Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mphamvu ya Moni

Mphamvu ya Moni

“MULI BWANJI?”

Mwacionekele, nthawi zambili mumakamba mau amenewa popatsa ena moni. Nthawi zina, popeleka moni timacita kugwilana kumanja kapena kugwada. Zimene anthu amakamba na kucita popeleka moni, zimasiyana malinga ndi madela amene amakhala. Koma zolinga zopelekela moni n’zolingana. Ndipo ena amaona kuti kusapatsa ena moni kapena kusayankha akatipatsa moni, n’kusoŵa cikondi kapena kupanda ulemu.

Koma anthu ena sakhala omasuka kupeleka moni, cifukwa ca manyazi kapena cifukwa codziona monga osafunika. Kwa ena, cimakhala covuta kupeleka moni kwa anthu cifukwa cosiyana mtundu, cikhalidwe, udindo, msinkhu, kumene anakulila, kapena cifukwa cakuti si mwamuna kapena mkazi mnzawo. Koma kupeleka moni, ngakhale wacidule cabe, kungakhale na zotulukapo zabwino.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi kupeleka moni kuli na ubwino wanji? Nanga Mau a Mulungu amaphunzitsanji pa nkhani yopeleka moni?’

MUZIPELEKA MONI KWA ANTHU AMTUNDU ULIWONSE

Koneliyo anali munthu woyamba kukhala Mkhristu kucokela ku mitundu ina. Pomulandila mumpingo wacikhristu, mtumwi Petulo anati: “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Pambuyo pake, Petulo analemba kuti Mulungu “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Nthawi zambili, tikamva mau amenewa timaganizila za anthu amene akuphunzila coonadi. Koma Petulo analangiza Akhristu kuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale.” (1 Pet. 2:17) Conco, ni bwino kumapatsa moni anthu ena, mosasamala kanthu za mtundu wawo, cikhalidwe, kapena kumene anakulila. Kucita izi kumaonetsa kuti timawakonda na kuwalemekeza.

Mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Landilanani, monga mmene Khristu anatilandilila.” (Aroma 15:7) Iye anachula maina a abale amene anali ‘kumulimbikitsa.’ Kulimbikitsana n’kofunika kwambili, maka-maka masiku ano, cifukwa Satana akulimbana kwambili ndi anthu a Mulungu.—Akol. 4:11; Chiv. 12:12, 17.

Zitsanzo za m’Baibo zimaonetsa kuti kupeleka moni sikuthandiza cabe anthu kukhala omasuka, koma kumathandizanso m’njila zina zambili.

KUPELEKA MONI NI NJILA YOLIMBIKITSILA ENA NA KUWAONETSA CIKONDI

Yehova atatsala pang’ono kusamutsila moyo wa Mwana wake m’mimba mwa Mariya, anatumiza mngelo kuti akakambe naye. Mngeloyo anayamba na moni. Anati: “Mtendele ukhale nawe, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.” Mariya ‘anadabwa kwambili’ na mau amenewa. Iye sanadziŵe kuti n’cifukwa ciani mngeloyo anali kukamba naye. Poona zimenezi, mngeloyo anati: “Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomela mtima.” Ndiyeno anafotokozela Mariya kuti colinga ca Mulungu n’cakuti iye adzabeleke Mesiya. Mariya sanakhalebe wodabwa, ndipo mwaulemu anayankha kuti: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zicitike ndithu kwa ine.”—Luka 1:26-38.

Mngeloyo anaona kuti ni mwayi wapadela kupeleka uthenga umenewu wocokela kwa Yehova. Sanadzione kuti ni wapamwamba kwambili cakuti sangakambe na munthu wopanda ungwilo. Ndipo pokamba na Mariya, anayamba mwa kupeleka moni. Tingaphunzilepo ciani pamenepa? Tiyenela kukhala okonzeka kupatsa anthu moni na kuwalimbikitsa. Mwa kupeleka moni, tingathandize ena kudziona kuti ni ofunika pakati pa anthu a Yehova.

