Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pemphani Thandizo

Pemphani Thandizo

Pemphani Thandizo

“Ndipo wina akam’laka mmodziyo, aŵili adzacilimika.”—Mlaliki 4:12.

NGATI tili na anthu otithandiza pamene tikumenyana na mdani, kaya mdaniyo akhale wamphamvu bwanji, nthawi zambili timapambana. Conco, ngati mukufuna kugonjetsa cizolowezi cosuta fodya, mungapemphe anthu ena kuti akuthandizeni. Mungapemphe anthu a pabanja panu, anzanu, kapena anthu ena amene mukuona kuti angakuthandizeni.

Anthu amene poyamba anali kusuta fodya koma anasiya angakuthandizeni kwambili cifukwa angamvetse vuto lanu komanso angadziŵe mmene angakuthandizileni. Bambo wina wa ku Denmark, dzina lake Torben, anati: “Thandizo limene ena ananipatsa kuti nisiye kusuta fodya linali lofunika kwambili.” Abraham, yemwe amakhala ku India, analemba kuti: “Cikondi cimene anthu apabanja panga komanso Akhristu anzanga anali kunisonyeza cinanithandiza kwambili kuti nisiye kusuta.” Komabe nthawi zina thandizo limene acibale na anzanu angapeleke silingakhale lokwanila.

Mwacitsanzo, bambo wina dzina lake Bhagwandas anati: “Nakhala nikusuta fodya kwa zaka 27 koma nitadziŵa zimene Baibo imanena zokhudza zizolowezi zoipa, m’pamene n’naganiza zosiya kusuta. N’nayesetsa kuti nicepetse kusuta. N’napeza anzanga ena oceza nawo. Ndiponso n’napita kwa alangizi kuti anithandize. Koma palibe cinathandiza. Tsiku lina usiku n’napemphela kwa Yehova Mulungu kuti anithandize. Ndipo kenako n’nasiya kusuta.”

Cinthu cinanso cimene cingathandize ni kukonzekela mavuto amene mungakumane nawo ngati mutasiya kusuta. Kodi mungakumane ni mavuto otani? Nkhani yotsatila ifotokoza za mavuto amenewa.

KODI NI BWINO KUGWILITSA NCHITO

MANKHWALA?

Masiku ano kuli makampani ambili amene akupanga mankhwala othandiza anthu kusiya kusuta fodya ndipo akupanga ndalama zambili. Koma musanaganize zogwilitsa nchito mankhwala amenewa, dzifunseni mafunso otsatilawa:

Kodi ubwino wake ni wotani? Akuti mankhwala ambili otele amacepetsa cibaba komanso mavuto ena amene amabwela munthu akasiya kusuta fodya. Koma anthu ena amati mankhwalawa amangothandiza munthu kwa nthawi yocepa. Conco, ngati mukufuna kugwilitsa nchito mankhwala amenewa muyenela kufufuza kuti mudziŵe zenizeni.

Kodi kuopsa kwake n’kotani? Mankhwala ena amacititsa anthu kusanza, kukhumudwa, komanso kukhala na maganizo ofuna kudzipha. Dziŵani kuti mankhwala ena amakhalanso na nikotini amene amayambitsa matenda ena. Conco, munthu amene amagwilitsa nchito mankhwala amenewa, cilakolako cake cofuna kusuta fodya sicithelatu.

Kodi njila zina zosiyila fodya ni zotani? Pakafukufuku wina, pa anthu 100 aliwonse amene anakwanitsa kusiya kusuta fodya, 88 ananena kuti anangosiya popanda kugwilitsa nchito mankhwala aliwonse.