Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 3 2021 | Kodi Muyenela Kukhulupilila Kuti Kuli Mlengi?

Anthu ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya mmene cilengedwe na moyo padziko zinayambila. Magazini ino ya Galamuka! ikuthandizani kudziŵa mfundo zina zocititsa cidwi pankhaniyi, zimene zidzakuthandizani kusankha nokha zoyenela kukhulupilila. Kodi zam’cilengedwe zinangokhalako zokha kapena zinacita kulengedwa na Mulungu? Kudziŵa yankho pa funso limeneli kungakupindulitseni kwambili.

 

Kodi Mungakhulupilile Ziti?

Anthu ambili amathedwa nzelu na mafunso okhudza cilengedwe komanso mmene moyo unayambila.

Zimene Cilengedwe Cimatiuza

Zinthu zonse zam’cilengedwe, kuphatikizapo dziko lapansi zimaoneka kuti zinapangidwa m’njila yakuti moyo ukhalepo. Kodi n’kutheka kuti zimaoneka conco cifukwa zinapangidwa na winawake?

Zimene Zamoyo Zimatiuza

Zamoyo zimapangitsa pulaneti lathuli kukhala lokongola kwambili. Kodi zamoyo zimatiuza ciani ponena za mmene moyo unayambila?

Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza

Kodi asayansi amadziŵa mmene cilengedwe kuphatikizapo moyo zinayambila?

Zimene Baibo Imatiuza

Kodi zimene imakamba zimagwilizana na mfundo zotsimikizika za sayansi?

Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika

Ngati mwakhutila na umboni wakuti kuli Mulungu wamphamvuzonse, mungapindule palipano komanso m’tsogolo.

Pendani Umboni

Onani nokha ngati pali cifukwa cokhulupilila kuti kuli Mlengi.