Mtumwi Paulo anali kudziŵa Akhristu ambili a m’mipingo ya ku Asia Minor na ku Europe. M’makalata ake, anachula maina awo na kuwapatsa moni. Citsanzo ni zimene analemba mu Aroma caputa 16. Paulo anapeleka moni kwa Akhristu anzake ambili. Iye anachula Febe kuti “mlongo wathu,” ndipo analimbikitsa abale kuti ‘amulandile mwa Ambuye mmene analandilila oyelawo, ndi kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo lawo.’ Paulo anapeleka moni kwa Purisika ndi Akula, ndipo anakamba kuti iye “komanso mipingo yonse ya anthu a mitundu ina,” anali kuwayamikila. Paulo anapelekanso moni kwa Akhristu ena a m’nthawi yake, amene masiku ano si odziŵika kweni-kweni. Anapeleka moni kwa ‘wokondedwa wake Epeneto,’ ndiponso “Turufena ndi Turufosa, akazi ogwila nchito mwakhama potumikila Ambuye.” Inde, Paulo anali kukonda kupeleka moni kwa abale na alongo ake.—Aroma 16:1-16.

Mwacionekele, iwo anakondwela kudziŵa kuti Paulo anali kuwaganizila. Ndipo izi ziyenela kuti zinalimbitsa kwambili cikondi cawo kwa Paulo komanso pakati pawo. Kuwonjezela apo, moni wacikondi umenewo unalimbikitsa Akhristu ena na kuwathandiza kukhalabe olimba m’cikhulupililo. Inde, kupeleka moni wocokela pansi pamtima na kuyamikila ena kungalimbitse ubwenzi wathu na iwo. Ndiponso kumagwilizanitsa atumiki a Mulungu okhulupilika.

Pamene mtumwi Paulo anafika pa doko la ku Potiyolo, ananyamuka ulendo wake wopita ku Roma. Atayandikila ku Roma, Akhristu a kumeneko anabwela kuti amulandile. Paulo atawaona capatali “anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:13-15.) Nthawi zina, tingapeleke moni kwa ena mwa kumwetulila cabe kapena kuwakwezela dzanja. Izi zingaoneke ngati zazing’ono, koma zingalimbikitse munthu, ngakhale amene ni wopanikizika maganizo kapena wokhumudwa.

POYAMBILA PABWINO

Nthawi ina, mtumwi Yakobo anafuna kupeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu anzake. Ena mwa Akhristuwo anali kucita cigololo cauzimu mwa kukhala paubwenzi na dziko. (Yak. 4:4) Conco, iye anawalembela kalata. Koma kodi anayamba bwanji kalata yake asanapeleke uphungu?

Anayamba na mau akuti: “Ine Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikupeleka moni kwa mafuko 12 amene ali obalalika.” (Yak. 1:1) Mwacionekele, sicinali covuta kwa Akhristuwo kulandila uphungu wake, cifukwa moni umene anawapatsa unaonetsa kuti nayenso anali kapolo mnzawo kwa Mulungu. Ndithudi, kupeleka moni modzicepetsa kungathandize munthu kukhala womasuka musanayambe kukamba naye nkhani yaikulu.

Kuti moni wathu ukhale wolimbikitsa, olo kuti ni wacidule, tifunika kuupeleka mocokela pansi pamtima ndi mwacikondi. Tiyenela kucita izi ngakhale kuti munthu amene tam’patsa moniyo sanaikileko nzelu. (Mat. 22:39) Mwacitsanzo, tsiku lina mlongo wina wa ku Ireland anafika pa Nyumba ya Ufumu misonkhano itangotsala pang’ono kuyamba. Pamene anali kuloŵa, m’bale wina anamwetulila na kukamba kuti: “Mwacoma bwanji? Takulandilani.” Mlongoyo anangokhala pampando osayankha.

Patapita mawiki angapo, mlongoyo anapita kwa m’bale uja na kumufotokozela kuti kwa nthawi yaitali, iye wakhala akulimbana na vuto lalikulu kunyumba kwake. Iye anati: “Tsiku lija n’nali wokhumudwa ngako, cakuti n’natsala pang’ono kuphonya misonkhano. Zambili zimene tinaphunzila pa misonkhano ija sinizikumbukila, kupatulapo moni wanu. Unanithandiza kukhala womasuka. Zikomo kwambili.”

Poyamba m’baleyo sanazindikile mphamvu ya moni wacidule umene anapeleka. Iye anakamba kuti: “Pamene mlongoyo ananiuza mmene moni wanga wacidule unamukhudzila, n’nakondwela kuti n’namupatsa moni. N’namvela bwino kwambili.”

Solomo analemba kuti: “Tumiza mkate wako pamadzi, cifukwa pakapita masiku ambili udzaupezanso.” (Mlal. 11:1) Ngati tiyesetsa kupeleka moni kwa ena, maka-maka Akhristu anzathu, timawalimbikitsa, ndipo na ise timalimbikitsidwa. Conco, sitiyenela kudelela mphamvu ya moni.