Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO | SARA

Mulungu Anamucha Mfumukazi

Mulungu Anamucha Mfumukazi

SARA anaŵelamuka na kuyang’ana capatali. Anchito ake anali kugwila nchito mwakhama ndi mwacimwemwe motsatila malangizo ake. Nayenso Sara anali kugwila nchito yake mwakhama. Yelekezani kuti mukumuona akudziwongola manja. Mwina iye anali bize kusoka kacigamba pa tenti imene inali nyumba yawo. Tenti ya ubweya wa mbuzi imeneyo inali yojujuka cifukwa ca dzuŵa na mvula. Izi zinakumbutsa Sara kuti wakhala umoyo wokuka-kuka kwa zaka zambili. Tsopano dzuŵa linali litayamba kuloŵa. Tsikulo m’maŵa anali ataona Abulahamu * akucoka panyumba, ndiyeno m’madzulo maso ake anali kunjila kuyembekezela mwamuna wake. Mwacizoloŵezi, akuona mwamuna wake akutulukila capatali kumtunda, ndipo nkhope yake yokongola ikumwetulila.

Panali patapita zaka 10 kucokela pamene Abulahamu anatsogolela banja lake kuoloka Mtsinje wa Firate kuloŵa m’dziko la Kanani. Modzipeleka Sara anacilikiza mwamuna wake pa ulendowu kupita kumalo osadziŵika. Iye anadziŵa kuti mwamuna wake anali na mbali yofunika kwambili pokwanilitsa colinga ca Yehova codzatulutsa mbeu komanso mtundu wodalitsidwa. Nanga Sara anali na mbali yanji? Iye anali wosabeleka, ndipo apa n’kuti wafika zaka 75. Ayenela kuti anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi lonjezo la Yehova lidzakwanitsidwa bwanji popeza ine sinibeleka?’ Zikanakhala zomveka ngati iye anada nkhawa ngakhale kutaya mtima.

Nthawi zina, nafenso timafuna kudziŵa nthawi pamene malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwa. Timavutika kuleza mtima maka-maka ngati tiyembekezela kuti zinthu zimene timakonda zicitike. Tiphunzilapo ciani pa cikhulupililo colimba ca mayi ameneyu?

“YEHOVA ANANDITSEKA”

Banjali linali litangobwelako ku Iguputo. (Genesis 13:1-4) Linamanga misasa m’dela la mapili ca kum’mawa kwa Beteli, kapena kuti Luzi, malinga ndi mmene Akanani anali kuchulila. M’delali, Sara anali kukwanitsa kuona kukula kwa Dziko Lolonjezedwa. M’dzikoli munali midzi ya Akanani na misewu imene anthu oyenda ku madela akutali anali kuseŵenzetsa. Komabe, midzi imeneyo inali yosiyana ndi kumene Sara anakulila. Iye anakulila mumzinda wa Uri, ku Mesopotamiya. Mzindawu unali pa mtunda wa makilomita 1,900. Kumeneko anasiya abululu ŵake, zinthu zabwino za mumzinda wotukuka umenewo wokhala ndi mamaliketi na mashopu, komanso nyumba yake yabwino, mwina yokhala na mapaipi a madzi. Ngati tingayelekeze kuti tikuona Sara akuyang’ana ca kum’mawa mosakondwa, kuyewa zinthu zabwino za mumzinda umene anakulila, ndiye kuti sitim’dziŵa bwino mkazi woopa Mulungu ameneyu.

Pokamba za cikhulupililo ca Abulahamu na Sara, onani zimene mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba patapita zaka 2,000. Anati: “Akanakhala kuti anali kumangokumbukila malo amene anacokela, mpata wobwelela akanakhala nawo.” (Aheberi 11:8, 11, 15) Abulahamu na Sara sanaganizilepo zimene anasiya kumbuyo. Sembe iwo anakhala na maganizo amenewo, akanabwelela ku Uri, ndipo akanataya mwayi waukulu umene Yehova anali kudzawapatsa. Komanso sakanakhala zitsanzo zabwino pankhani ya cikhulupililo colimba kwa anthu mamiliyoni ambili.

M’malo moyang’ana zakumbuyo, Sara anayang’ana za kutsogolo. Anapitiliza kucilikiza mwamuna wake paulendo wawo wokuka-kuka, kum’thandiza kulonga matenti, kutsogolela ziŵeto, na kumanga misasa. Anapililanso mavuto na kusintha kwa zinthu mu umoyo wake. Yehova anabwelezanso lonjezo lake kwa Abulahamu, koma sanakambepo za Sara.—Genesis 13:14-17; 15:5-7.

