Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 2

Baibulo ni Buku Yocokela kwa Mulungu

Baibulo ni Buku Yocokela kwa Mulungu

1, 2. N’cifukwa ciani Baibulo ni mphatso yokondweletsa kwambili?

KODI mungamvele bwanji ngati mnzanu wakupatsani mphatso yabwino imene simunayembekezele? Mungakondwele kwambili ndi kumuyamikila. Ndipo mudzadziŵa kuti amakuganizilani.

2 Nayo Baibulo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Inde, Baibulo imatipatsa cidziwitso cimene sitingapeze kwina kulikonse. Mwacitsanzo, imatiuza kuti Mulungu analenga kumwamba, dziko lapansi, mwamuna woyamba ndi mkazi woyamba. Imatipatsa mfundo zotithandiza tikakumana ndi mavuto. Baibulo imatiphunzitsa kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake cokonza dziko lapansi kukhala malo abwino. Kukamba zoona, Baibulo ni mphatso yokondweletsa kwambili.

3. N’ciani cimene mudzaona pophunzila Baibulo?

3 Pamene muphunzila Baibulo, mudzaona kuti Mulungu afuna kuti inu mukhale bwenzi lake. Mukadziŵa zambili za iye, ubwenzi wanu ndi iye udzalimba kwambili.

4. N’ciani cimakufikani pa mtima ponena za Baibulo?

4 Baibulo ili m’zinenelo pafupifupi 2,600. Ndipo ma Baibulo amene apulinthiwa amafika m’mabiliyoni. Pa dziko lonse lapansi, anthu 90 pa anthu 100 alionse angaŵelenge Baibulo m’cinenelo cawo. Ndipo mlungu uliwonse, anthu opitilila wani miliyoni amalandila Baibulo. Zoona, palibe buku ingafanane ndi Baibulo.

5. N’cifukwa ninji timati Baibulo ‘inauzilidwa ndi Mulungu’?

5 Baibulo ni ‘youzilidwa ndi Mulungu.’ (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16.) Koma ena angaganize kuti, ‘Amene analemba Baibulo ni ŵanthu. Ndiye ingakhale bwanji yocokela kwa Mulungu?’ Pa funso limeneli, Baibulo imayankha kuti: “Anthu analankhula mau ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.” (2 Petulo 1:21) Tiyelekeze conco: Ambuye amakhala ndi mdzukulu wawo. Tsiku lina apempha mdzukuluyo kuti awalembele kalata ndi kuitumiza. Kodi tingakambe kuti mwini wake wa kalatayo n’ndani? Ni kalata ya ambuye, osati ya mdzukulu wawo. Mdzukulu anangokhala monga kalembela cabe. N’cimodzi-modzi ndi Mulungu. Iye ndiye mlembi weni-weni, kapena kuti mwini-wake wa Baibulo. Anthu amene anawagwilitsila nchito anali akalembela ake cabe. Mulungu ndiye anawatsogolela kuti alembe maganizo ake. Inde, Baibulo ni “mau a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13; onani Zakumapeto 2.

BAIBULO IMAKAMBA ZOONA

6, 7. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti nkhani zonse za m’Baibulo n’zogwilizana?

6 Kulemba Baibulo kunatenga zaka zopitilila 1,600. Ndipo olemba Baibulo anakhalako pa nthawi zosiyana-siyana. Ena anali ophunzila kwambili, koma ena anali osaphunzila. Mwacitsanzo, mlembi wina anali dokota, ena anali alimi, asodzi, aciŵeta, aneneli, mafumu, ndi oweluza. Olo kuti amene analemba Baibulo anali anthu osiyana-siyana, nkhani zake zonse n’zogwilizana kuyambila ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Baibulo siimanga ndi kumasula, mmene ena amakambila. *

7 Macaputala oyamba m’Baibulo amatiuza mmene mavuto anayambila pa dziko. Koma macaputala otsilizila amatiuza mmene Mulungu adzacotselapo mavuto onse, ndi kukonza dziko lapansi kukhala paradaiso. Mu Baibulo muli nkhani za mbili ya anthu yotenga zaka masauzande. Nkhanizo zimaonetsa kuti cifunilo ca Mulungu cimakwanilitsika nthawi zonse.

8. Pelekani zitsanzo zoonetsa kuti Baibulo imakamba zoona pa nkhani za sayansi.

8 Baibulo si buku yophunzitsa za sayansi, kapena za ku sukulu. Koma ikakambapo pa sayansi, nthawi zonse imakamba zoona. Ndipo n’zimene tingayembekezele ndi buku yocokela kwa Mulungu. Mwacitsanzo, buku ya Levitiko ili ndi malangizo a Mulungu amene Aisiraeli anali kutsatila kuti matenda asafalikile. Malangizo amenewo analembedwa kale kwambili anthu akalibe kudziŵa za tudoyo toyambitsa matenda. Baibulo imakambanso zoona kuti dziko lapansi lili m’malele. (Yobu 26:7) Cina, kumbuyoku anthu ambili anali kukhulupilila kuti dziko lapansi ni lafulati. Koma pa nthawi imeneyo, Baibulo inali itakamba kale kuti dziko lapansi ni lozungulila.—Yesaya 40:22.

