Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Luso Lanu Lophunzila Zinthu?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Luso Lanu Lophunzila Zinthu?

Anthu amafuna kuphunzila zinthu zambili, kaya za kusukulu, za kunchito, kapena zinthu zina. Ndipo zipangizo zamakono zingawathandize. Kuposa kale lonse, tsopano n’zosavuta anthu kuphunzila zinthu zambili ali kunyumba kwawo, ngakhale ali phee pampando.

Komabe, ambili amene amakonda kuseŵenzetsa kwambili zipangizo zamakono, amakhala na mavuto monga . . .

  • kulephela kuika maganizo awo pa zimene akuŵelenga.

  • kulephela kuika maganizo pa cinthu cimodzi.

  • kusungulumwa mwamsanga akakhala paokha.

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

KUŴELENGA

Anthu amene amakonda kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, nthawi zina amangoŵelenga nkhani mwapatali-patali kapena mothamanga, moti sakwanitsa kumvetsa mfundo yaikulu ya nkhaniyo.

Kuŵelenga mothamanga kumathandiza ngati mufuna kupeza yankho mwamsanga pa funso linalake. Koma kuŵelenga kotelo si kwabwino ngati nkhani imene mukuŵelenga mufuna kuimvetsetsa.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumakwanitsa kuŵelenga nkhani yaitali mosamala? Nanga kucita zimenezi kungakuthandizeni bwanji pophunzila zinthu?—MIYAMBO 18:15.

KUIKA MAGANIZO PA CINTHU CIMODZI

Anthu ena amaganiza kuti zipangizo zamakono zingawathandize kucita zinthu ziŵili pa nthawi imodzi—mwacitsanzo, kulembela meseji bwenzi lawo kwinaku akuŵelenga. Koma popeza kuti maganizo awo amakhala ogaŵikana, sangacite bwino zonse ziŵili makamaka ngati zonse zifuna kuikilapo mtima.

Kuika maganizo pa cinthu cimodzi cimene mukucita kungakhale kovuta, koma kumathandiza kuti muphunzile zinthu. Mtsikana wina dzina lake Grace anati: “Sulakwitsa zinthu zambili komanso supanikizika maganizo kwambili. Naphunzila kuti ni bwino kuika maganizo anga pa cinthu cimodzi na kupewa kuceutsidwa na zinthu zina.”

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumalephela kumvetsetsa na kukumbukila zimene mwaŵelenga cifukwa coyesa kucita zinthu zingapo pa nthawi imodzi?—MIYAMBO 17:24.

PAMENE MULI NOKHA

Anthu ena samvela bwino kukhala okha pamalo a zii, ndipo amayamba kuseŵenzetsa zipangizo zawo pofuna kudzisangulutsa. Mzimayi wina dzina lake Olivia anati: “Cimanivuta kungokhala phee kwa mphindi 15 popanda kugwila foni yanga, kapena tabuleti, kapenanso kuyatsa TV.”

Komabe, nthawi imene munthu ali yekha, imam’patsa mwayi wosinkhasinkha, ndipo kusinkhasinkha n’kofunika kwambili kuti munthu aphunzile zinthu, kaya ni mwana kapena wamkulu.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Pamene muli nokha, kodi mumakwanitsa kuseŵenzetsa mpata umenewo posinkhasinkha?—1 TIMOTEYO 4:15

ZIMENE MUNGACITE

PENDANI MMENE MUMASEŴENZETSELA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Kodi mungaseŵenzetse bwanji zipangizo zamakono kuti zikuthandizeni pophunzila zinthu? Kodi kuseŵenzetsa zipangizo zamakono kungakulepheletseni bwanji kuganizila zinthu mozama pophunzila?

MFUNDO YA M’BAIBO: “Usunge nzelu zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”—MIYAMBO 3:21.