Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungacite Ciani Kuti Mujaile mu Mpingo Wanu Watsopano?

Mungacite Ciani Kuti Mujaile mu Mpingo Wanu Watsopano?

ALLEN * anati: “N’nali kumvela mantha kukukila kuno. Sin’nali kudziŵa kuti ningapeze anzanga na kuti ena adzakhala omasuka nane.” Lomba, Allen wayamba kuzoloŵela kukhala mu mpingo watsopano umene anakukilako, umene uli pa msenga wa makilomita 1,400, kucoka kwawo.

Ngati munakukila mu mpingo wina, n’kutheka kuti inunso muli na mantha. N’ciani cingakuthandizeni kuti mujaile? Nanga mungacite ciani ngati muona kuti zikukuvutani kujaila? Komanso, kodi mungawathandize bwanji alendo amene akukila mu mpingo wanu kuti zisawavute kujaila?

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUJAILE NA KUPITA PATSOGOLO

Ganizilani citsanzo ici: Ngati mwanyula mtengo pamalo ena kuti mukauwokele pena, umayamba wakwinyilila. Zimakhala conco cifukwa pounyula, mumacotsa ina mwa mizu yake kuti usakuvuteni kunyamula. Koma mukauwoka, posakhalitsa umayamba kumela mizu ina. Mofananamo, ngati mwakukila mu mpingo wina, mukhoza kumakhala womangika. Mu mpingo wanu wakale, munali wozika “mizu,” titelo kukamba kwake, cifukwa munali na mabwenzi abwino ndiponso munali na cizolowezi cabwino cocita zinthu zauzimu. Koma pamene mwasamukila mu mpingo wina, mufunika kuzika mizu yatsopano kuti mupitilize kukhala wolimba kuuzimu. N’ciani cingakuthandizeni kucita zimenezi? Ni kuseŵenzetsa mfundo za m’Malemba. Tiyeni tione zina mwa mfundo zimenezi.

Munthu amene amaŵelenga Mau a Mulungu nthawi zonse, amakhala “ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”Sal. 1:1-3.

Mtengo umafunika madzi nthawi zonse kuti ukhale wathanzi. Nayenso Mkhristu amafunika kuphunzila Mau a Mulungu nthawi zonse kuti akhale wolimba kuuzimu. Conco, pitilizani kuŵelenga Baibo tsiku lililonse, na kupezeka ku misonkhano ya mpingo nthawi zonse. Pitilizani kucita kulambila kwa pabanja na phunzilo laumwini nthawi zonse. Zilizonse zimene munali kucita mu mpingo wanu wakale, n’zimenenso muyenela kucita mu mpingo watsopano kuti mukhalebe olimba kuuzimu.

“Wothilila ena mosaumila nayenso adzathililidwa mosaumila.”Miy. 11:25.

Kugwila nchito yolalikila nthawi zonse kudzakuthandizani kukhala wolimba kuuzimu na kujaila mwamsanga mu mpingo watsopano. Kevin, amene ni mkulu mu mpingo, anati: “Cimene cinatithandiza kwambili ine na mkazi wanga ni kucita upainiya wothandiza titangofika mu mpingo watsopano. Posapita nthawi, tinadziŵana na abale na apainiya, komanso tinalidziŵa bwino gawo.” Roger, amene anakukila ku malo amene ali pa msenga wopitilila makilomita 1,600 kucokela kwawo, anakamba kuti: “Cinthu cofunika cimene mungacite kuti mujaile mu mpingo watsopano ni kupita mu ulaliki kaŵili-kaŵili. Cinanso, muyenela kudziŵitsa akulu kuti ndinu wokonzeka kuthandiza pa nchito iliyonse, kaya ni yoyeletsa pa Nyumba ya Ufumu, kukambako nkhani za volontiya pa misonkhano, kapena kutengako winawake m’motoka yanu popita ku misonkhano. Abale na alongo akaona kuti ndinu wodzipeleka, adzayamba kugwilizana namwe.”

“Futukulani mtima wanu.”2 Akor. 6:13.