9. Kodi kuona mtima kwa olemba Baibulo kumatitsimikizila ciani?

9 Ngakhale pa nkhani za mbili yakale, Baibulo imakamba zoona. Koma mabuku oculuka amene amafotokoza mbili yakale, alembi ake anali osaona mtima. Mwacitsanzo, ngati mtundu wawo wagonjetsedwa pa nkhondo, sanali kulemba zimenezo. Koma olemba Baibulo anali oona mtima, anali kulemba ngakhale pamene Aisiraeli agonjetsedwa. Anali kulembanso ngakhale zolakwa zawo. Mwacitsanzo, m’buku ya Numeri, Mose amatiuza colakwa cikulu cimene anacita, ndi kuti Mulungu anamulanga. (Numeri 20:2-12) Conco, kuona mtima kwa anthu amene analemba Baibulo ni umboni wina woonetsa kuti Baibulo inacokeladi kwa Mulungu. Pa cifukwa cimeneci, tiyenela kuikhulupilila.

BUKU YA MALANGIZO OTHANDIZA

10. N’cifukwa ninji malangizo a m’Baibulo ali othandiza lelo lino?

10 Baibulo ‘inauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ni yopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuongola zinthu.’ (2 Timoteyo 3:16) Zoona, malangizo a m’Baibulo ni othandiza kwambili masiku ano. Yehova amadziŵa cibadwa cathu cifukwa ndiye anatilenga. Amamvetsetsa mmene timaganizila ndi mmene timamvelela mumtima mwathu. Amatidziŵa bwino kupambana mmene ife eni ake timadzidziŵila, ndipo amafuna kuti tizikondwela ndi umoyo. Cinanso, iye amadziŵa zinthu zimene zingatithandize ndi zimene zingatipweteke.

11, 12. (a) Kodi Yesu anapeleka malangizo othandiza ati m’Mateyu caputala 5 mpaka 7? (b) Nanga n’ciani cina cimene tingaphunzile m’Baibulo?

11 M’buku ya Mateyu caputala 5 mpaka 7, timapezamo malangizo abwino amene Yesu anapeleka. Amakamba za mmene tingapezele cimwemwe, kumvana ndi anthu ena, kupemphela, ndi mmene tiyenela kuonela ndalama. Olo kuti malangizo amenewa anawapeleka zaka 2,000 zapitazo, akali othandizabe ngakhale masiku ano.

12 M’Baibulo, Yehova amatiphunzitsanso mfundo zimene zingatithandize kukhala ndi banja lacimwemwe, kukhala odalilika panchito, ndi kukhala mwa mtendele ndi anthu anzathu. Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwa anthu onse, zilibe kuti ndife ndani, kaya tikhala kuti, kapena tili ndi mavuto anji.—Ŵelengani Yesaya 48:17; onani Zakumapeto 3.

ULOSI WA M’BAIBULO NI WODALILIKA

Wolemba Baibulo, Yesaya, analosela kuti mzinda wa Babulo udzagonjetsedwa

13. Kodi Yesaya anati n’ciani cidzacitikila mzinda wa Babulo?

13 M’Baibulo muli maulosi osiyana-siyana. Ndipo ambili anakwanilitsika kale. Mwacitsanzo, Yesaya analosela kuti mzinda wa Babulo udzawonongedwa. (Yesaya 13:19) Mzindawo unali wocinjilizika kwambili. Unali ndi mpanda utali wa zipupa, mageti olimba, ndi mtsinje. Koma Yesaya anafotokoza mwatsatane-tsatane mmene adani adzaugonjetsela mzinda umenewo. Analosela kuti madzi adzauma mu mtsinje ndipo mageti adzasiyidwa otseguka. Iye anati adani adzagonjetsa mzindawo mosalimbana ndi aliyense. Anacita kuchula ngakhale dzina la munthu amene adzagonjetsa Babulo kuti ni Koresi.—Ŵelengani Yesaya 44:27–45:2; onani Zakumapeto 4.

14, 15. Kodi ulosi wa Yesaya unakwanilitsika bwanji?

14 Patapita zaka 200 kucokela pamene Yesaya analemba ulosi umenewu, panafika gulu la asilikali kuti awononge mzinda wa Babulo. Muganiza mtsogoleli wawo anali ndani? Monga mwa ulosi, anali Koresi, mfumu ya ku Perisiya. Zinthu zinali m’malo tsopano kuti mbali zonse zokhudza ulosi umenewo zikwanilitsike.

