NSANJA YA MLONDA Na. 1 2025 | Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?

Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda nkhondo komanso ciwawa? N’zimene ambili amafuna. Koma amaona kuti n’zosatheka. Baibo imatiuza cifukwa cake anthu alephela kuthetsa nkhondo. Imapelekanso maumboni otsimikizila kuti n’zotheka kukhala ndi mtendele padziko lonse, ndiponso kuti zimenezi zidzacitikadi posacedwa.

M’magazini ino, mawu akuti “nkhondo” akukamba za kumenyana pakati pa magulu a nkhondo pa zifukwa za ndale. Maina a anthu ena amene achulidwa m’magazini ino asinthidwa.

 

Pa Nkhondo Pamacitika Zinthu Zoipa Kwambili

Asilikali komanso anthu amene anakhalako kumalo kumene kunali nkhondo amawadziwa bwino mavuto obwela cifukwa ca nkhondo.

Mmene Nkhondo Zimatikhudzila Tonsefe

Nkhondo imawononga zinthu komanso ndalama zambili. Onani zitsanzo.

Kodi Anthu Angakwanitse Kuthetsa Nkhondo?

Anthu akhala akucita zosiyanasiyana kuti athetse nkhondo ndi kukhazikitsa mtendele. Koma kodi zimene akucitazo zingabweletsedi mtendele padziko?

Cifukwa Cake Nkhondo Zikupitilizabe Kucitika

Baibo imafotokoza zimene zimayambitsa nkhondo.

Kodi Nkhondo Zidzatha Bwanji?

Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo ndi kubweletsa mtendele weniweni padziko lapansi.

Kupeza Mtendele wa Mumtima pa Nthawi ya Nkhondo

Palipano Baibo ikuthandiza anthu amene anakhudzidwa ndi nkhondo.

Kodi Munadzifunsapo Mafunso Awa?

Kodi nkhondo zidzathadi padzikoli? Baibo imapeleka yankho lolimbikitsa la funso limeneli, komanso limayankha mafunso ena pa nkhani imeneyi.