Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Lolani Kuti “Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolelani

Lolani Kuti “Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolelani

LISA * anakamba kuti: “Kukoma mtima kwa abale na alongo kunanikhudza mtima kwambili.” Iye anali kukamba za cimene cinam’kopa kuti ayambe kuphunzila coonadi. Nayenso Anne anati, “Kukoma mtima kwawo n’kumene kunanikopa kwambili kuposa zimene anali kuphunzitsa.” Tsopano, alongo aŵili amenewa amakondwela kuŵelenga Baibo na kusinkhasinkha zimene amaŵelenga. Koma kukoma mtima n’kumene kunawathandiza kwambili kuti abwele m’coonadi.

Kodi tingaonetse bwanji kukoma mtima kumene kungakhudze anthu otizungulila? Tiyeni tione njila ziŵili izi: malankhulidwe athu na zocita zathu. Kenako, tikambilane za anthu amene tiyenela kuwakomela mtima.

“LAMULO LA KUKOMA MTIMA KOSATHA” LIKHALE PA LILIME LANU

Mkazi wochulidwa pa Miyambo caputala 31 ali na “lamulo la kukoma mtima kosatha” pa lilime lake. (Miy. 31:26) Iye amalola kuti “lamulo” limeneli lizimutsogolela pa zokamba zake na mmene amazikambila. Tate nayenso ayenela kukhala na “lamulo” limeneli pa lilime lake. Makolo ambili amadziŵa bwino kuti kulankhula mwaukali kumam’kwinyililitsa mwana, cakuti zingakhale zovuta mwanayo kuwamvela. Koma ngati alankhula naye mokoma mtima, cidzakhala cosavuta mwanayo kuwamvela.

Kaya ndinu kholo kapena ayi, kodi mungadziŵe bwanji kulankhula mokoma mtima? Yankho tilipeza pa ciganizo coyambilila pa Miyambo 31:26: “Amatsegula pakamwa pake mwanzelu.” Zimenezi zimafuna kusankha bwino mawu okamba komanso mmene tingawakambile. Nthawi zambili zimakhala bwino kumadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene nifuna kukamba zidzaputa mkwiyo kapena zidzabweletsa mtendele?’ (Miy. 15:1) Ndithudi, cimakhala canzelu kuyamba taganiza tisanalankhule.

Mwambi wina umati: ‘Kulankhula mosaganizila kumalasa ngati lupanga.’ (Miy. 12:18) Anthu amakhudzidwa na mawu athu komanso mmene timawakambila. Tikadziŵa zimenezi tidzakhala osamala polankhula. Kutsatila “lamulo la kukoma mtima kosatha,” kudzatithandiza kupewa kulankhula mawu acipongwe komanso mosasamala. (Aef. 4:31, 32) Kukamba mawu abwino komanso kuwakamba m’njila yoyenela, kudzatithandiza kucotsa maganizo olakwika komanso kupewa kukamba zosayenela. Yehova anapeleka citsanzo cabwino pa nkhaniyi, pamene anatsimikizila mtumiki wake Eliya ataopsezedwa. Mngelo woimilako Yehova analankhula mawu “acifatse apansipansi.” (1 Maf. 19:12) Komabe, kukhala wokoma mtima kumafuna zambili osati cabe kukamba mawu abwino. Timafunikanso kucita zinthu zoonetsa kuti ndife okoma mtima. Motani?

KUKOMELA MTIMA ANTHU ANZATHU KUMAWALIMBIKITSA

Timatengela citsanzo ca Yehova tikamalankhula mawu abwino na kucita zinthu mokoma mtima. (Aef. 4:32; 5:1, 2) Lisa amene tamuchula kuciyambi, anafotokoza mmene a Mboni anam’komela mtima. Iye anati: “Banja lathu litauzidwa mosayembekezela kuti lisamuke, mabanja aŵili mu mpingo mwathu anatenga chuthi kuti adzatithandize kulonga katundu. Panthawiyo, n’nali n’sanayambe n’komwe kuphunzila Baibo.” Nchito za kukoma mtima zimenezo zinalimbikitsa Lisa kuti ayambe kuphunzila coonadi.

Nayenso Anne, amene tamuchula kuciyambi, anayamikila mmene Mboni zinam’komela mtima. Iye anati: “Cifukwa ca zimene anthu anali kunicita, cinali covuta kwa ine kukhulupilila aliyense. Conco n’takumana na Mboni, n’nakayikila zolinga zawo. N’nadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani anthu awa akucita nane cidwi?’ Koma kukoma mtima kwa woniphunzitsa Baibo kunanithandiza kuyamba kum’khulupilila mphunzitsiyo.” Kodi panatuluka zabwino zotani? Iye anati: “M’kupita kwa nthawi, n’nayamba kuika maganizo anga pa zimene n’nali kuphunzila.”

