Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi pa Zozizwitsa Zayesu Mungaphunzilepo Ciani?

Kodi pa Zozizwitsa Zayesu Mungaphunzilepo Ciani?

Kodi pa Zozizwitsa Zayesu Mungaphunzilepo Ciani?

MUNGADABWE kudziŵa kuti m’nkhani za m’Baibo za moyo wa Yesu padziko lapansi mulibe mawu acinenelo coyambilila akuti “cozizwitsa.” Mawu a Cigiriki (dyʹna·mis) amene nthawi zina awamasulila kuti “cozizwitsa” kwenikweni amatanthauza “mphamvu.” (Luka 8:46) Tingawamasulilenso kuti “nzelu” kapena “nchito zamphamvu.” (Mateyu 11:20; 25:15) Malinga na zimene katswili wina ananena, mawu a Cigiriki amenewa “amanena za nchito yaikulu imene yacitika, ndipo amanena maka-maka mphamvu imene yacititsa nchitoyo. Amasonyeza kuti nchitoyo yacitika mwa mphamvu ya Mulungu.”

Mawu ena a Cigiriki (teʹras) nthawi zambili amawamasulila kuti “zodabwitsa” kapena “zozizwa.” (Yohane 4:48; Machitidwe 2:19) Mawu amenewa amasonyeza maka-maka zimene anthu amacita akaona zimenezo. Kaŵili-kaŵili, anthu ambili oonelela ndiponso ophunzila a Yesu anali kudabwa na kuzizwa akaona nchito zamphamvu zimene Yesu anali kucita.—Marko 2:12; 4:41; 6:51; Luka 9:43.

Mawu acitatu a Cigiriki (se·meiʹon) onena za zozizwitsa za Yesu amatanthauza “cizindikilo.” Katswili wina wamaphunzilo Robert Deffinbaugh anati mawu amenewa “amasonyeza tanthauzo lenileni la cozizwitsa.” Ananenanso kuti: “Cizindikilo ndico cozizwitsa cimene cimathandiza kumvetsa coonadi cinacake conena za Ambuye wathu Yesu.”

Kodi Anali kunyengeza Anthu Kapena Anali na Mphamvu Yocokela kwa Mulungu?

Baibo silimanena kuti zozizwitsa za Yesu zinali zongopusitsa anthu kapena kuwanyengeza pofuna kuwasangalatsa. Zinali kusonyeza “ukulu wake wa Mulungu,” monga zinacitikila pankhani ya mnyamata amene Yesu anam’tulutsa ciwanda. (Luka 9:37-43) Kodi nchito zamphamvu zimenezi zingakhale zosatheka kwa Mulungu Wamphamvuyonse amene amanenedwa kuti ali na ‘mphamvu zazikulu’? (Yesaya 40:26) Ndithudi ayi!

Mauthenga Abwino amachula zozizwitsa za Yesu zokwana pafupifupi 35. Koma sachula zozizwitsa zonse zimene anacita. Mwacitsanzo, pa Mateyu 14:14 pamati: ‘[Yesu] anaona khamu lalikulu la anthu, nacitila iwo cifundo, nacilitsa akudwala awo.’ Sananenepo kuti ni anthu odwala angati amene anawacilitsa panthawi imeneyi..

Nchito zamphamvu zimenezi zinali zofunika kwambili potsimikizila zimene Yesu anali kunena kuti ni Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwa. Malemba amasonyezadi kuti mphamvu zimene Mulungu anam’patsa zinamuthandiza Yesu kucita zozizwitsa. Mtumwi Peturo anafotokoza Yesu kuti ni “mwamuna wocokela kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziŵa nokha.” (Machitidwe 2:22) Panthawi ina, Peturo ananena kuti “Mulungu anam’dzoza iye [Yesu] ndi mzimu woyela ndi mphamvu; amene anapita-pita nacita zabwino, nacilitsa onse osautsidwa ndi mdyerekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.”—Machitidwe 10:37, 38.