Yesetsani kukulitsa cikondi canu pa abale. Melissa na a m’banja lake atakukila mu mpingo wina, anali kucita zinthu zowathandiza kupeza mabwenzi atsopano. Iye anati: “Misonkhano isanayambe komanso ikasila, tinali kucezako na abale na alongo pa Nyumba ya Ufumu. Kucita izi kunatipatsa mwayi wokamba nawo nkhani zina m’malo mowapatsa moni cabe.” Izi zinathandizanso a m’banjali kudziŵa mwamsanga maina a abale na alongo. Kuwonjezela apo, anafutukula mtima wawo mwa kucelezako ena kunyumba kwawo. Zimenezi zinathandiza kuti ubwenzi wawo na anthu a mumpingo watsopano ulimbe. Iye anakambanso kuti: “Tinapatsana manamba ya foni n’colinga cakuti azitiitanako pakakhala zocitika zauzimu kapena zina.”

Ngati mumacita manyazi kukamba na anthu amene simuwadziŵa, mungayambe mwa kucita tunthu tung’ono-tung’ono. Mwacitsanzo, pokamba na anthu, muzimwetulila olo kuti poyamba simungafune kucita zimenezi. Kumwetulila kudzacititsa ena kuyamba kumasuka nanu. Paja Baibo imati, “maso owala amapangitsa mtima kusangalala.” (Miy. 15:30) Rachel, amene anasamukila kutali na kumene anakulila, anati: “Mwacibadwa, ndine wamanyazi. Nthawi zina, nimacita kudzikakamiza kuti nikambe na abale na alongo mu mpingo wanga watsopano. Nimakonda kupita kwa munthu amene wakhala pansi m’Nyumba ya Ufumu, amenenso sakukamba na aliyense kuti nikambe naye. Munthu ameneyo angakhale kuti nayenso ni wamanyazi ngati ine.” Bwanji osacipanga kukhala colinga canu kuti misonkhano ikalibe kuyamba kapena ikatha, muzikambako na munthu amene simum’dziŵa?

Monga mlendo, kwa mawiki angapo oyambilila, mungakhale okondwa kudziŵana na anthu amene kale simunali kuwadziŵa. Koma m’kupita kwa nthawi, anthu angaleke kukuonani kuti ndinu “mlendo.” Zikafika apa, mungafunike kucita khama kuti mupitilize kupeza mabwenzi atsopano.

Mtengo akaunyula kuti auwokele pamalo ena umakwinyilila, koma akauwoka, umamela mizu yatsopano

DZIPATSENI NTHAWI YOKWANILA YAKUTI MUJAILE

Mitengo ina mukaiwoka, imatenga nthawi itali kuti igwile kusiyana na ina. Mofananamo, ena cingawatengele nthawi itali kuti ajaile mu mpingo watsopano poyelekezela na ena. Ngati papita nthawi itali kucokela pamene munakukila mu mpingo wina koma zikukuvutani kujaila, n’ciani cingakuthandizeni? Muyenela kutsatila mfundo za m’Baibo izi:

“Conco tisaleke kucita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”Agal. 6:9.

Mufunika kukhala oleza mtima na kudzipatsa nthawi yokwanila yakuti mujaile. Mwacitsanzo, amishonale ambili otsiliza maphunzilo a Giliyadi akatumiziwa ku dziko lina, amakhala kumeneko zaka zambili asanabwelele ku dziko lawo kukaceza. Kucita izi kumawathandiza kupanga ubwenzi na abale a kudzikolo, ndiponso kumawathandiza kuti ajaile cikhalidwe catsopano.

Alejandro, amene wakhala na umoyo wokuka-kuka, anazindikila kuti pamatenga nthawi kuti munthu ajaile mu mpingo watsopano. Iye anati: “Pamene tinakuka, mkazi wanga anati, ‘Anzanga onse anatsala mu mpingo wathu wakale.’” Iye anakumbutsa mkazi wakeyo kuti zimene anakamba n’zimenenso anakamba zaka ziŵili zapitazo, pamenenso anali kukuka. Koma m’zaka ziŵilizo, mkaziyo anagwilizana na abale na alongo ena, ndipo nawonso anakhala mabwenzi ake apamtima.