Onani kuti Lisa komanso Anne, anakhudzidwa mtima kwambili na mmene abale na alongo mu mpingo anawakomela mtima. Izi zinawathandiza kuti ayambe kuphunzila coonadi, kukhulupilila Yehova, na anthu ake.

TENGELANI MULUNGU MWA KUKOMELA MTIMA ANTHU ENA

Anthu ena amalankhula mokoma mtima, komanso amamwetulila cifukwa ndico cikhalidwe cawo kapena cibadwa cawo. Izi n’zoyamikilika. Koma kukoma mtima kongotengela cikhalidwe cathu kapena cibadwa cathu, sindiko kotengela citsanzo ca kukoma mtima kwa Mulungu.—Yelekezelani na Machitidwe 28:2.

Kukoma mtima kwaumulungu ni cipatso cimene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Conco, kuti tionetse kukoma mtima kwenikweni, tiyenela kulola mzimu wa Mulungu kutsogolela maganizo athu na zocita zathu. Tikatelo, ndiye kuti tikutengela citsanzo ca Yehova na Yesu. Ndipo ife Akhristu timakhala na cidwi ceniceni pa anthu ena. Conco, kukonda Yehova Mulungu komanso anthu anzathu n’kumene kumatilimbikitsa kuonetsa khalidwe la kukoma mtima. Inde, kukoma mtima ni khalidwe lamphamvu limene limacokela mu mtima, ndipo Mulungu amakondwela nalo.

NDANI AMENE TIYENELA KUWAKOMELA MTIMA?

N’cosavuta kukomela mtima anthu amene nawonso amatikomela mtima, kapena amene timadziŵa. (2 Sam. 2:6) Njila imodzi imene tingawaonetsele kukoma mtima ni kuwayamikila. (Akol. 3:15) Koma bwanji ngati taona kuti munthu wina si woyenelela kum’komela mtima?

Ganizilani izi: Yehova ni citsanzo cabwino koposa pa nkhani yoonetsa kukoma mtima kwakukulu, ndipo Mawu ake amatiphunzitsa kuti tiyenela kuonetsa khalidwe limeneli. Mawu akuti “kukoma mtima kwakukulu,” amagwilitsidwa nchito nthawi zambili m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Kodi Mulungu amatikomela mtima m’njila zotani?

Ganizilani anthu mamiliyoni amene Yehova wakhala akuwakomela mtima. Iye akucita zimenezi powagaŵila zosoŵa pa umoyo wawo. (Mat. 5:45) Ndipo iye anayamba kutikomela mtima ngakhale pamene ife tisanam’dziŵe n’komwe. (Aef. 2:4, 5, 8) Mwacitsanzo, iye anapeleka Mwana wake wapamtima, wobadwa yekha, kuti awombole mtundu wonse wa anthu. Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova anapeleka dipo “malinga ndi cuma ca kukoma mtima kwake kwakukulu.” (Aef. 1:7) Cina, ngakhale kuti Yehova timam’cimwila na kukhumudwitsa, saaleka kutitsogolela na kutiphunzitsa. Malangizo ake na mawu ake ali ngati “mvula yowaza.” (Deut. 32:2) Kunena zoona, sitingakwanitse kum’bwezela pa zonse zimene amaticitila mwa kukoma mtima kwake. Conco, tsogolo lathu lonse latsamila pa cisomo ca Yehova.—Yelekezelani na 1 Petulo 1:13.

Mosakayika, kukoma mtima kwa Yehova kumatipangitsa kum’konda kwambili ndiponso kumatilimbikitsa. Conco, m’malo mocita kusankha anthu amene tiyenela kuwakomela mtima, tiyeni titengele citsanzo ca Yehova pokomela mtima aliyense nthawi zonse. (1 Ates. 5:15) Tikamakhala okoma mtima, timakhala ngati moto wothuma bwino m’nyengo yozizila. Ndipo timakhala dalitso kwa a m’banja mwathu, alambili anzathu, ogwila nawo nchito, anzathu a kusukulu, ndiponso kwa anthu oyandikana nawo.

Ganizilani anthu m’banja mwanu kapena abale na alongo mu mpingo amene angapindule ngati mukamba mawu abwino, na kuwacitila zinthu mokoma mtima. Mu mpingo mungakhale wina amene akusoŵekela thandizo losamalila pa nyumba pake, kapena zinthu zina monga kukam’gulila zinthu. Kuwonjezela apo, mukakumana na munthu mu ulaliki amene akufunikila thandizo lina lake, bwanji osapeleka thandizolo?

Tiyeni tizitengela citsanzo ca Yehova mwa kulola “lamulo la kukoma mtima kosatha” kutitsogolela pa zokamba na zocita zathu.

^ Maina asinthidwa.