Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Ofalitsa Ufumu ku Britain—Galamukani!”

“Ofalitsa Ufumu ku Britain—Galamukani!”

“OFALITSA Ufumu ku Britain—Galamukani!!” Ici cinali cilengezo cofunika kucitapo kanthu mwamsanga. (mogwilizana ndi Informant, * ya December 1937, ya ku London) Nkhaniyo inalinso ndi kamutu kakuti: “Ciŵelengelo Sicikuwonjezeka pa Zaka 10 Zapitazi.” Lipoti la ulaliki loyambila mu 1928 mpaka mu 1937 imene inalembewa patsamba loyamba, inaonetsa kuti zimenezi n’zoonadi.

PANALI APAINIYA AMBILI

N’ciani cinapangitsa kuti nchito yolalikila ibwelele m’mbuyo ku Britain? M’mipingo yambili, cangu ca mu ulaliki cinali citacepa ndipo utumiki wawo unali pamodzi-mpamodzi. Kuwonjezela apo, ofesi ya nthambi inali itasankha kuti m’dzikolo mukhale cabe apainiya pafupi-fupi 200, amene anali kutumikila m’magawo akutali osati m’mipingo. Conco, ofesi ya nthambi inauza ofalitsa amene anali kudzakhala apainiya kuti m’dziko la Britain munalibe gawo lokwanila kutumikilamo, ndipo inawalimbikitsa kuti adzafunika kukacita upainiya ku maiko ena a ku Ulaya. Apainiya ambili anayamikila zimenezo cakuti anacoka ku Britain ndi kupita ku maiko ena monga France. Anacita izi ngakhale kuti sanali kudziŵa cinenelo ca kumeneko.

“PEMPHO LAKUTI ACITEPO KANTHU”

Kope ya Informant ya mu 1937, inaika mlingo wa maola 1 miliyoni amene ofalitsa anafunika kukwanilitsa mu 1938. Kuti akwanitse ciŵelengeco, ofalitsa anafunika kuthela maola 15 pa mwezi, ndipo apainiya maola 110. Anafunikanso kulinganiza tumagulu twaulaliki kuti tuzilalikila kwa maola asanu, na kuika maganizo pa maulendo obwelelako m’madzulo mkati mwa mlungu.

Mokondwa apainiya anaika maganizo awo pa ulaliki wakumunda

Ofalitsa ambili anakondwela ngako na makonzedwe atsopano aulaliki amenewo. Mlongo wina dzina lake Hilda Padgett * anati: “Limenelo linali pempho locokela ku likulu limene ambili aife tinali kuliyembekezela. Posapita nthawi, panakhala zotulukapo zabwino ngako.” Nayenso Mlongo E. F. Wallis anati: “Kuthela maola 5 mu ulaliki kwa masiku angapo mu wiki kunali kokondweletsa kwambili. Palibe cimene cikanabweletsa cimwemwe cacikulu kupambana kugwila nchito ya Ambuye kwa masiku athunthu. . . . Tinali kufika panyumba tili olema, koma tinali acimwemwe.” Wacicepele wina dzina lake Stephen Miller anaona kuti nchitoyo inafunika kucitika mwamsanga, ndipo anacitapo kanthu. Anali wofunitsitsa kugwilako nawo nchitoyo akapeza mpata. Iye anali kukumbukila magulu a ofalitsa akulalikila kwa masiku athunthu pa manjinga, ndiyeno m’madzulo anali kuliza nkhani zojambulidwa. Iwo anali kucita khama mu ulaliki poseŵenzetsa zikwangwani ndi kucitanso ulaliki wa mumseu pogaŵila magazini.

Informant inalinso na pempho yatsopano yakuti: “Tifuna gulu la apainiya okwana 1,000.” Pempho yatsopano imeneyi inacititsa kuti apainiya asamatumikile kutali na mipingo, koma akhale m’mipingomo kuti aithandize na kuilimbikitsa. Mlongo wina dzina lake Joyce Ellis anati: “Abale ambili anazindikila kuti afunika kuyamba upainiya. Olo kuti panthawiyo n’nali cabe na zaka 13, inenso n’nali kufuna kuyamba upainiya.” Mu July 1940, anakwanilitsa colinga cake atafika zaka 15. Nayenso Peter, amene anadzakhala mwamuna wa Mlongo Joyce, anamvela pempho yakuti “Galamukani.” Iye “anayamba kuganizila zoyamba upainiya.” Conco, mu June 1940 atakwanitsa zaka 17, anachova njinga pa msenga wa makilomita 105 kupita ku tauni ya Scarborough kukatumikila monga mpainiya.

Cyril na Kitty Johnson anali apainiya atsopano odzipeleka kwambili. Iwo anagulitsa nyumba na katundu wawo kuti ndalamazo ziŵathandize pocita utumiki wa nthawi zonse. Cyril analeka nchito, ndipo mwezi ukalibe kusila onse anayamba upainiya. Iye anakamba kuti: “Tinali na cidalilo cakuti tidzakwanitsa utumiki umenewu. Tinaucita na mtima wonse ndi mwacimwemwe.”

KUKHALA NA NYUMBA ZA APAINIYA

Pamene ciŵelengelo ca apainiya cinali kuwonjezeka mofulumila, abale audindo anapanga makonzedwe a mmene angathandizile gulu la apainiyawo. Mu 1938, Jim Carr, amene anali mtumiki wadela (tsopano timati woyang’anila dela) anathandiza kupeza nyumba zokhalamo apainiya m’mizinda. Magulu a apainiya analimbikitsidwa kukhala pamodzi na kulalikila mogwilizana, kuti asamawononge ndalama zambili. Mu mzinda wa Sheffield, anali kucita lendi nyumba ina yaikulu, ndipo m’bale waudindo ndiye anali kuiyang’anila. Mpingo wa kumeneko unapeleka ndalama na katundu wa m’nyumba. Jim anati: “Aliyense anathandiza kuti zinthu ziyende bwino.” Apainiya akhama okwana 10 anali kukhala m’nyumba imeneyo, ndipo anali kucita zinthu zauzimu nthawi zonse. Anali “kukambilana lemba [la tsiku] m’maŵa uliwonse asanayambe kudya. Tsiku lililonse, apainiyawo anali kuyenda kukalalikila m’magawo awo osiyana-siyana mumzindawo.”

Apainiya atsopano anawonjezeka ku Britain

Ofalitsa ndi apainiya anakwanitsa mlingo wa maola 1 miliyoni mu 1938. Ndipo malipoti anaonetsa kuti mbali zonse za utumiki wakumunda zinawonjezeka. Mwacitsanzo, pa zaka 5 cabe ciŵelengelo ca ofalitsa m’dziko la Britain cinawonjezeka kuŵilikiza katatu. Makonzedwe atsopanowo pa nchito ya Ufumu anathandiza atumiki a Yehova kupilila panthawi yankhondo imene inali kudzacitika mtsogolo.

Masiku ano, pamene nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo ili pafupi, ciŵelengelo ca apainiya ku Britain cawonjezekanso. Pa zaka zoposa 10 zapitazi, ciŵelengelo ca apainiya cinafika 13,224 mu October 2015. Apainiya amenewa ni ogalamuka m’njila yakuti amaona utumiki wa nthawi zonse kuti ni nchito yofunika mu umoyo wawo wonse.

^ par. 3 Imene inadzachedwa kuti Utumiki Wathu wa Ufumu.

^ par. 8 Mbili ya Mlongo Padgett inalembewa mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1995 masa. 19-24.