15 Usiku umene adani anazungulila mzinda, Ababulo anali paphwando. Mitima inali phee m’malo, ali ndi cidalilo conse kuti mzinda wawo unali wocinjilizika mokwana. Unali wochingika ndi mpanda utali wacipupa ndi mtsinje wozungulila. Koma kunja, Koresi ndi asilikali anali kukumba cimfolo copatutsila madzi kuti acepe mu mtsinjewo. Pamene madzi anapunguka kwambili, asilikali aku Perisiya aja anangoyenda ndi kuwoloka bwino-bwino. Nanga kodi cimpanda cacipupa citali-tali cija, anacigumula bwanji kuti aloŵe mkati mwa mzinda? Iyo siinali nkhani. Anangopeza kuti mageti ali citsegukile. Monga mwa mau a ulosi, asilikali aja analanda mzindawo popanda kumenya nkhondo.

16. (a) Kodi Yesaya analosela ciani za Babulo? (b) Nanga timadziŵa bwanji kuti ulosi wa Yesaya unakwanilitsikadi?

16 Yesaya analoselanso kuti mzinda wa Babulo ukadzawonongedwa, simudzakhalanso munthu. Iye anati: “M’Babulo simudzakhalanso anthu, ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo.” (Yesaya 13:20) Kodi mau amenewa anakwanilitsika? Ku dziko la Iraq n’kumene kunali mzinda wa Babulo. Ndipo malowo ali pa mtunda wa makilomita 80 kumwela kwa Baghdad. Koma malowo ni matongwe [bwinja] okha-okha mpaka lelo, sikukhala munthu aliyense. Yehova anapyanga mzinda wa Babulo ndi cipyango [tsace] ca ciwonongeko.—Yesaya 14:22, 23. *

Matongwe a mzinda wa Babulo

17. N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila malonjezo onse a Mulungu?

17 Taona kuti maulosi ambili a m’Baibulo anakwanilitsika. Izi zitipatsa cifukwa cokhulupilila kuti zimene Baibulo imakamba za tsogolo lathu, zidzakwanilitsika ndithu. Sitikaikila kuti Yehova adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso. (Ŵelengani Numeri 23:19.) Ndithudi, tili ndi ciyembekezo ca “moyo wosatha, cimene Mulungu amene sanganame analonjeza kalekale.”—Tito 1:2. *

BAIBULO IKHOZA KUSINTHA UMOYO WANU

18. Kodi Paulo anati ciani za “Mau a Mulungu”?

18 Taphunzila kale kuti palibe buku ina imene ingafanane ndi Baibulo, ndipo nkhani zake zonse n’zogwilizana. Pamene ikamba za sayansi kapena za mbili yakale, imakamba zoona. M’Baibulo mulinso malangizo opatsa nzelu ndi maulosi ambili amene anakwanilitsika kale. Si izi cabe. Mtumwi Paulo anati: ‘Mau a Mulungu ni amoyo ndi amphamvu.’ Kodi mau amenewa atanthauza ciani?—Ŵelengani Aheberi 4:12.

19, 20. (a) Kodi Baibulo ingakuthandizeni bwanji kudziŵa mtundu wa munthu amene muli? (b) Mungaonetse bwanji kuti mumayamikila mphatso ya Baibulo?

19 Mau amenewa atanthauza kuti Baibulo ili ndi mphamvu yosintha umoyo wanu. Ingakuthandizeni kumvetsetsa mtundu wa munthu amene inu muli. Ingakuthandizeninso kumvetsetsa maganizo anu ndi mtima wanu. Mwacitsanzo, tikhoza kukamba kuti timakonda Mulungu. Koma kuti zioneke kuti timamukonda zoona, tifunika kucita zimene timaphunzila m’Baibulo.

20 Kukamba zoona, Baibulo ni buku yocokela kwa Mulungu. Iye amafuna kuti muziiŵelenga, kuiphunzila ndi kuikonda. Onetsani kuti mumayamikila mphatso imeneyi, ndipo pitilizani kuiphunzila. Mwa kucita zimenezi, mudzadziŵa cifunilo ca Mulungu kwa anthu. M’nkhani yotsatila, tidzaphunzila za cifunilo ca Mulungu cimeneco.

^ ndime 6 Anthu ena amakamba kuti Baibulo imadzitsutsa, koma zimenezi si zoona. Onani mutu 7 m’buku yakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? yolembedwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Ngati mufuna kudziŵa zambili za maulosi a m’Baibulo, ŵelengani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse, pa masamba 27 mpaka 29, kolembedwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 17 Kuwonongedwa kwa mzinda wa Babulo, ni citsanzo cimodzi cabe ca maulosi ambili a m’Baibulo amene anakwanilitsika. Maulosi ena okamba za Yesu Khiristu mungawapeze pa Zakumapeto 5.