NSANJA YA MLONDA Na. 2 2020 | Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Anthu afunsa funso limeneli kwa zaka zambili. Koma yankho lake lingapezeke mosavuta m’Baibo.

“Ufumu Wanu Udze”—Pemphelo Limene Anthu Ambili Amapeleka

Kodi ni mafunso ati okamba za Ufumu wa Mulungu amene tifunika kupeza mayankho ake kuti timvetse tanthauzo la pemphelo limeneli?

N’cifukwa Ciani Tifunikila Ufumu wa Mulungu?

Anthu opanda ungwilo akamadzilamulila okha, zotulukapo zake zimakhala mavuto.

Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndani?

Olemba Baibo angapo ndithu analemba zimene zinali kudzathandiza anthu kudziŵa amene adzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. M’mbili yonse ya anthu, zinthu zonsezi zinakwanilitsidwa ndendende pa munthu mmodzi.

Nanga Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulila Dziko Lapansi?

Ena mwa otsatila a Yesu okhulupilika anafunanso kudziŵa. Kodi Yesu anayankha bwanji funso lawo?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacita Zotani?

Yesu anali kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndilo boma limene lidzacotsapo mavuto padzikoli. Kodi Ufumu wa Mulungu wacita kale zotani potithandiza kukhala wotsimikiza za zimene udzacita?

Sankhani Kucilikiza Ufumu wa Mulungu Palipano!

Yesu analimbikitsa otsatila ake kufuna-funa Ufumu coyamba. Kodi mungacite bwanji zimenezo?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Anthu ambili amapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Koma kodi munadzifunsapo kuti Ufumu wa Mulungu n’ciani? Nanga udzacita ciani?