Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Nakhala na Mwayi Wotumikila Pamodzi ndi Amuna Auzimu

Nakhala na Mwayi Wotumikila Pamodzi ndi Amuna Auzimu

CAPAKATI pa zaka za m’ma 1930, atate anga a James Sinclair ndi amayi, a Jessie Sinclair, anasamukila m’dela la Bronx, mumzinda wa New York. Mmodzi wa anzawo atsopano anali Willie Sneddon, amene anacokela ku Scotland, kumenenso makolo anga anacokela. Atangokumana koyamba, anayamba kukambilana zokhudza mabanja awo. Izi zinacitika zaka zingapo ine nisanabadwe.

Amayi anauza a Willie kuti Nkhondo Yaikulu itangotsala pang’ono kuyamba, atate awo ndi alongo awo anamila pamadzi boti yawo itagunda bomba yocheledwa pamadzi ku North Sea. A Willie anauza amayi kuti: “Atate anu ali ku helo!” * Izi zinawadabwitsa kwambili amayi. A Willie anali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo apa m’pamene amayi anayambila kumva coonadi ca m’Baibo.

Willie ndi Liz Sneddon

Zimene a Willie anakamba zinawakhumudwitsa amayi, cifukwa anali kudziwa kuti atate wawo anali munthu wabwino. Koma a Willie ananenanso kuti: “Kodi mungadabwe ngati nakuuzani kuti Yesu atamwalila anapita ku helo?” Atamva zimenezi, amayi anakumbukila za ciphunzitso ca kuchechi kwawo, cimene cinali kunena kuti Yesu anapita ku helo, ndipo pa tsiku lacitatu anaukitsidwa. Conco, iwo anadzifunsa kuti, ‘Ngati helo ni malo ozunzilako anthu oipa, n’cifukwa ciani Yesu anapita kumeneko?’ Kuyambila pamenepo, amayi anakhala na cidwi cofuna kudziwa coonadi. Anayamba kusonkhana ndi Mpingo wa Bronx, ndipo anabatizika mu 1940.

Nili na amayi, ndipo pambuyo pake nili na atate

M’zaka zimenezo, makolo acikhristu sanali kulimbikitsidwa kweni-kweni kuphunzitsa ana awo Baibo. Pamene n’nali mwana, atate ndiwo anali kunisamalila ngati amayi apita kumisonkhano ndi muulaliki kumapeto kwa wiki. Patapita zaka zocepa, ine na atate tinayamba kupita pamodzi na amayi kumisonkhano. Amayi anali akhama pa nchito yolalikila uthenga wabwino ndipo anali kucititsa maphunzilo a Baibo ambili kwa anthu acidwi. Panthawi ina yake, anali kuphunzila ndi anthuwo m’magulu cifukwa manyumba awo anali oyandikana. Nikavalila sukulu, n’nali kuyenda nawo muulaliki. Mwa njila imeneyi, n’naphunzila zambili zokhudza Baibo ndi mmene ningaphunzitsile ena zimene imakamba.

Pamene n’nali wacicepele sin’nali kucikonda kweni-kweni coonadi. N’nali kucitenga mopepuka. Komabe, nitatsala pang’ono kukwanitsa zaka 12, n’nakhala wofalitsa Ufumu. Kuyambila nthawiyo, n’nayamba kupita muulaliki mokhazikika. N’tafika zaka 16, n’nadzipeleka kwa Yehova, ndipo n’nabatizika pa July 24, 1954, pa msonkhano wacigawo ku Toronto, m’dziko la Canada.

