Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Yakobo anakhala kholo la Mesiya cifukwa cogula udindo kwa Esau wokhala woyamba kubadwa?

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

M’nthawi ya Aisiraeli, kodi kukhala pa mzela wa makolo a Mesiya kunadalila kukhala oyamba kubadwa?

M’mbuyomu, takambapo zoonetsa zimenezi. Ndipo zinaoneka kukhala zogwilizana na lemba la Aheberi 12:16. Limati Esau ‘sanayamikile zinthu zopatulika,’ ndipo “anapeleka [kwa Yakobo] udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi cakudya codya kamodzi kokha.” Izi zinamveka ngati kuti pamene Yakobo anatenga udindo wokhala woyamba kubadwa, analoŵa pa mzela wa makolo a Mesiya.—Mat. 1:2, 16; Luka 3:23, 34.

Komabe, kuzionanso bwino nkhani za m’Baibo kuonetsa kuti munthu sanafunikile kukhala woyamba kubadwa kuti akhale kholo la Mesiya. Tiyeni tioneko maumboni ena:

Pa ana a Yakobo (Isiraeli), woyamba kubadwa mwa Leya anali Rubeni. Pambuyo pake, Yakobo anabala Yosefe, mwana wake woyamba kwa mkazi wake wokondeka, Rakele. Pamene Rubeni anacita colakwa, udindo monga woyamba kubadwa unacoka kwa iye n’kupita kwa Yosefe. (Gen. 29:31-35; 30:22-25; 35:22-26; 49:22-26; 1 Mbiri 5:1, 2) Ngakhale n’conco, mzela wa makolo a Mesiya sunapitile mwa Rubeni kapena Yosefe, koma mwa Yuda, mwana wacinayi wa Yakobo kwa Leya.—Gen. 49:10.

Luka 3:32 imachula anthu enanso asanu pa mzela wa makolo a Mesiya. Zioneka kuti aliyense wa iwo anali woyamba kubadwa. Boazi anabala Obedi, amenenso anadzabala Jese.—Rute 4:17, 20-22; 1 Mbiri 2:10-12.

Komabe, Davide mwana wa Jese sanali woyamba kubadwa. Iye anali wothela pa ana 8 aamuna. Koma mzela wobadwila wa Mesiya unapitila mwa Davide. (1 Sam. 16:10, 11; 17:12; Mat. 1:5, 6) Wotsatila anali Solomo, ndipo nayenso sanali woyamba kubadwa.—2 Sam. 3:2-5

Koma izi sizitanthauza kuti kukhala woyamba kubadwa kunalibe phindu. Kukhala mwana woyamba kubadwa wamwamuna unali udindo wolemekezeka, ndipo nthawi zambili iye ndiye anali kuyang’anila banja atate ake akamwalila. Komanso, ndiye anali kulandila magawo aŵili a coloŵa.—Gen. 43:33; Deut. 21:17; Yos. 17:1.

Koma zinali zotheka kucotsa udindo wokhala woyamba kubadwa kucoka kwa wina kupita kwa wina. Mwacitsanzo, Abulahamu anacotsa udindo umenewu kwa Isimaeli n’kuupeleka kwa Isaki. (Gen. 21:14-21; 22:2) Komanso monga mmene takambila, udindo wokhala woyamba kubadwa unacotsedwa kwa Rubeni n’kupelekedwa kwa Yosefe.

Tsopano tiyeni tikambilanenso lemba la Aheberi 12:16, limene limati: “Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikila zinthu zopatulika, ngati Esau, amene anapeleka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi cakudya codya kamodzi kokha.” Ni mfundo yanji maka-maka imene mtumwi Paulo anali kukamba pa lembali?

Mtumwi Paulo pamenepa sanali kufotokoza za mzela wobadwila wa Mesiya. Iye anali atangolimbikitsa kumene Akhristu ‘kuwongola njila zimene mapazi awo anali kuyendamo.’ Mwa ici, iwo akanalandila “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” Koma kucita ciwelewele kukanawalepheletsa kulandila kukoma mtimako. (Aheb. 12:12-16) Mwa kucita ciwelewele, iwo akanakhala ngati Esau, amene analephela ‘kuyamikila zinthu zopatulika,’ cifukwa cocita dyela na zinthu zakuthupi.

Esau anakhalako m’nthawi ya makolo akale, ndipo n’kutheka kuti nthawi zina anali kukhala na mwayi wopelekako nsembe. (Gen. 8:20, 21; 12:7, 8; Yobu 1:4, 5) Koma cifukwa cokonda zinthu zakuthupi, iye anasinthanitsa mwayi umenewo na cakudya ca mphodza codya kamodzi kokha. Mwina iye anacita izi pofuna kupewa mavuto amene analoseledwa kuti adzacitikila mbadwa za Abulahamu. (Gen. 15:13) Esau anaonetsanso kuti anali kukonda zinthu zakuthupi ndi kusayamikila zinthu zopatulika, mwa kukwatila akazi aŵili a mitundu ina. Izi zinabweletsa cisoni kwa makolo ake. (Gen. 26:34, 35) Iye anali wosiyana ngako na Yakobo, amene anaonetsetsa kuti wakwatila mkazi wolambila Mulungu woona.—Gen. 28:6, 7; 29:10-12, 18.

Kodi zimene takambilanazi zatiphunzitsa ciani ponena za mzela wobadwila wa Yesu, Mesiya? Taona kuti nthawi zina mzelawo unali kupitila mwa mwana woyamba kubadwa, koma osati nthawi zonse. Ayuda anali kuidziŵa mfundo imeneyi na kuivomeleza. Ndiye cifukwa cake iwo anavomeleza kuti Khristu ni mbadwa ya Davide, mwana wa Jese wothela.—Mat. 22:42.