Tsopano, Sara anaona kuti inali nthawi youza Abulahamu za pulani imene anali kuganizila kwa nthawi yaitali. Yelekezani kuti mukumuona akuoneka wododoma pamene akuti: “Yehova ananditseka kuti ndisabeleke ana.” Ndiyeno anapempha mwamuna wake kuti abeleke ana kupitila mwa wanchito wake wamkazi, Hagara. Ganizilani cabe mmene Sara anavutikila maganizo popempha mwamuna wake zimenezo. Masiku ano, pempho limeneli lingaoneke lacilendo, koma m’nthawiyo zinali zofala mwamuna kutenga mkazi waciŵili, kapena cisumbali, kuti abeleke ana. * Mwina Sara anaganiza kuti zimenezo zidzathandiza kuti colinga ca Mulungu cotulutsa mtundu mwa Abulahamu cikwanilitsidwe. Mulimonsemo, Sara anali wofunitsitsa kupanga cosankha covuta cimeneci. Nanga Abulahamu anacita ciani? Timaŵelenga kuti iye “anamvela mau a [Sara].”—Genesis 16:1-3.

Kodi nkhaniyi imaonetsa kuti Sara anakamba maganizo ake mosonkhezeledwa na Yehova? Iyai. Zimene anakamba zinangoonetsa maganizo aumunthu. Iye anaona kuti Mulungu ndiye anacititsa mavuto ake, ndipo sanaganizilepo kuti Mulungu angakhale na njila ina yothetsela mavutowo. Njila imene Sara anaona kuti ingathandize ikanam’bweletsela mavuto. Ngakhale n’conco, maganizo akewo anaonetsa kuti sanali wodzikonda. Popeza tili m’dziko limene anthu ake amaika zofuna zawo patsogolo, kodi citsanzo ca Sara si colimbikitsa kwa ise? Ngati timaika cifunilo ca Mulungu patsogolo m’malo mwa zofuna zathu zadyela, tidzatengela cikhulupililo ca Sara.

“UNASEKA IWE”

Pasanapite nthawi yaitali, Hagara anakhala ndi pathupi pa Abulahamu. Mwina poganiza kuti pathupi pakum’pangitsa kukhala wofunika kwambili kuposa Sara, Hagara anayamba kunyoza mbuye wake. Izi zinam’khumudwitsa kwambili Sara wosabeleka! Mwa cilolezo ca Abulahamu ndi thandizo la Mulungu, Sara anadzudzula Hagara mwamseli. Hagara anabeleka mwana dzina lake Isimaeli, ndiyeno panapita zaka zambili. (Genesis 16:4-9, 16) Panthawi imene uthenga wa Yehova unamvekanso, Sara anali na zaka 89 ndipo mwamuna wake anali na zaka 99. Unali uthenga wosangalatsa kwambili.

Apanso, Yehova analonjeza bwenzi lake Abulahamu kuti adzam’culukitsila mbeu yake. Cina, Mulungu anam’sintha dzina. Pofika pano, iye anali kudziŵika kuti Abulamu. Koma Yehova anam’patsa dzina lakuti Abulahamu, limene limatanthauza “Tate wa mitundu yambili.” Tsopano kwa nthawi yoyamba, Yehova anaonetsa mbali imene Sara anali nayo. Iye anasintha dzina lake lakuti Sarai, limene liyenela kuti linali kutanthauza “Wolongolola,” na kum’patsa dzina lakuti Sara limene ife tonse timadziŵa. Kodi dzinali limatanthauzanji? Limatanthauza “Mfumukazi.” Yehova anafotokoza cifukwa cimene anam’patsila dzinali. Anati: “Ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wocokela mwa iye. Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambili ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambili ya anthu.”—Genesis 17:5, 15, 16.

Lonjezo la Yehova lakuti adzatulutsa mbeu imene idzadalitsa mitundu yonse ya anthu inali kudzakwanilitsika kupitila mwa mwana wa Sara. Dzina limene Mulungu anapatsa mwanayo lakuti Isaki, limatanthauza “Kuseka.” Pamene Abulahamu anadziŵa koyamba kuti Yehova adzadalitsa Sara mwa kum’patsa mwana, “anagwada n’kuŵelama mpaka nkhope yake pansi, n’kuyamba kuseka.” (Genesis 17:17) Iye anadabwa na kukondwela kwambili. (Aroma 4:19, 20) Nanga bwanji Sara?

