NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA August 2014

Magazini ino ili ndi nkhani zophunzila za September 29 mpaka October 26, 2014.

Kodi Mumalandila “Cakudya pa Nthawi Yoyenela”?

Kuti munthu akhale wolimba kuuzimu, kodi ayenela kuŵelenga zinthu zonse zimene kapolo wokhulupilika amatipatsa?

Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova

Phunzilani mmene kupanduka kumakhudzila amuna ndi akazi. Phunzilani zimene akazi ena okhulupilika anacita m’nthawi zakale. Ndiponso, phunzilani mmene akazi acikristu amacilikizila nchito ya Mulungu masiku ano.

Gwilitsilani Nchito Mau a Mulungu​—Ndi Amoyo

Mboni zonse za Yehova zimafuna kulalikila mogwila mtima. Onani njila zothandiza za mmene tingagwilitsile nchito Mau a mphamvu a Mulungu ndi tumapepala twauthenga pokambilana ndi anthu.

Mmene Yehova Amayandikila kwa Ife

Tiyenela kukhala paubale wabwino ndi Yehova. Phunzilani mmene dipo ndi Baibulo zionetsela kuti Yehova amatikokela kwa iye.

Muzimvetsela Mau a Yehova Kulikonse Kumene Mungakhale

Phunzilani cifukwa cake n’kofunika kumvetsela mau a Yehova ndi kulankhula naye. Nkhani ino idzatithandiza kudziŵa mmene tingapewele kulola Satana ndi zilakolako za uchimo kutilepheletsa kumvetsela kwa Yehova.

‘Bwelelani Mukalimbikitse Abale Anu’

Ngati m’bale kale anali kutumikila monga mkulu koma tsopano salinso, kodi iye angayambenso ‘kuyesetsa kuti akhalenso woyang’anila’?

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Pamene Yesu anakamba kuti anthu amene adzaukitsidwa “sadzakwatila kapena kukwatiwa,” kodi anali kukamba za ciukililo ca padziko lapansi?

ZA M'NKHOKWE YATHU

“Seŵelo la Eureka” Linathandiza Ambili Kuphunzila Coonadi

Seŵelo lacidule limeneli locokela ku “Seŵelo la Cilengedwe” linali kuonetsedwa m’midzi ngakhale popanda malaiti.