NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA April 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya June 4-July 8, 2018.

Njila Yopezela Ufulu Weni-weni

Anthu ambili amalakalaka kukhala omasuka ku mavuto monga umphawi, tsankho, na kupondelezedwa, ndipo ena amafuna kukhala na ufulu wolankhula kapena wodzisankhila zocita. Kodi n’zotheka kukhala na ufulu weni-weni?

Tumikilani Yehova, Mulungu wa Ufulu

Kodi mzimu wa Yehova unatimasula bwanji? Nanga tingapewe bwanji kuseŵenzetsa molakwika ufulu umene Mulungu anatipatsa?

Amuna a Paudindo—Tengelani Citsanzo ca Timoteyo

Cioneka kuti Timoteyo anali kudzikayikila pamene anayamba kutumikila pamodzi na mtumwi Paulo. Kodi akulu na atumiki othandiza angaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Timoteyo?

Tengelani Yehova—Mulungu Amene Amapeleka Cilimbikitso

Kuyambila kale, anthu a Yehova akhala akufunikila cilimbikitso.

“Tiyeni Tilimbikitsane, Ndipo Tiwonjezele Kucita Zimenezi”

Popeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi, tiyenela kumaganizila kwambili za umoyo wa abale na alongo athu kuti tiwalimbikitse pamene kuli kofunikila.

Acicepele, Kodi Mumaika Zolinga Zauzimu Patsogolo?

Nthawi zina, acicepele kupanga zosankha kumawavuta. Kodi angapange bwanji zosankha mwanzelu pa nkhani zimene zimakhudza tsogolo lawo?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciani n’kosaloleka kuti munthu aziika zofalitsa za Mboni za Yehova pa mawebusaiti ena kapena pa malo ocezela a pa intaneti?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciani mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso, mau a pa Salimo 144 anasinthiwako?