NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA October 2017

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya November 27-December 24, 2017.

MBILI YANGA

Kucita Zimene Yehova Watilamula Kumabweletsa Madalitso

Mu 1952, Olive Matthews na mwamuna wake anavomela kupita ku Ireland, kukacita upainiya. Kodi Yehova anawadalitsa bwanji?

“Tizisonyezana Cikondi Ceni-ceni m’Zocita Zathu”

Tingaonetse bwanji kuti tili na cikondi ceni-ceni?

Coonadi ‘Sicibweletsa Mtendele Koma Lupanga’

Kodi “lupanga” limene Yesu anakamba kuti adzabweletsa n’ciani? Nanga ni mavuto anji amene tingakumane nawo cifukwa ca lupanga limeneli?

Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

Kodi munthu ameneyu anali ndani? Kodi panali ubale wanji pakati pa iye na Yesu? Nanga nkhani yake itikhudza bwanji masiku ano?

Mmene Masomphenya a Zekariya Amakukhudzilani

Mpukutu wouluka; mkazi wovininkhilidwa m’ciwiya copimila, ndi akazi aŵili ouluka mumlengalenga. N’cifukwa ciani Mulungu anaonetsa Zekariya masomphenya ocititsa cidwi amenewa?

Magaleta na Cisoti Cacifumu Zimakutetezani

Mapili amkuwa, magaleta okonzekeletsedwa kaamba ka nkhondo, ndi mkulu wa ansembe wolongewa ufumu. Kodi masomphenya otsilizila a Zekariya anawatsimikizila ciani anthu a Mulungu?

Kuonetsa Kukoma Mtima Kamodzi Cabe

Mmene munthu wotsutsa anayambila kucita cidwi na coonadi ca m’Baibo ataonetsedwa kukoma mtima kamodzi cabe.

Kodi Mudziŵa?

Kodi Ayuda anali na cizoloŵezi canji cimene cinapangitsa Yesu kuwaletsa kulumbila?