Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cilango cimatsogolela mwana monga mmene coongolela boti cimathandizila kuti iziyenda bwino

KWA MAKOLO

6: Cilango

6: Cilango

ZIMENE CIMATANTHAUZA

Mau akuti cilango angatanthauze kutsogolela kapena kuphunzitsa. Nthawi zina, zimenezi zimaphatikizapo kulangiza mwana kuti asiye khalidwe loipa. Koma kaŵili-kaŵili kumaphatikizapo kum’phunzitsa makhalidwe abwino, amene angam’thandize kupanga zosankha zabwino kuyambila ali mwana.

CIFUKWA CAKE N’COFUNIKA

Masiku ano, makolo ena analekelatu kupeleka cilango kwa ana awo kuopela kuti mwina angayambe kudziona osafunika. Komabe, makolo anzelu amaika malamulo oyenelela na kuphunzitsa ana awo kutsatila malamulowo.

“Ana amafunika kuwapatsa malamulo kuti akule bwino. Popanda cilango, ana amakhala monga boti imene ilibe coongolela, imene pothela pake ingapindamuke.”—Pamela.

ZIMENE MUNGACITE

Muzicita zimene mwakamba. Ngati mwana wanu satsatila malamulo anu, musalephele kum’patsa cilango. Koma mufunika kukhala wokonzeka kumuyamikila akatsatila malamulo anu.

“Nimayamikila ana anga kaŵili-kaŵili cifukwa cokhala omvela m’dziko limene ambili ni osamvela. Kuwayamikila kumawathandiza kuti azilandila uphungu mosavuta akalakwitsa.”—Christine.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.”—Agalatiya 6:7.

Muzipeleka cilango coyenelela. Popeleka cilango kwa mwana, muziganizila zaka zake, zimene amadziŵa, komanso kukula kwa colakwa cimene wacita. Cilango cimakhala cothandiza kwambili ngati cigwilizana ndi zimene mwana walakwa. Mwacitsanzo, ngati mwana wanu saseŵenzetsa bwino foni, mungamulande foniyo kapena kumuletsa kucita zinthu zina pafoni kwa kanthawi. Komabe, pewani kukulitsa nkhani zing’ono-zing’ono, cabe cifukwa cakuti simunakondwele na zimene mwana wacita.

“Nimayesetsa kuona ngati mwana wanga walakwitsa zinthu mwadala, kapena wangocita zinthu mosaganiza bwino. Pali kusiyana pakati pa kukhala na cizoloŵezi ca khalidwe loipa limene lingafunike kulithetsa, na kulakwitsa kumene kungafunikile cabe kum’thandiza kuti azindikile zimenezo.”—Wendell.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.

Muziwalangiza mwacikondi. Zimakhala zosavuta ana kulandila cilango na kugwililapo nchito ngati adziŵa kuti makolo awo acita zimenezo cifukwa coŵakonda.

“Mwana wathu akalakwitsa zina zake, tinali kumutsimikizila kuti timakondwela ndi zabwino zimene anacita m’mbuyomo. Tinali kumufotokozela kuti mbili yake siingawonongeke malinga ngati waongolela zimene walakwitsa, ndipo ise tilipo kuti tim’thandize kucita zimenezo.”—Daniel.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.”—1 Akorinto 13:4.