Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Baibo na Tsogolo Lanu

Baibo na Tsogolo Lanu

YELEKEZELANI kuti mukuyenda mu mseu m’madzulo ndipo kuli mdima. Ngakhale kuti dzuŵa laloŵa kale, simukuda nkhawa cifukwa muli na toci yamphamvu. Mukaunika pansi, mukwanitsa kuona bwino-bwino zimene zili pafupi. Mukaunika kutsogolo, mukwanitsa kuona bwino-bwino zinthu zimene zili patali kwambili.

M’njila ina, Baibo ili ngati toci ya mphamvu imeneyi. Monga mmene taonela m’nkhani zapita, Mau a Mulungu angatithandize kulimbana na mavuto amene tonsefe timakumana nawo tsiku na tsiku m’dziko loipali. Koma Baibo imatithandizanso m’njila zina. Imatithandiza kudziŵa bwino zam’tsogolo. Kudziŵa zimenezi kumatithandiza kuzindikila njila yabwino imene tingatsatile pa umoyo wathu kuti tikakhale na mtendele wosatha na umoyo wokhutilitsa m’tsogolo. (Salimo 119:105) Kodi imatithandiza bwanji?

Tiyeni tikambilane njila ziŵili za mmene Baibo imatithandizila kukhala na ciyembekezo codalilika ca m’tsogolo: 1 Imatithandiza kukhala na umoyo waphindu, ndipo 2 imatiphunzitsa mmene tingapangile ubwenzi wosatha na Mlengi wathu.

1 UMOYO WAPHINDU

Baibo imapeleka malangizo odalilika amene angatithandize kulimbana na mavuto athu, koma sizokhazo. Baibo siilimbikitsa kuti tizingoganizila za mavuto athu kapena zofuna zathu zokha. M’malomwake, imatithandizanso kuzindikila kuti palinso zinthu zina zofunikila kupambana ise. Tikatelo, m’pamene timakhala na umoyo waphindu.

Mwacitsanzo, ganizilani mfundo iyi ya m’Baibo yakuti: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Kodi mukumbukila pamene munathandizapo munthu wina wosoŵa mwakuthupi? Kapena pamene munali kumvetsela mwachelu mnzanu pokukhutulilani zakukhosi kwake? Kodi simunakondwele kuti munatonthoza wina wake tsikulo?

Tikathandiza wina, timakhala na cimwemwe cacikulu ngati sitiyembekezela winayo kutibwezela. Mlembi wina anati: “Kukamba zoona, kupatsa kumadalitsa nthawi zonse—malinga ngati tipeleka tilibe maganizo ofuna cotibwezela.” Conco, tikathandiza ena—maka-maka amene sangakwanitse kutibwezela—pamakhala mphoto yake. Timatengako mbali pa kuthandiza ena. Zoona, timagwila nchito pamodzi na Mlengi, amene amaona kukoma mtima kumeneko monga nkhongole imene tamukongoza. (Miyambo 19:17) Iye amayamikila kwambili zimene timacitila anthu ovutika, ndipo walonjeza kukatipatsa moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi—ciyembekezo ca tsogolo labwino!—Salimo 37:29; Luka 14:12-14. *

Koposa zonse, Baibo imatiphunzitsa kuti tikhoza kukhala na umoyo waphindu mwa kulambila Mulungu woona, Yehova. Mau ake amatilangiza kuti tiyenela kumutamanda, kum’patsa ulemu, ndi kumumvela. (Mlaliki 12:13; Chivumbulutso 4:11) Tikacita zimenezi, ndiye kuti tacita cinthu camtengo wapatali, ndipo timasangalatsa Mlengi wathu. Iye amatilangiza kuti: “Khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga.” (Miyambo 27:11) Tangoganizani! Timatha kum’kondweletsa Atate wathu wacikondi wakumwamba pamene tipanga zosankha mwanzelu, zozikidwa pa mfundo za m’Baibo. Potifunila zabwino, Mulungu amafuna kuti tizipindula mwa kutsatila malangizo ake. (Yesaya 48:17, 18) Zoonadi, timakhala na umoyo waphindu kwambili pamene tilambila Wolamulila wa cilengedwe conse na kucita zinthu zom’kondweletsa.

2 KUPALANA UBWENZI NA MLENGI WATHU

Baibo imatilangizanso kuti tiyenela kukhala pa ubwenzi na Mlengi wathu. Imakamba kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Nthawi zina, tikhoza kukaikila ngati n’zothekadi kukhala pa ubwenzi na Mlengi wamphamvu yonse. Koma Baibo imatitsimikizila kuti ngati ‘timufunafuna Mulungu . . . tidzamupezadi.’ (Machitidwe 17:27) Uphungu wa m’Baibo wakuti tikhale pa ubwenzi na Mulungu ungatithandize kupeza tsogolo labwino. Motani?

Olo tiyesetse bwanji, patokha sitingakwanitse kum’thaŵa mdani wathu woipitsitsa amene ni imfa. (1 Akorinto 15:26) Komabe, Mulungu ni wamuyaya. Iye sadzafa, ndipo amafuna kuti mabwenzi ake nawonso akhale na moyo wamuyaya. Mwa mau acidule ndi amphamvu otsatilawa, Baibo imatiuza zimene Yehova amafuna kucitila anthu omufuna-funa. Imati: “Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.”—Salimo 22:26.

Mungacite ciani kuti mupalane ubwenzi wamuyaya na Mulungu? Pitilizani kuphunzila za iye kupitila m’Mau ake, Baibo. (Yohane 17:3; 2 Timoteyo 3:16) M’pempheni kuti akuthandizeni kumvetsetsa Malemba. Baibo imatitsimikizila kuti ngati ‘tipempha kwa Mulungu’ mocokela pansi pamtima kuti atipatse nzelu, iye adzatipatsa. * (Yakobo 1:5) Cothela, muyenela kuyetsetsa kuseŵenzetsa zimene muphunzila. Lolani Mau a Mulungu kukutsogolelani monga “nyale younikila kumapazi [anu],” na “kuwala kounikila njila [yanu],” lomba mpaka muyaya.—Salimo 119:105.

^ par. 8 Kuti mudziŵe zambili za lonjezo la Mulungu la moyo wosatha m’Paradaiso, onani nkhani 3 m’buku yakuti, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, yolembewa na Mboni za Yehova.

^ par. 13 Mboni za Yehova zimaphunzitsa anthu Baibo mahala. Zingakuthandizeni kuti muzimvetsetsa Malemba. Kuti mudziŵe mmene izi zimacitikila, tambani vidiyo yakuti, Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? Mungaipeze pa jw.org, mwa kulemba dzina la vidiyo imeneyi pa malo ofufuzila.

Mulungu ni wamuyaya. Iye amafuna kuti mabwenzi ake nawonso akhale na moyo wamuyaya