Zozizwitsa za Yesu zinali kuyendelana na uthenga wake. Pa Marko 1:21-27 pamasonyeza zimene anthu anacita atamva zimene Yesu anali kuphunzitsa ndiponso ataona cozizwitsa cake cina. Pa Marko 1:22 pamati anthu “anazizwa ndi ciphunzitso cake,” ndipo pa vesi 27 pamanena kuti anthu “anazizwa” Yesu atatulutsa ciwanda. Nchito zamphamvu za Yesu na uthenga wake zinapeleka umboni wakuti anali Mesiya wolonjezedwa.

Yesu sikuti anapeleka umboni wakuti anali Mesiya mwa mawu okha kapenanso mwa zocita zake zina, koma iye anatelonso mwa mphamvu zocitila zozizwitsa zimene Mulungu anam’patsa. Patabuka mafunso onena za nchito na udindo wake, Yesu anayankha molimba mtima kuti: “Ine ndili nawo umboni woposa wa Yohane [Mbatizi]; pakuti nchito zimene Atate anandipatsa ndizitsilize, nchito zomwezo ndizicita zindicitila umboni, kuti Atate anandituma Ine.”—Yohane 5:36.

Umboni Wakuti Zinali Zenizeni

Kodi tingatsimikize bwanji kuti zozizwitsa za Yesu zinali zenizeni? Onani zina zimene zikusonyeza kuti zinali zenizeni.

Pocita nchito zamphamvu, Yesu sanafune kuti anthu azim’tamama. Anali kuonetsetsa kuti anali kucita cozizwitsa cina ciliconse kuti Mulungu apatsidwe ulemu na kulemekezedwa. Mwacitsanzo, asanacilitse munthu wosaona, Yesu ananena motsindika kuti munthuyo acilitsidwa “kuti nchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.”—Yohane 9:1-3; 11:1-4.

Mosiyana na anthu ocita zinthu zongonyengeza anthu, amatsenga, ndiponso ocilitsa anthu mwa kuwapemphelela, Yesu sanali kugodomalitsa anthu maganizo, kuwanyengeza, kucita zionetselo zofuna kugometsa anthu, zamatsenga, kapena kucita zonyamula anthu maganizo. Sanatsatile zikhulupililo za anthu kapena kugwilitsa nchito zinthu zimene ankati n’zopatulika. Taonani kudzicepetsa kwa Yesu pamene anali kucilitsa anthu aŵili osaona. Nkhaniyo imati: “Yesu anagwidwa ndi cifundo, nakhudza maso awo; ndipo pomwepo anapenyanso, nam’tsata iye.” (Mateyu 20:29-34) Pamenepa sanacite mwambo wina uliwonse kapena cionetselo. Yesu anali kucita zozizwitsa poyela, ndipo nthawi zambili anali kuzicita anthu ambili akuona. Sanali kugwilitsa nchito malo ocita kukonzedwa mwapadela, kapenanso zipangizo zina zapadela. Mosiyana na zimenezi, zimene anthu masiku ano amati n’zozizwitsa nthawi zambili zimakhala zopanda umboni wotsimikizilika.—Marko 5:24-29; Luka 7:11-15.

Nthawi zina Yesu anali kunena kuti munthu amene wacilitsidwayo ali na cikhulupililo. Koma Yesu sanali kulephela kucilitsa munthu cifukwa cakuti munthuyo analibe cikhulupililo. Ali ku Kapernao ku Galileya, anthu ‘anabwela nawo kwa iye anthu ambili ogwidwa na mizimu yoipa; ndipo iye anatulutsa mizimuyo na mawu, nacilitsa akudwala onse.’Mateyu 8:16.

Yesu anali kucita zozizwitsa pofuna kuthandiza anthu pa zimene analidi kufunikila pamoyo wawo, osati kungofuna kusangalatsa anthu amene anali kuonelela. (Marko 10:46-52 Luka 23:8) Ndipo Yesu sanacite zozizwitsa kuti apeze phindu m’njila ina iliyonse.—Mateyu 4:2-4; 10:8.

Nanga Bwanji Mauthenga Abwino?

