Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

UTUMIKI wathu ndi wofunika kwambili ndipo ndi wamtengo wapatali. Koma anthu ena amene timalalikila, saona conco. Ngakhale acite cidwi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, ena saona kufunika kophunzila nafe Mau a Mulungu.

Mwacitsanzo, taganizilani za Gavin. Iye anali kufika pa misonkhano ya mpingo, koma sanali kufuna kuphunzila Baibulo. Gavin anakamba kuti sanali kudziŵa zambili zokhudza Baibulo, ndipo sanafune kuti ena adziŵe zimenezo. Iye sanafune kuloŵa m’cipembedzo ciliconse cifukwa anali kuopa kunamizidwa. Muganiza bwanji, kodi zinali zotheka kuthandiza Gavin? Ganizilani zinthu zabwino zimene zimatulukapo munthu akaphunzila Baibulo. Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mau anga adzatsika ngati mame, ngati mvula yoŵaza pa udzu.” (Deuteronomo 31:19, 30; 32:2) Tiyeni tiphunzile zinthu zina zokhudza mame ndi kuona mmene utumiki wathu ulili ngati mame n’colinga cakuti tiziphunzitsa anthu mogwila mtima, “kaya akhale a mtundu wotani.”—1 Timoteyo 2:3, 4.

KODI UTUMIKI WATHU ULI NGATI MAME M’NJILA ZITI?

Mame amadontha pang’onopang’ono. Mame amapangika pang’onopang’ono pamene mpweya umasintha ndi kupanga tumadontho twa madzi. Kodi mau a Yehova ‘anatsika bwanji ngati mame’? Iye anali kukamba ndi anthu ake mokoma mtima, modekha, ndi mwacikondi. Tingatengele citsanzo cake mwa kulemekeza zimene ena amakhulupilila. Tiyenelanso kuwathandiza kuganizila mfundo zimene tikuwaphunzitsa ndi kusankha okha zocita. Tikamaonetsa cidwi anthu ena, io adzakhala okonzeka kumvetsela uthenga wathu, ndipo ulaliki wathu udzakhala wogwila mtima.

Mame amatsitsimula. Ulaliki wathu ungakhale wotsitsimula tikamagwilitsila nchito njila zosiyanasiyana pophunzitsa anthu coonadi. Chris, m’bale amene anayamba kuphunzila Baibulo ndi Gavin, sanakakamize Gavin kuti ayambe kuphunzila Baibulo. M’malomwake, iye anagwilitsila nchito njila zosiyanasiyana kuti am’thandize kuyamba kuphunzila Baibulo. Chris anauza Gavin kuti m’Baibulo muli uthenga wofunika kwambili, ndipo kuphunzila uthengawo kungamuthandize kupindula ndi misonkhano. Kenako, Chris anauza Gavin kuti maulosi a m’Baibulo ndi amene anamuthandiza kukhulupilila kuti Baibulo limakamba zoona. Pambuyo pake, io anayamba kukambilana maulosi ndi mmene anakwanilitsidwila. Gavin anatsitsimulidwa ndi makambilano amenewo, ndipo anayamba kuphunzila Baibulo.

Mame ndi ofunika kwambili pa moyo. M’nyengo yotentha ku Isiraeli, nthawi zina mvula sikugwa kwa miyezi ingapo. Popanda mame, zomela zimafota ndi kufa. Yehova ananenelatu kuti masiku ano, m’dziko mudzakhala ngati muli cilala, kutanthauza kuti anthu adzakhala ndi ludzu “lofuna kumva mau a Yehova.” (Amosi 8:11) Iye analonjeza kuti odzozedwa adzakhala “ngati mame ocokela kwa Yehova,” pamene akulengeza uthenga wabwino wa Ufumu mothandizidwa ndi a “nkhosa zina.” (Mika 5:7; Yohane 10:16) Uthenga umene timalalikila ndi njila ina imene Yehova amathandizila anthu amene ali ndi ludzu la coonadi kuti adzapeze moyo. Kodi timaona uthenga umenewu kukhala wofunika kwambili?

Mame ndi dalitso locokela kwa Yehova. (Deuteronomo 33:13) Ulaliki wathu ungakhale dalitso, kapena mphatso kwa anthu amene angaulandile. Gavin anadalitsidwa cifukwa cophunzila Baibulo ndipo anapeza mayankho a mafunso ake onse. Iye anapita patsogolo mwamsanga, kenako anabatizidwa, ndipo panopa iye ndi mkazi wake Joyce, amasangalala kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu.

Mboni za Yehova zikulalikila uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi

MUZIONA UTUMIKI WANU KUKHALA WOFUNIKA KWAMBILI

Kuyelekezela nchito yathu ndi mame, kungatithandizenso kuona kuti khama limene aliyense wa ife amacita mu ulaliki n’lofunika kwambili. Cifukwa ciani tikutelo? Kadontho kamodzi ka madzi kamacita zocepa, koma madontho ambili amanyowetsa nthaka. Mofananamo, nthawi zina mungaone kuti zimene mumacita mu ulaliki sizokwanila. Koma cifukwa ca khama la atumiki onse a Yehova, amene alipo mamiliyoni ambili, uthenga wabwino ukulengezedwa “ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Kodi utumiki wathu ndi dalitso la Yehova kwa ena? Ndithudi, uthenga wathu udzakhala ngati mame amene amadontha pang’onopang’ono, amatsitsimula, ndipo ndi ofunika kwambili pa moyo.