Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Aramagedo n’ciani?

Anthu ena amakhulupilila kuti . . .

idzakhala nkhondo ya zida za nyukiliya, kapena kusintha kwa nyengo kowononga cilengedwe. Imwe muganiza bwanji?

Zimene Baibo imakamba

Aramagedo ni malo ophiphilitsa oimila “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Nkhondo yowononga anthu oipa.—Chivumbulutso 16:14, 16.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Mulungu adzamenya nkhondo ya Aramagedo osati kuti awononge dziko, koma kuti aliteteze kwa anthu amene akuliwononga.—Chivumbulutso 11:18.

  • Nkhondo ya Aramagedo idzathetsa nkhondo zonse.—Salimo 46:8, 9.

Kodi n’zotheka kupulumuka nkhondo ya Aramagedo?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Iyai

  • Kapena

Zimene Baibo imakamba

“Khamu lalikulu” la anthu ocokela m’mitundu yonse lidzapulumuka “cisautso cacikulu,” cimene cidzathetsedwa pa nkhondo ya Aramagedo.—Chivumbulutso 7:9, 14.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Mulungu afuna kuti anthu ambili akapulumuke Aramagedo. Iye amawononga anthu oipa ngati palibe mwina mocitila.—Ezekieli 18:32.

  • Baibo ifotokoza zimene tingacite kuti tikapulumuke Aramagedo.—Zefaniya 2:3.