Posapita nthawi, amuna atatu alendo, anabwela ku hema wa Abulahamu. Tsikulo, kunali kotentha kwambili, koma banja lokalamba limeneli mwamsanga linapita kukalandila alendo. Abulahamu anauza Sara kuti: “Fulumila! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu ya seya, uukande, ndipo upange makeke ozungulila.” Kale, kuceleza alendo cinali cinchito. Abulahamu sanangosiila mkazi wake kugwila yekha nchitoyo. Iye anathamanga kukapha ng’ombe yaing’ono, ndipo anakonza zakudya na zakumwa zambili. (Genesis 18:1-8) “Amuna” amenewo anali angelo a Yehova. Mwacionekele, mtumwi Paulo anaganizila cocitika ici polemba kuti: “Musaiŵale kuceleza alendo, pakuti potelo, ena anaceleza angelo mosadziŵa.” (Aheberi 13:2) Kodi na imwe simungatengele citsanzo cabwino ca Abulahamu na Sara coceleza alendo?

Sara anali kukonda kuceleza alendo

Mmodzi wa angelowo anabwelezanso lonjezo la Mulungu kwa Abulahamu lakuti Sara adzabeleka mwana, apo n’kuti Sara sakuonekela. Anali m’hema wake kumvetsela. Iye anadabwa atamvela kuti adzabeleka mwana mu ukalamba wake, cinthu cimene cinali cacilendo kwa iye. Conco, Sara anaseka mumtima mwake, akukamba kuti: “Kodi mmene ndathelamu, zoona ndingakhaledi ndi cisangalalo cimeneci, komanso ndi mmene mbuyanga wakalambilamu?” Ndiyeno mngelo anawongolela Sara mwa kufunsa kuti, “Kodi pali cosatheka ndi Yehova?” Mwacibadwa, Sara anacita mantha ndipo anafuna kukana. Iye anakamba mokweza kuti: “Sindinaseketu ine ayi!” Koma mngelo anati: “Ayi! Unaseka iwe.”—Genesis 18:9-15.

Kodi kuseka kwa Sara kuonetsa kuti analibe cikhulupililo? Iyai. Baibo imati: “Mwa cikhulupililo, Sara nayenso analandila mphamvu yokhala ndi pakati ngakhale kuti anali atapitilila zaka zobeleka, cifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupilika.” (Aheberi 11:11) Sara anali kum’dziŵa Yehova, anali kudziŵa kuti angakwanilitse lonjezo lililonse. N’ndani amene safuna kukhala na cikhulupililo ca conco? Tifunika kum’dziŵa bwino Mulungu amene analemba Baibo. Tikatelo, tidzaona kuti mpake Sara kukhala na cikhulupililo cimene anali naco. Zoona Yehova ni wokhulupilika, ndipo amakwanilitsa malonjezo ake. Nthawi zina, angacite zimenezo m’njila imene ingatidabwitse kapena kuikaikila.

“MVELA MAU AKE”

Yehova anadalitsa Sara cifukwa ca cikhulupililo cake

Ali na zaka 90, Sara anakondwela kwambili kuona kuti zimene anali kulaka-laka mu umoyo wake zacitika. Anabeleka mwana apo n’kuti mwamuna wake wokondedwa ali na zaka 100. Abulahamu anacha mwanayo kuti Isaki, kapena kuti “Kuseka,” monga mmene Mulungu anakambila. Yelekezani kuti mukuona Sara akumwetulila uku akukamba kuti: “Mulungu anandisekeletsa ine, onse akumva adzasekela pamodzi ndi ine.” (Genesis 21:6) Mphatso ya Yehova yozizwitsa imeneyi inam’sangalatsa masiku ake onse. Komabe, mphatsoyo inabweletsa udindo waukulu kwa iye.