Tadziŵa za zozizwitsa za Yesu kudzela m’Mauthenga Abwino anayi. Kodi pali zifukwa zodalilila nkhani zimenezi pamene tikupenda ngati zozizwitsa za Yesu zinali zenizeni? Inde, zifukwa zilipo..

Monga taonela, zozizwitsa za Yesu zinali kucitikila pagulu, anthu ambili akuona. Mabuku a Mauthenga Abwino amene analembedwa cakoyambilila analembedwa ambili mwa anthu amene anaona zozizwitsazi ali na moyo. Pankhani yakuti olemba Mauthenga Abwino anali oona mtima, buku lakuti The Miracles and the Resurrection linati: “N’kulakwa kwambili kunena kuti olemba Mauthenga Abwino anali kulemba dala nkhani zambili-mbili za zozizwitsa pofuna kubisa zimene zinacitikadi n’colinga cofalitsa cikhulupililo cawo. . . . Iwo anali kungofuna kulemba zoona zokha-zokha.”

Anthu aciyuda otsutsa Cikristu sanakayikilepo nchito zamphamvu za m’Mauthenga Abwino. Iwo anali kukayikila mphamvu imene inali kucititsa zimenezi basi. (Marko 3:22-26) Ngakhale amene anadzakhala otsutsa analephela kutsutsadi zozizwitsa za Yesu. M’malomwake, zisanakwane zaka 100 ndiponso pambuyo pa zaka 100 Kristu Atabwela, panali maumboni a zozizwitsa zimene Yesu anacita. Ndithudi, tili na zifukwa zokwanila zokhulupilila kuti nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za zozizwitsa za Yesu n’zenizeni.

Khalidwe la Munthu Amene Anali kucita Zozizwitsazi

Kuti timvetse zozizwitsa za Yesu sitingalekele pamfundo yakuti zozizwitsa zake zinali zenizeni. Pofotokoza nchito zamphamvu zimene Yesu anacita, Mauthenga Abwino amanena za munthu amene anali kukhudzidwa mtima kwambili ndiponso wacifundo koposa, wocita cidwi na moyo wa anthu anzake.

Taonani nkhani ya munthu wodwala khate amene anafika kwa Yesu na kum’condelela momvetsa cisoni kuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Yesu ‘atagwidwa cifundo,’ anatansa dzanja na kukhudza munthu wodwala khateyo, nanena kuti: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” Munthuyo anacilitsidwa nthawi yomweyo. (Marko 1:40-42) Cotelo, Yesu anasonyeza kuti cisoni n’cimene cinkamupangitsa kugwilitsila nchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa zocitila zozizwitsa.

Kodi cinacitika n’ciani Yesu atakumana na anthu amene ananyamula malilo akucokela m’mudzi wa Nayini? Mnyamata amene anali atamwalilayo anali mwana mmodzi yekhayo wa mkazi wina wa masiye. Yesu ‘atagwidwa cifundo’ na mayiyo, anam’yandikila nanena kuti: “Usalile.” Ndiyeno anaukitsa mwana wa mayiyo.—Luka 7:11-15.

Phunzilo lolimbikitsa kwambili limene tikutengapo pa zozizwitsa za Yesu n’lakuti anali ‘kugwidwa cifundo’ ndipo anali kucita zinthu kuti athandize anthu. Koma zozizwitsa zimenezi sikuti ni mbili cabe. Pa Ahebri 13:8 pamati: “Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lelo, ndi ku nthawi zonse.” Panopo akulamulila monga Mfumu kumwamba, ndipo ni wokonzeka ndiponso angagwilitse nchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa zocitila zozizwitsa m’njila yaikulu zedi kuposa mmene anacitila ali padziko lapansi pano. Posacedwapa, Yesu adzagwilitsila nchito mphamvuzo kucilitsila anthu omvela. Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani kuphunzila zambili ponena za ciyembekezo ca m’tsogolo cabwino kwambili cimeneci..

[Zithunzi]

Zozizwitsa za Yesu zinali kusonyeza “ukulu wake wa Mulungu”

[Cithunzi]

Yesu anali munthu amene amakhudzidwa mtima kwambili