NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA February 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya April 8-May 5, 2019

Khalanibe na Mtima Wamphumphu!

Kodi kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauzanji? Nanga n’ciani cingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu?

Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Mukondweletse Yehova

Kodi Mose na Yesu anaonetsa bwanji citsanzo cabwino pankhani yokhala wofatsa? Kodi tingapeze madalitso otani ngati tikhala ofatsa?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuonetsa Kuyamikila?

Kodi tingaphunzile ciani kwa Yehova, Yesu, komanso kwa Msamariya wakhate, pankhani yoonetsa kuyamikila?

Cikondi na Cilungamo M’nthawi ya Aisiraeli

Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji mmene Mulungu amaonela cikondi na cilungamo?

MBILI YANGA

Coloŵa Cauzimu Cimene N’nalandila Cinanithandiza Kupita Patsogolo

Ŵelengani nkhani yofotokoza za umoyo wa M’bale Woodworth Mills, amene wakhala akutumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka 80.

Kodi mudziŵa?

Kodi masunagoge anayamba bwanji?