Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Anu?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Anu?

Mukamapemphela, kodi muganiza kuti Mulungu amamvadi mapemphelo anu?

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

  • Mulungu amamvetsela. Baibo imatitsimikizila kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi. . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Salimo 145:18, 19.

  • Mulungu amafuna kuti muzipemphela kwa iye. Baibo imati: “Pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” —Afilipi 4:6.

  • Mulungu amasamala kwambili za imwe. Mulungu amadziŵa bwino kwambili mavuto athu na nkhawa zathu, ndipo amafuna kutithandiza. Baibo imati: “Citani zimenezi pamene mukumutulila nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.