KUTUMIKILA PA BETELI

Abale ena a mumpingo wathu anali atatumikilapo pa Beteli, ndipo ena anali kutumikilabe pa Beteli. Citsanzo cawo cinanilimbikitsa kwambili. N’nali kucita cidwi na maluso awo pokamba nkhani ndi pofotokoza coonadi ca m’Baibo. Ngakhale kuti matica a kusukulu kwathu anali kufuna kuti nikacite maphunzilo a ku yunivesiti, colinga canga cinali kukatumikila ku Beteli. Conco, n’tabatizika pa msonkhano wacigawo wa ku Toronto, n’nasaina fomu yofunsila utumiki wa pa Beteli. N’nasainanso fomu ina yofunsila utumiki wa pa Beteli mu 1955, pa msonkhano wacigawo ku Yankee Stadium, mumzinda wa New York. Pasanapite nthawi yaitali, n’nalandila ciitano cokayamba utumiki wa pa Beteli ku Brooklyn pa September 19, 1955. Apa n’kuti nili na zaka 17. Tsiku laciŵili la utumiki wanga pa Beteli, n’nayamba kuseŵenzela m’fakitale yokonzela mabuku ku 117 Adams Street. Pasanatenge nthawi, n’nayamba kuseŵenzela pa mashini osonkhanitsa mabuku. Mashini amenewo anali kusonkhanitsa zigawo za mapeji 32 za mabuku, zimene pambuyo pake zinali kusokewa na mashini osokela mabuku.

Nili na zaka 17, n’nayamba utumiki wa pa Beteli ku Brooklyn

N’taseŵenza pafupi-fupi kwa mwezi umodzi m’fakitale yokonzela mabuku, n’naikidwa m’Dipatimenti ya Magazini cifukwa n’nali kudziŵa kutaipa. Panthawiyo, abale na alongo anali kulemba maadiresi a anthu amene alembetsa kuti azilandila magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani. Maadiresiwo anali kuwalemba pa tumalata tung’ono-tung’ono. Patangopita miyezi yocepa, n’nayamba kuseŵenzela m’Dipatimenti Yotumiza Mabuku. Klaus Jensen, amene anali kuyang’anila dipatimenti imeneyo, ananipempha kuti niziyenda na dilaiva wa thilaki yonyamula makatoni a zofalitsa. Zofalitsazo zinali kupelekedwa ku madoko, ndipo pambuyo pake anali kuzitumiza m’maiko osiyana-siyana padziko lonse. Komanso panali masaka a magazini amene anali kufunika kupelekedwa ku positi ofesi n’colinga cakuti awatumize ku mipingo yonse ya m’dziko la United States. M’bale Jensen anakamba kuti nchito ya manja inganithandize kukhala wathanzi. Panthawiyo, n’nali wocepa thupi kwambili ndipo n’nali kulemela makilogilamu 57 cabe. Koma maulendo opita ku madoko ndi ku positi ofesi ananithandiza kukhala wolimba. M’bale Jensen anali kudziŵa bwino nchito yoniyenelela.

Cinanso cimene Dipatimenti ya Magazini inali kucita ndi kutumiza magazini amene mipingo yaitanitsa. Conco, n’nadziŵa kuculuka kwa zinenelo zimene magazini athu anali kupulintiwa ku Brooklyn ndi kutumizidwa m’maiko ena padziko lapansi. Zambili mwa zinenelozo n’nali nisanazimvepo, koma n’nali wokondwa kudziŵa kuti magazini ambili-mbili anali kutumizidwa kumaiko akutali. Sin’nali kudziŵa kuti m’zaka za kutsogolo, nidzakhala na mwayi wokacezela abale m’maiko amenewo.

