Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Kuwonjezela pa zimene Baibo imakamba, kodi palinso umboni wotani woonetsa kuti Aisiraeli anakhalako akapolo ku Iguputo?

Baibo imafotokoza kuti pambuyo pakuti Amidiyani atenga Yosefe kupita naye ku Iguputo, kholo lake Yakobo pamodzi na banja lake anasamuka kucoka ku Kanani kupita ku Iguputo. Iwo anakakhala ku Iguputo m’cigawo ca Goseni, pafupi na mtsinje wa Nile. (Gen. 47:1, 6) Aisiraeli “anapitiliza kuculukana ndi kukhala amphamvu koposa.” Conco, Aiguputo anacita mantha kwambili ndi ana a Isiraeli, ndipo anayamba kuwagwilitsa nchito yaukapolo.—Eks. 1:7-14.

Koma anthu ena otsutsa masiku ano amakamba kuti nkhani ya m’Baibo imeneyi si yoona, ni nthano cabe. Ngakhale n’conco, umboni ulipo woonetsa kuti mbadwa za Semu * zinakhalako akapolo ku Iguputo wakale.

Mwacitsanzo, ofukula za m’matongwe anapeza malo osiyana-siyana kumpoto kwa Iguputo, kumene kale kunali kukhala anthu. Dr. John Bimson anafotokoza kuti pali umboni woonetsa kuti ku dela limeneli la kumpoto kwa Iguputo, kuli malo okwana 20 kapena kuposapo, amene kunali kukhala mbadwa za Semu. Kuwonjezela apo, katswili wina wofufuza zinthu zakale za ku Iguputo, dzina lake James K. Hoffmeier anakamba kuti: “Kuyambila ca m’ma 1800 kufika mu 1540 B.C, dziko la Igupto linali malo okhumbilika oti anthu olankhula cinenelo ca Ayuda ndi Aluya ocokela kumadzulo kwa Asia n’kusamukilako.” Iye anakambanso kuti: “Iyi ni nthawi imodzi-modzi imene Abulahamu, Isaki, na Yakobo anakhalako, ndipo igwilizana na nthawi komanso zocitika zofotokozedwa m’buku la Genesis.”

Palinso umboni wina umene unapezeka kum’mwela kwa Iguputo. Colembapo ca gumbwa ca m’ma 2000 B.C.E–1600 B.C.E, cimene akatswili ena anapeza cili na maina a akapolo amene anali kugwila nchito pa nyumba inayake kum’mwela kwa Iguputo. Oposa 40 pa maina amenewo ni a Ciheberi komanso a zinenelo zina za Aluya. Akapolo amenewo, kapena kuti atumiki, anali kugwila nchito yophika, yowomba nsalu, na nchito zina zolemetsa. Hoffmeier anati: “Popeza Ayuda ndi Aluya oposa 40 anali kuseŵenza pa nyumba imodzi ku Thebaid [kumwela kwa Iguputo], ciŵelengelo ca Ayuda ndi Aluya mu Iguputo monse ciyenela kuti cinali cacikulu kwambili, maka-maka ku cigawo cimene mtsinje wa Nile umathilila m’nyanja yaikulu.”

Katswili wina wofukula za m’matongwe, dzina lake David Rohl analemba kuti ena mwa maina a akapolo amenewo “amaoneka ngati ni ocokela m’Baibo.” Mwacitsanzo, pa zidutswa za colembapo ca gumbwa cimene akatswili anapeza kum’mwela kwa Iguputo, pali maina ofanana na akuti Isakara, Aseri, Sifira. (Eks. 1:3, 4, 15) Rohl anatsiliza na mawu akuti: “Umenewu ni umboni wamphamvu woonetsa kuti Aisiraeli anakhalako akapolo ku Iguputo.”

Dr. Bimson anati: “Nkhani ya m’Baibo ya ukapolo wa Aisiraeli ku Iguputo na ulendo wawo wocoka ku Iguputo ni mbili yokhala na umboni wodalilika.”

^ ndime 4 Semu anali mmodzi wa ana atatu a Nowa. Mbadwa za Semu ziphatikizapo Aelamu, Asuri, Akasidi oyambilila, Aheberi, Asiriya, komanso mitundu yosiyana-siyana ya Aluya.