NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA March 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya May 6-June 2, 2019

Cikuniletsa Kubatizika N’ciani?

Anthu ena akaphunzila za Yehova, amawayawaya kubatizika. N’ciani cingawathandize kugonjetsa zopinga zilizonse zimene zingawapangitse kuzengeleza kubatizika?

Mvelani Mawu a Yehova

Kodi Yehova amakamba nafe bwanji masiku ano? Kodi timapindula bwanji ngati timvela Mulungu?

Muzimvelela Ena Cifundo

Kodi Yehova na Yesu anaonetsa bwanji kuti amamvelela ena cifundo, nanga tingatengele bwanji citsanzo cawo?

Onetsani Cifundo Pamene Muli mu Ulaliki

Kodi ni njila zinayi ziti zimene tingawonetsele cifundo kwa anthu amene timakumana nawo mu ulaliki?

Ubwino—Kodi tingalikulitse bwanji khalidwe limeneli?

Kodi ubwino n’ciani? N’cifukwa ciani tiyenela kulikulitsa khalidwe limeneli?

Yehova Amaona Kuti “Ameni” Wanu ni Wofunika

Anthu ambili amakonda kukamba kuti ‘ameni’ pambuyo pa pemphelo. Kodi liwu limeneli limatanthauza ciani nanga limaseŵenzesedwa bwanji m’Baibo?