Onani zimene zilipo

KUCEZA NA | RACQUEL HALL

Mzimayi Waciyuda Afufuzanso Mozama Cikhulupililo Cake

Mzimayi Waciyuda Afufuzanso Mozama Cikhulupililo Cake

Mayi ake a Racquel Hall ni Myuda ndipo kwawo ni ku Israel pomwe bambo ake ni a ku Austria koma anayamba Ciyuda. Agogo ake akucikazi anali m’gulu lomenyela ufulu wa Ayuda ndipo anasamukila ku Israel mu 1948. Caka cimeneci ni cimene dziko la Israel linayamba kudzilamulila lokha. Mtolankhani wa Galamuka! anafunsa Racquel cimene cinam’pangitsa kuti aganizilenso za cikhulupililo cake ca Ciyuda.

Tiuzeni za moyo wanu.

N’nabadwila ku United States m’caka ca 1979. Nili na zaka zitatu, ukwati wa makolo anga unatha. Cifukwa ca zimenezi n’naleledwa na mayi anga okha ndipo ananiphunzitsa cikhalidwe caciyuda. N’nali kupitanso kusukulu ya Ciyuda. Nili na zaka 7, tinasamukila ku Israel ndipo tinakhalako caka cimodzi. N’nayamba sukulu ina ya komweko yomwe amaicha kibbutz. Kenako tinasamukila ku Mexico.

Ngakhale kuti kudela limene tinali kukhala kunalibe masunagoge, n’nali kuyesetsabe kutsatila cikhalidwe ca Ciyuda. Tsiku la Sabata likakwana, n’nali kuyatsa makandulo, kuŵelenga buku la Ciyuda lochedwa Torah komanso kupemphela pogwilitsa nchito buku lamapemphelo. Nikakhala kusukulu, n’nali kukonda kuuza anzanga kuti zipembedzo zonse zinacokela m’cipembedzo cathu. N’nali nisanaŵelengepo Cipangano Catsopano comwe cimanena zimene Yesu Khristu anali kuphunzitsa komanso utumiki wake. Ndipo mayi anga anali kuniletsa kuti nisadzayelekeze kuŵelenga Cipangano Catsopano cifukwa cidzanisokoneza.

Ndiye n’ciani cinakupangitsani kuŵelenga Cipangano Catsopano?

N’takwanitsa zaka 17, n’nasamukilanso ku United States kuti nikamalize maphunzilo anga. Nili kumeneko, mnzanga wina yemwe anali Mkhristu ananiuza kuti siningakhale wosangalala popanda kudziŵa za Yesu.

Ataniuza zimenezi n’namuyankha kuti: “Anthu amene amakhulupilila Yesu ni osoceletsedwa.”

Ananifunsa kuti: “Kodi iwe unaŵelengapo Cipangano Catsopano?”

N’namuyankha kuti: “Ayi.”

Kenako ananiuza kuti: “Ndiye ungaweluze bwanji kuti anthu amene amakhulupilila Yesu ni osoceletsedwa pomwe iweyo sudziŵa ciliconse cokhudza Yesu?”

Zimene ananenazo zinanipweteka kwambili cifukwa pamoyo wanga nimaona kuti munthu amene amafulumila kuweluza anzake iye asakudziŵapo ciliconse pa nkhaniyo ni wopusa. Mwamanyazi n’natenga Baibo yake n’kukayamba kuŵelenga Cipangano Catsopano.

Kodi zimene munaŵelengazo zinakukhudzani bwanji?

N’nadabwa kwambili kudziŵa kuti amene analemba Cipangano Catsopano anali Ayuda. Komanso pamene n’nali kuŵelenga, n’nali kuona kuti Yesu anali Myuda wacifundo, wodzicepetsa komanso wofunitsitsa kuthandiza anthu osati kuwadyela masuku pamutu. Moti n’napita ku laibulale kukabweleka mabuku ofotokoza za Yesu. Komabe mabuku onsewo sananipatse umboni woti Yesu anali Mesiya. Mabuku ena anali kufotokoza kuti Yesu ni Mulungu, zomwe zinali kunisokoneza kwambili. N’nali kudzifunsa kuti ngati Yesu ali Mulungu, ndiye popemphela anali kupemphela kwa ndani? Komanso Yesu anafa, pomwe Baibo imati: “Inu [Mulungu] simufa.” *

Munatani kuti mupeze mayankho pa mafunso amenewo?