Nili na Robert Wallen, Charles Molohan, ndi Don Adams

M’caka ca 1961, n’nauzidwa kuti nizitumikila mu Ofesi ya Wosunga Cuma, imene inali kuyang’anilidwa ndi m’bale Grant Suiter. Pambuyo pa zaka zingapo, n’naitanidwa ku ofesi ya M’bale Nathan Knorr, amene anali kutsogolela nchito ya padziko lonse panthawiyo. Iye ananifotokozela kuti mmodzi wa abale oseŵenzela mu ofesi yake adzaloŵa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, imene idzatenga mwezi wathunthu. Anafotokozanso kuti pambuyo pake m’baleyo adzayamba kutumikila m’Dipatimenti ya Utumiki. Conco, n’nauzidwa kuti nizigwila nchito imene iye anali kucita, ndipo n’nayamba kutumikila pamodzi ndi m’bale Don Adams. N’nakondwela kutumikila na m’baleyu, amenenso analandila fomu yanga yofunsila utumiki wa pa Beteli pa msonkhano wa cigawo mu 1955. Abale enanso aŵili amene anali kutumikila m’dipatimenti imeneyi ndi m’bale Robert Wallen ndi Charles Molohan. Tonse anayi tinatumikila pamodzi kwa zaka zoposa 50. Zoonadi, unali mwayi waukulu kutumikila pamodzi na amuna okhulupilika ndi auzimu amenewa.—Sal. 133:1.

Ulendo wanga woyamba woyendela nthambi, ku Venezuela, mu 1970

Kuyambila m’caka ca 1970, nakhala na mwayi woyendela maofesi a nthambi osiyana-siyana a Watch Tower Society. N’nali kuyendela maofesi a nthambi angapo kwa mawiki ocepa m’caka ciliconse kapena pambuyo pa zaka ziŵili. Izi zinali kuphatikizapo kucezela mabanja a Beteli ndi amishonale padziko lonse, kuwalimbikitsa mwauzimu, ndi kupenda mafaelo a ofesi ya nthambi. N’nali na mwayi wokumana ndi amishonale akale amene analoŵa makilasi oyambilila a Sukulu ya Giliyadi, ndipo anali kutumikilabe mokhulupilika m’maiko amene anatumizidwa. Ndithudi, wakhala mwayi wamtengo wapatali kuyenda m’maiko oposa 90, mu utumiki umenewu.

Nakhala na mwayi wamtengo wapatali wocezela abale m’maiko oposa 90

N’NAPEZA MNZANGA WOKHULUPILIKA

Abale na alongo onse otumikila pa Beteli ku Brooklyn anauzidwa kuti azisonkhana m’mipingo ya mumzinda wa New York. Ine n’nauzidwa kuti nizisonkhana mumpingo wa ku Bronx. Mpingo woyamba m’dela limeneli utakula, anaugaŵa. Mpingo woyambawo ni umene ine n’nali kusonkhanamo, ndipo unayamba kuchedwa Upper Bronx.

Ca pakati pa zaka za m’ma 1960, banja lina la Mboni locokela ku Latvia limene linaphunzilila coonadi m’dela la kumwela kwa Bronx, linasamukila m’gawo la mpingo wathu. Mwana wamkazi woyamba m’banjali, dzina lake Livija, anayamba upainiya wa nthawi zonse atangotsiliza maphunzilo a ku sekondale. Patapita miyezi yocepa, anasamukila ku Massachusetts kukatumikila kumpingo umene unali na ofalitsa Ufumu ocepa. Tinayamba kulembelana makalata. N’nali kumufotokozela zokhudza mpingo wathu. Nayenso anali kunifotokozela za mmene nchito yolalikila inali kupitila patsogolo ku Boston.

Nili na Livija

Patapita zaka zocepa, Livija anaikidwa kukhala mpainiya wapadela. Anali wofunitsitsa kucita zambili mu utumiki wa Yehova cakuti anafunsila utumiki wa pa Beteli, ndipo anaitanidwa mu 1971. N’naona kuti Yehova wayankha pemphelo langa. Pa October 27, 1973, tinakwatilana ndipo M’bale Knorr ndi amene anatikambila nkhani ya cikwati. Umenewu unalidi mwayi waukulu. Lemba la Miyambo 18:22 limati: “Kodi munthu wapeza mkazi wabwino? Ndiye kuti wapeza cinthu cabwino, ndipo Yehova amakondwela naye.” Ine na Livija takhala na mwayi wotumikila limodzi pa Beteli kwa zaka zoposa 40. Pali pano, tikali kucilikiza mpingo wa m’dela la Bronx.

