Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Coonadi Ponena za Kutsogolo

Coonadi Ponena za Kutsogolo

Kodi munadzifunsapo kuti n’ciani cidzacitika kutsogolo? Baibo imatiuza kuti posacedwa, pa dziko lapansi padzacitika zinthu zapadela zimene zidzakhudza munthu aliyense.

Yesu anafotokoza mmene ‘tidzadziŵile kuti ufumu wa Mulungu wayandikila.’ (Luka 21:31) Iye anakamba kuti kudzakhala nkhondo zikulu-zikulu, zivomezi za mphamvu, njala, komanso milili. Ndipo izi n’zimene zikucita masiku ano.—Luka 21:10-17.

Baibo imakambanso kuti mu “masiku otsiliza” a ulamulilo wa anthu, anthu adzakhala na makhalidwe oipa. Mungaŵelenge za makhalidwe oipa amenewa pa 2 Timoteyo 3:1-5. Mosakaikila, mukaona makhalidwe oipa amenewa, mumakhulupilila kuti ulosi wa m’Baibo umenewu ukukwanilitsika masiku ano.

Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Zitanthauza kuti nthawi ili pafupi yakuti Ufumu wa Mulungu usinthe zinthu pa dziko lapansi, na kupangitsa anthu kukhala na umoyo wabwino. (Luka 21:36) Kupitila m’Baibo, Mulungu analonjeza kuti adzakonza dziko lapansi kukhala malo abwino, ndipo zinthu zidzakhala bwino kwa anthu amene adzakhala m’dzikolo. Onani zitsanzo zocepa izi.

ULAMULILO WABWINO

“Kenako anamupatsa [Yesu] ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenelo zosiyanasiyana azimutumikila. Ulamulilo wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—DANIELI 7:14.

Tanthauzo lake: Mungakhale na mwayi wokasangalala na moyo mu ulamulilo wa boma labwino kwambili la pa dziko lonse lokhazikitsidwa na Mulungu, limene Mwana wake ndiye Mfumu.

THANZI LABWINO

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala’”—YESAYA 33:24.

Tanthauzo lake: Simudzadwala kapena kulemala, ndipo mudzakhala na moyo kwamuyaya.

MTENDELE WOCULUKA

“Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—SALIMO 46:9.

Tanthauzo lake: Sikudzakhalanso nkhondo, ndipo mavuto onse obwela cifukwa ca nkhondo adzathelatu.

DZIKO LAPANSI LIDZADZALA NDI ANTHU ABWINO

“Woipa sadzakhalakonso . . . Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi.”—SALIMO 37:10, 11.

Tanthauzo lake: Sikudzakhalanso anthu oipa, koma anthu okhawo ofunitsitsa kumvela Mulungu.

DZIKO LAPANSI LIDZAKHALA PARADAISO

“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—YESAYA 65:21, 22.

Tanthauzo lake: Dziko lonse lidzakhala lokongola. Mulungu adzayankha pemphelo lathu lakuti cifunilo cake cicitike, “pansi pano.” —Mateyu 6:10.