NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA July 2014

Magazini ino ili ndi nkhani zophunzila za September 1 mpaka 28, 2014.

Anadzipeleka Mofunitsitsa​—ku Micronesia

Anthu ocokela ku maiko ena amene akutumikila pa zilumba za Pacific amakumana ndi mavuto atatu ofanana. Nanga n’ciani cathandiza alengezi a Ufumu amenewa kugonjetsa mavutowo?

“Yehova Amadziŵa Anthu Ake”

Kodi ‘maziko’ ndi ‘cidindo’ zochulidwa pa 2 Timoteyo 2:19 zimatithandiza bwanji kudziŵa anthu a Yehova?

Anthu a Yehova “Aleke Kucita Zosalungama”

Mau akuti ‘kuleka kucita zosalungama’ agwilizana bwanji ndi zocitika za m’nthawi ya Mose? Tiphunzilapo ciani pa zocitika zimenezo?

MBILI YANGA

Kutaikilidwa Atate​—Kupeza Atate

Ŵelengani mbili ya m’bale Gerrit Lösch, wa m’Bungwe Lolamulila.

“Inu Ndinu Mboni Zanga”

Kodi kudziŵika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova kumatanthauzanji?

“Mudzakhala Mboni Zanga”

N’cifukwa ninji Yesu anati “mudzakhala mboni zanga,” osati mboni za Yehova? Tingacite ciani kuti tipitilize kucitila umboni mwacangu?