KUTUMIKILA PAMODZI NA ABALE A KHRISTU

Kutumikila pamodzi na M’bale Knorr unali mwayi waukulu. Iye anali kutumikila mwakhama pofuna kupititsa patsogolo coonadi. Komanso anali kukonda kwambili amishonale padziko lonse lapansi. Ambili mwa amishonalewo ndi amene anakhala Mboni zoyambilila ku maiko amene anatumizidwa kukatumikila. Zinali zacisoni kuona M’bale Knorr akuvutika na matenda a khansa mu 1976. Tsiku lina, ali pabedi, ananipempha kuti nimuŵelengele zofalitsa zina zimene zinali kufunika kupulintiwa. Ananipemphanso kuti niitane M’bale Frederick Franz kuti nayenso adzamvetsele zimene n’nali kuŵelenga. Patapita nthawi, n’nadziŵa kuti M’bale Knorr anali kuthela nthawi yoculuka kuŵelengela zofalitsa M’bale Franz cifukwa ca vuto lake la maso.

Kuyendela nthambi ya ku Togo pamodzi ndi m’bale Daniel Sydlik ndi mkazi wake Marina, mu 1977

M’bale Knorr anamwalila mu 1977, koma onse amene anali kumudziŵa ndi kum’konda anatonthozedwa podziŵa kuti anatsiliza moyo wake wa padziko lapansi ali wokhulupilika. (Chiv. 2:10) Pambuyo pake, M’bale Franz ndiye anakhala wotsogolela nchito yathu.

Panthawiyo, n’nali mlembi wa m’bale Milton Henschel, amene anatumikila pamodzi na M’bale Knorr kwa zaka zambili m’mbuyomo. M’bale Henschel ananiuza kuti kuyambila nthawiyo udindo wanga waukulu pa Beteli udzakhala kuthandiza M’bale Franz pa zilizonse zimene angafune thandizo. Nthawi zonse, n’nali kumuŵelengela zofalitsa zatsopano zikalibe kupulintiwa. M’bale Franz anali na luso lomvetsela mwachelu nikamaŵelenga, ndiponso anali kukumbukila zinthu kwambili. Zinali zokondweletsa kum’thandiza mwanjila imeneyo kufikila pamene anatsiliza moyo wake wa padziko mu December 1992.

Ku 124 Columbia Heights, kumene n’natumikila kwa zaka zambili

Nimaona kuti zaka 61 zimene nakhala nikutumikila pa Beteli zatha mofulumila kwambili. Makolo anga onse anafa ali okhulupilika kwa Yehova, ndipo niyembekezela mwacidwi kudzawalandila m’dziko labwino latsopano. (Yoh. 5:28, 29) Palibe ciliconse cimene tingapeze m’dziko loipali cimene cingalingane na mwayi wogwila nchito pamodzi ndi amuna ndi akazi okhulupilika potumikila anthu a Mulungu padziko lonse lapansi. Ine na Livija tingakambe motsimikiza kuti pa zaka zonse zimene takhala mu utumiki wa nthawi zonse, ‘cimwemwe cimene Yehova amapeleka cakhala malo athu acitetezo.’—Neh. 8:10.

Nchito yofalitsa coonadi ca Ufumu ikupitilizabe, ndipo siidalila munthu mmodzi m’gulu la Yehova. Zakhala zokondweletsa ndiponso mwayi kutumikila kwa zaka zambili pamodzi na abale na alongo akhama ndi okhulupilika. Ambili mwa abale odzozedwa amene n’nali kutumikila nawo anatsiliza moyo wawo wa padziko lapansi. Koma ndine woyamikila ngako kuti n’natumikila Yehova pamodzi ndi amuna auzimu ndi okhulupilika amenewa.

[Mau apansi]

^ par. 5 Mau a m’zinenelo zoyambilila za Baibo akuti Sheol ndi Hades amatanthauza manda a anthu onse. Koma m’Mabaibo ena, mau amenewa anawamasulila kuti “helo.”