Pamene Isaki anali na zaka 5, banja lonse linakonza phwando lalikulu, kukondwelela kuti mwanayo wasiya kuyamwa. Koma panali vuto. Timaŵelenga kuti Sara anali ‘kuona’ khalidwe loipa. Isimaeli, mwana wa zaka 19 wa Hagara, anapitiliza kuvutitsa Isaki wacicepele. Kuvutitsaku sikunali kwa maseŵela cabe. Mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba za khalidwe la Isimaeli kuti kunali kuzunza. Sara anaona kuti kuvutitsa kumeneku kunali kuika moyo wa mwana wake pa ciwopsezo. Anali kudziŵa kuti Isaki sanali cabe mwana wamba, koma anali na mbali yofunika kwambili pa colinga ca Yehova. Conco, molimba mtima anakamba na Abulahamu mosapita m’mbali. Anapempha kuti Abulahamu athamangitse Hagara na Isimaeli.—Genesis 21:8-10; Agalatiya 4:22, 23, 29.

Kodi Abulahamu anacitanji? Timaŵelenga kuti: “Abulahamu anaipidwa nazo kwambili zimenezi cifukwa ca mwana wake.” Abulahamu anali kum’konda Isimaeli, ndipo monga kholo sanafune kukhala zii. Komabe, Yehova anali kuidziŵa nkhani yonse. Conco, nayenso analoŵelelapo. Timaŵelenga kuti: “Koma Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Usaipidwe ndi ciliconse cimene Sara wakhala akunena kwa iwe cokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mvela mau ake, cifukwa amene adzachedwa mbeu yako adzacokela mwa Isaki.’” Yehova anatsimikizila Abulahamu kuti Hagara na mwana wake adzawasamalila. Abulahamu anagonjela mokhulupilika.—Genesis 21:11-14.

Sara anali mkazi wabwino kwa Abulahamu, inde mnzake womuyenelela. Sanali kungouza mwamuna wake zom’komela m’khutu ayi. Pakakhala vuto limene lingakhudze banja lawo na tsogolo lawo, anali kuuza mwamuna wake moona mtima. Sitiyenela kuganiza kuti kukamba moona mtima n’kupanda ulemu. Mtumwi Petulo, mwamuna wokwatila, anakamba za Sara kuti anali citsanzo cabwino pankhani yolemekeza mwamuna wake. (1 Akorinto 9:5; 1 Petulo 3:5, 6) Kukamba zoona, sembe Sara anakhala zii osakambapo ciliconse, zikanaonetsa kuti sakulemekeza Abulahamu, cifukwa zinthu sizikanayenda bwino kwa mwamuna wake komanso m’banja lawo lonse. Mwacikondi Sara anakamba zimene zinali zofunikila.

Akazi ambili a pabanja amayamikila citsanzo ca Sara. Potengela citsanzo cake, iwo amakambilana ndi amuna awo moona mtima ndi mwaulemu. Nthawi zina, akazi ena angakonde kuti Yehova aloŵelelepo pa nkhani inayake monga anacitila kwa Sara. Komabe, iwo amatengela cikhulupililo colimba ca Sara, cikondi, na kuleza mtima kwake.

Yehova anacha Sara kuti “Mfumukazi,” koma Sara sanayembekezele kucitilidwa zinthu monga mfumukazi

Olo kuti Yehova ndiye anacha mkazi wokondedwa ameneyu kuti “Mfumukazi,” Sara sanayembekezele kucitilidwa zinthu monga mfumukazi. Mpake kuti iye atamwalila ali na zaka 127, Abulahamu “analoŵa muhema kukamulila Sara.” * (Genesis 23:1, 2) Iye anamuyewa kwambili mkazi wake wokondedwa. Mosakaikila, nayenso Yehova Mulungu amamuyewa mkazi wokhulupilika ameneyu, ndipo alaka-laka kudzamuukitsa m’paradaiso padziko lapansi. Sara, na onse amene amatengela cikhulupililo cake, akuyembekezela kudzasangalala kwamuyaya.—Yohane 5:28, 29.

^ par. 3 Poyamba, banjali linali kudziŵika kuti Abulamu ndi Sarai mpaka pamene Mulungu anasintha maina awo. Koma m’nkhani ino tidzaseŵenzetsa maina amene amadziŵika nawo kwambili.

^ par. 10 Kwa kanthawi, Yehova analola anthu kukwatila mphali komanso kukhala na zisumbali. Koma pambuyo pake anapatsa Yesu Khristu mphamvu yolamula kuti ukwati uzikhala wa mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi, monga mmene zinalili poyamba mu Edeni.—Genesis 2:24; Mateyu 19:3-9.

^ par. 25 Sara ndiye mkazi yekha amene Baibo imachula zaka zake pamene anamwalila.