NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA August 2017

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya September 25-October 22, 2017.

Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?

Atumiki a Yehova okhulupilika akale anafunsa Mulungu kuti adziŵe kuti adzakumana ndi mavuto mpaka liti. Koma iye sanawadzudzule.

“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”

Kodi munadzifunsapo kuti n’cifukwa ciani Mulungu analola kuti mukumane na mavuto ena ake? Ngati n’conco, n’ciani cingakuthandizeni kupilila na kuika cidalilo conse mwa Yehova?

MBILI YANGA

Kupilila Ziyeso Kumabweletsa Madalitso

N’cifukwa ciani Mboni zimene zinaikidwa ku Siberia zinali kufunsa ng’ombe zogula pamene m’ceni-ceni zinali kufuna nkhosa? Yankho tingaipeze m’nkhani yolimbikitsa yofotokoza mbili ya Pavel ndi Maria Sivulsky.

Mmene Timavulila Umunthu Wakale ndi Kusauvalanso

Tifunika kucita khama kuti tivule umunthu wakale ndi kuyesetsa kuti tisauvalenso. Tingakwanitse bwanji kucita zimenezi, ngakhale kuti mwina tinazoloŵela kwambili makhalidwe oipa?

Mmene Timavalila Umunthu Watsopano ndi Kusauvulanso

Ndi thandizo la Yehova, tingakwanitse kukhala na makhalidwe amene Mulungu afuna. Ganizilani mmene mungaonetsele makhalidwe monga cifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, na kufatsa.

Cikondi—Khalidwe Lamtengo Wapatali

Malemba amaonetsa kuti cikondi ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela wa Yehova umabala. Kodi cikondi n’ciani maka-maka? Kodi mungakulitse bwanji khalidwe limeneli? Nanga mungalionetse bwanji pa zocita zanu za tsiku na tsiku?

ZA M'NKHOKWE YATHU

“N’liti Pamene Tidzakhala na Msonkhano Wina Waukulu?”

N’ciani cinacititsa msonkhano wa mu 1932 ku Mexico City kukhala wapadela, ngakhale kuti anthu opezekapo anali ocepa?

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

N’cifukwa ciani zimene Mateyu na Luka analemba zokhudza umoyo wa Yesu ali mwana, ndi mzela wake wobadwila zimasiyana?