tonse timalakwa. (Aroma 3:23) Koma mwa kupitiliza “kumenya nkhondo yabwino yosunga cikhulupililo,” tingapambane pankhondo yolimbana ndi matupi athu opanda ungwilo.—1 Tim. 6:12.

17. Tingawatsatile motani maganizo amene Kristu Yesu anali nao? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

17 Maganizo athu: Kuti tikhale ndi khalidwe labwino, tiyenela kukhala ndi maganizo oyenela. Mtumwi Paulo anati: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Kristu Yesu anali nao.” (Afil. 2:5) Kodi Yesu anali ndi khalidwe lotani? Iye anali wodzicepetsa. Ndipo kudzicepetsa kumeneku  kunamuthandiza kucita zambili mu ulaliki. Nthawi zonse, iye anali kuganizila zolalikila ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Maliko 1:38; 13:10) Yesu anagwilitsila nchito Mau a Mulungu pophunzitsa. (Yoh. 7:16; 8:28) Iye anali kuphunzila Malemba mwakhama kuti aziwagwila mau, kuwateteza, ndi kuwafotokoza bwino. Ngati ndife odzicepetsa ndi acangu mu ulaliki, ndipo ngati timacita phunzilo laumwini, tidzakhala ndi maganizo monga a Kristu.

Nthawi zonse Yesu anali kuganizila zolalikila ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu (Onani ndime 17)

18. Tingathandizile motani pa nchito yofunika ya Yehova?

18 Thandizo lathu: Cifunilo ca Yehova n’cakuti ‘onse akumwamba, ndi apadziko lapansi,’ apinde maondo ao. (Afil. 2:9-11) Ngakhale kuti Yesu anali ndi udindo waukulu, modzicepetsa anagonjela kwa Atate wake. Nafenso tiyenela kucita cimodzimodzi. (1 Akor. 15:28) Nanga tingacite motani zimenezi? Tingacite zimenezi pamene ndi mtima wonse tigwila nchito ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila.’ (Mat. 28:19) Ndiponso timafuna ‘kucitila onse zabwino,’ makamaka abale athu ndi anzathu.—Agal. 6:10.

19. Tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

19 Timayamikila kwambili kuti Yehova amatiuza kuti tiike maganizo athu pa zinthu zakumwamba. Ndiye cifukwa cake, tiyenela ‘kuvula colemela ciliconse ndi . . . kuthamanga mopilila mpikisano umene atiikila.’ (Aheb. 12:1) Conco, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kugwila nchito ndi ‘moyo wathu wonse ngati kuti tikucitila Yehova.’ Tikatelo, Atate wathu wakumwamba adzadalitsa khama lathu.—Akol. 3:23, 24.