N’nali kufunitsitsa kudziŵa coonadi cifukwa n’nali kudziŵa kuti coonadi sicidzitsutsa. N’napemphela kwa Mulungu mocokela pansi pamtima kwinaku nikukhetsa misozi. Aka kanali koyamba pamoyo wanga kuti nipemphele popanda kugwilitsa nchito buku lamapemphelo. N’tangomaliza kupemphela, n’namva kugogoda pacitseko. N’tatsegula n’naona kuti anali anthu aŵili a Mboni za Yehova. Iwo ananipatsa buku lothandiza pophunzila Baibo. N’taŵelenga bukuli komanso kuphunzila na a Mboniwa, n’nazindikila kuti zimene anali kukhulupilila zinali zocokela m’Baibo. Mwacitsanzo, a Mboni za Yehova amakhulupilila kuti Yesu sali mbali ya Utatu koma ni “Mwana wa Mulungu” * komanso “woyamba wa cilengedwe ca Mulungu.” *

Kenako n’nabwelelanso ku Mexico, komwe n’napitiliza kuphunzila na Mboni za Yehova za maulosi osiyana-siyana onena za Mesiya. N’nadabwa kuona kuti pali maulosi ambili onena za Mesiya. Koma n’nali kukayikilabe. N’nali kudzifunsa kuti: ‘Kodi ni Yesu yekha amene anacita zinthu mogwilizana na maulosi amenewa? Kodi sizingatheke kuti Yesu anali kucita zinthu mocenjela kuti azioneke ngati maulosiwo akukwanilitsidwa pa iye?’

N’ciani cinakupangitsani kukhulupililadi kuti Yesu ni Mesiya?

A Mboni za Yehova ananionetsa maulosi osiyana-siyana omwe munthu sangathe kuwakwanilitsa ngakhale atacita zinthu mocenjela. Mwacitsanzo, kutatsala zaka 700 kuti Mesiya abadwe, mneneli Mika analoselelatu kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu wa ku Yudeya. * Kodi pali munthu amene angasankhe yekha kumene akabadwile? Yesaya ananenelatunso kuti Mesiya adzaphedwa ngati cigawenga koma adzaikidwa m’manda na anthu olemela. * Yesu yekha ni amene anakwanilitsa maulosi onsewa.

Umboni winanso ni mzela umene Yesu anabadwila. Baibo linaloselelatu kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. * Ayuda akale anali kusunga mipukutu ya mibadwo ya makolo. Zikanakhala kuti Yesu sanabadwile mumzela wa Davide, adani ake akanatsutsa zoti Yesu ni Mesiya. Koma sananene ciliconse cifukwa aliyense anali kudziŵa kuti Yesu ni mbadwa ya Davide. Ndipo nthawi ina, khamu la anthu linali kumukuwila Yesu kuti “Mwana wa Davide.” *

M’caka ca 70 C.E., patatha zaka 37 Yesu atamwalila, asilikali aciroma anawononga mzinda wa Yerusalemu ndipo mipukutu ija inawonongedwa ndipo ina inasowa. Conco kuti anthu adziŵedi kuti Yesu ni Mesiya yemwe anabadwila mumzela wa Davide, anayenela kuonekela cisanafike caka ca 70 C.E.

Zimenezi zinakukhudzani bwanji?

Pa Deuteronomo 18:18, 19 pali ulosi wonena kuti Mulungu adzapatsa Aisiraeli mneneli ngati Mose. Pa ulosiwu Mulungu ananena kuti: “Amene sadzamvela mawu anga amene iye adzalankhule m’dzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.” N’tafufuza mozama m’Baibo lonse n’napeza kuti mneneli ameneyu anali Yesu wa ku Nazareti.

^ ndime 15 Habakuku 1:12.

^ ndime 17 Yohane 1:34.

^ ndime 17 Chivumbulutso 3:14.

^ ndime 20 Yesaya 53:3, 7, 9; Maliko 15:43, 46.

^ ndime 21 Yesaya 9:6, 7; Luka 1:30-32. M’buku la Mateyu caputala 1 muli mndandanda wa maina a makolo a Yosefe, omwe anali bambo ake a Yesu, ndipo m’buku la Luka caputala 3 muli mndandanda wa maina a makolo a Mariya.