“Usanene kuti: “N’cifukwa ciani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?” Pakuti si nzelu kufunsa funso lotele.”Mlal. 7:10.

Muzipewa kuyelekezela mpingo wanu watsopano na wakale. Mwacitsanzo, abale a mumpingo wanu watsopano angakhale osamasuka kweni-kweni poyelekezela na a mu mpingo wanu wakale. Koma muziika maganizo anu pa makhalidwe awo abwino, cifukwa n’zimene inunso mumafuna kuti iwo azikucitilani. Ofalitsa ena akakukila ku mpingo wina amazindikila kuti afunika kusintha mmene amaonela anthu ena kuti aonetse kuti amakondadi “gulu lonse la abale.”—1 Pet. 2:17.

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”Luka 11:9.

Pitilizani kupemphela kuti Mulungu akuthandizeni kujaila mu mpingo wanu watsopano. David, amene ni mkulu anati: “Musadzidalile. Zinthu zambili zimafunika thandizo la Yehova kuti tikwanitse kuzicita. Conco, ipempheleleni nkhaniyi.” Rachel, amene tamugwila mau poyamba anavomeleza zimenezi. Iye anati: “Ine na mwamuna wanga tikayamba kuona ngati kuti ena satiŵelengela mu mpingo, timamuuza Yehova mwacindunji m’pemphelo kuti, ‘Tithandizeni kudziŵa ngati ticita zinthu zimene zikulepheletsa ena kumasuka nase.’ Ndiyeno, timayesetsa kupatula nthawi yokwanila yoceza na abale na alongo.”

Makolo, ngati ana anu akuvutika kujaila mu mpingo watsopano, muzipemphela nawo pamodzi za nkhaniyo. Athandizeni kupeza anzawo atsopano mwa kupanga makonzedwe akuti muzikhala na maceza olimbikitsa.

THANDIZANI AMENE ASAMUKILA MU MPINGO MWANU KUKHALA OMASUKA

Mungacite ciani kuti muthandize anthu amene akukila mu mpingo mwanu? Akangofika, muziyesetsa kukhala bwenzi lawo leni-leni. Cimene cingakuthandizeni kucita izi ni kuganizila zimene inu mukanafuna kuti wina akucitileni mukanakhala kuti ndinu mlendo. Ndiyeno, acitileni zimenezo alendowo. (Mat. 7:12) Kodi anthu amene akukila mu mpingo mwanu mungawaitaneko kunyumba kwanu kuti mudzacite nawo kulambila kwa pabanja kapena kutamba nawo pulogilamu ya pa mwezi ya JW Broadcasting? Kodi mungawapemphe kuti mupite nawo mu ulaliki? Komanso ngati mwawaitanilako ku cakudya, sadzaiŵala mzimu wanu woceleza. N’zinthu zinanso ziti zimene mungacite kuti muthandize anthu amene abwela mu mpingo mwanu?

Carlos anati: “Titafika mu mpingo watsopano, mlongo wina anatiuza maina a mashopu amene tingagulemo zinthu zochipa. Izi zinatithandiza ngako.” Akhristu amene akukila m’dela lanu kucokela ku maiko ena angayamikile kuwauzako zovala zoyenelela zimene angavale m’nyengo yotentha, yozizila, kapena yamvula. Mungawathandizenso kukhala alaliki ogwila mtima mwa kuwauzako zokhudza mbili ya delalo, kapena kuwafotokozela zikhulupililo za cipembedzo zofala m’delalo.

KUPANGA MASINTHIDWE KULI NA MAPINDU AKE

Allen, amene tam’chula poyamba nkhani ino, wakhala mu mpingo watsopano kwa caka na miyezi. Iye anati: “Poyamba sin’nali womasuka na abale na alongo. Koma lomba, timamvela monga ndise a m’banja limodzi, ndipo ndine wokondwa ngako.” Allen, anazindikila kuti kukuka sikunamutaitse mabwenzi. Koma kunamupatsa mwayi wopeza mabwenzi ena atsopano, amene mosakayikila adzakhala anzake kwa moyo wake wonse.

^ par. 2 Maina ena asinthidwa.