Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mu Ufumu wa Mulungu, anthu “adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:11

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Baibo ingakuthandizeni kutsiliza nkhawa?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Iyai

  • Kapena

Zimene Baibo imakamba

‘Tulilani [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Baibo imatsimikizila kuti Mulungu angakuthandizeni kutsiliza nkhawa zanu.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Pemphelo lingakuthandizeni kupeza “mtendele wa Mulungu,” umene ungacepetse nkhawa zanu.—Afilipi 4:6, 7.

  • Cina, kuŵelenga Mau a Mulungu kungakuthandizeni kulimbana ndi nkhawa. —Mateyu 11:28-30.

Kodi n’zotheka nkhawa kuthelatu?

Ena amakhulupilila kuti . . .nkhawa na kuvutika maganizo ni mbali ya umoyo wa munthu, pamene ena amakhulupilila kuti nkhawa zimakasila m’moyo wina pambuyo pa imfa. Nanga imwe muganiza bwanji?

Zimene Baibo imakamba

Mulungu adzacotsapo zinthu zonse zobweletsa nkhawa. “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzakhala pamtendele.—Yesaya 32:18.

  • Nkhawa zonse na kuvutika maganizo zidzaiŵalika.—Yesaya 65:17.