NSANJA YA MLONDA Na. 3 2019 | Kodi Moyo Ni Uno Cabe Umene Ulipo?

Iyi ni funso imene anthu ambili amafunsa, ndipo yankho imene munthu angapeze ingakhudze kwambili umoyo wake wonse.

Palibe Angathaŵe Imfa

Ngakhale kuti anthufe tayesa-yesa kufuna kupewa ukalamba na imfa, sitinakwanitse kutelo. Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo?

Kufuna-funa Moyo Wautali

Asayansi ena odziŵa za maselo komanso odziŵa za majini, akuyesa-yesa kupeza cimene cimayambitsa ukalamba. Koma kodi zotulukapo za kafuku-fuku wawo zakhala zotani?

Tinalengedwa Kuti Tikhale na Moyo Kwamuyaya

Kodi n’ndani wa ife safuna kusangalala na moyo wautali?

N’cifukwa Ciani Timakalamba na Kufa?

Sicinali colinga ca Mulungu kuti anthufe tizifa. Makolo athu oyamba analengedwa na maganizo komanso matupi angwilo, ndipo sembe akalipo mpaka lelo.

Kodi Mdani Wathu Imfa, Adzagonjetsedwa Bwanji?

Mulungu anapanga makonzedwe acikondi kuti atiwombole ku mdani wathu imfa, mwa kulipila dipo.

Mungacite Ciani Kuti Mukapeze Moyo Weni-Weni?

Pali “msewu” wina wake umene mufunika kuyendamo, kuti mukakhale na moyo umene Mulungu akukonzela anthu amene amam’konda.

N’zotheka Kukhala na Umoyo Wacimwemwe Pali Pano

Kodi Baibo ingakuthandizeni bwanji kukhala wokhutila, kulimbitsa cikwati canu, kapena kupilila pamene mudwala?