Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 5

Kudziŵa Zoona pa Nkhani ya Matsenga ndi Ufiti

Kudziŵa Zoona pa Nkhani ya Matsenga ndi Ufiti

1. Kodi ni anthu ambili bwanji amene amakhulupilila matsenga ndi ufiti?

“MU Africa, palibe cifukwa cofunsila ngati mfiti ziliko kapena kulibe,” limatelo buku lakuti African Traditional Religion, ndipo limaonjezela kuti “kwa anthu a mu Africa, nkhani ya ufiti ni nkhani yaikulu kwambili.” Pa anthu amene amakhulupilila za matsenga ndi za ufiti, pali anthu osaphunzila ndi ophunzila kwambili. Nao atsogoleli a Cisilamu ndi Cikristu amakhulupilila za ufiti.

2. Kodi anthu ambili amakhulupilila kuti mphamvu ya matsenga imacokela kuti?

2 Anthu ambili mu Africa ali ndi cikhulupililo cakuti pali mphamvu inayake yauzimu. Amati Mulungu ndi amene amailamulila. Mizimu ndi makolo angaigwilitsile nchito. Ndipo anthu ena amadziŵa mmene angapezele mphamvu imenei ndi kuiseŵenzetsa, kaya m’njila yabwino (kutsilika) kapena m’njila yoipa (kulodza).

3. Kodi anthu amakhulupilila ciani pankhani ya kulodza?

3 Anthu amakhulupilila kuti munthu amalodza anthu amene amazondana nao. Amakhulupilila kuti munthu amene amalodza ena ali ndi mphamvu yotumiza mileme, nyoni, nchenche, ndi nyama zina kuti zikawapweteke. Ambili amakhulupilila kuti matsenga amacititsa anthu kuyambana, amaletsa kubala, amabweletsa matenda, ngakhale imfa.

4. Kodi anthu ambili amakhulupilila ciani za mfiti, ndipo ena amene anali mfiti anaulula ciani?

4 Kulodza ndi kutsilika sikumasiyana ndi ufiti. Anthu amakhulupilila kuti mfiti zimasiya matupi ao usiku ndi kuuluka kupita kukakumana ndi mfiti zina kapena kukaononga anthu amene amazondana nao. Popeza kuti matupi a mfiti amatsala ali gone pabedi, umboni wotsimikizila zimenezi umapelekedwa maka-maka ndi anthu amene analeka ufiti. Mwacitsanzo, magazini ina ya mu Africa inalemba zimene anthu amene analeka ufiti (maka-maka atsikana) anakamba kuti: “Ine ndinapha anthu 150 mwa kucititsa ngozi za galimoto.” “Ine ndinapha ana 5 mwa kuyamwa (kunyonkha) magazi ao onse.” “Ine ndinapha zisumbali zanga zitatu cifukwa zinandikana.”

5. Kodi kutsilika ni kucita bwanji?

5 Anthu amati kutsilika kumachinjiliza munthu ku zoipa. Amene amakonda kutsilika amavala mphete (maling’i) kapena zibangili zamatsenga. Amamwa kapena kudzola mankhwala kuti awachinjilize. Amabisa m’nyumba kapena kukumbila pansi zinthu zimene amakhulupilila kuti zimatsilika nyumba. Amadalila zithumwa zimene analembapo mau a m’Koran kapena a m’Baibo.

Mabodza ndi Cinyengo

6. Kodi Satana ndi viŵanda vake anacita ciani kale, ndipo kodi tiyenela kuiona bwanji mphamvu yao?

6 N’zoona kuti Satana ndi viŵanda vake ni adani oopsa a anthu. Ali ndi mphamvu yosokoneza maganizo ndi umoyo wa anthu, ndipo kale anali kuloŵa ndi kukhala mwa anthu ndi nyama. (Mateyu 12:43-45) Ngakhale kuti sitiyenela kucepetsa mphamvu yao, sitiyenela kuikulitsa.

7. Kodi Satana amafuna kuti tizikhulupilila ciani, nanga ni citsanzo citi cimene cionetsa zimenezi?

7 Satana ndi katswili wa cinyengo. Amapusitsa anthu kuti aziganiza kuti iye ali ndi mphamvu zoposa zimene ali nazo. Mwacitsanzo: Osati kale kwambili kudziko lina mu Africa kunali nkhondo. Asilikali akumeneko anali kugwilitsila nchito zokuzila mau kuopseza adani ao. Akafuna kuukila adani ao, asilikalio anali kuliza matepu olila mabomba akulu-akulu ndi mfuti zikulu-zikulu. Colinga cao cinali cakuti adani ao akamva zimenezo, aganize kuti asilikali amene akumenyana nao ali ndi zida zamphamvu. Nayenso Satana amacita cimodzi-modzi. Iye amafuna kuti anthu aziona ngati kuti ali ndi mphamvu zambili kuposa zimene ali nazo. Colinga cake ndi kuopseza anthu kuti azicita cifunilo cake osati ca Yehova. Tiyeni tsopano tikambitsilane mabodza atatu amene Satana amafuna kuti anthu aziwakhulupilila.

8. Kodi bodza lina limene Satana amafalitsa ndi labwanji?

8 Bodza loyamba limene Satana amafalitsa ndi ili: kulibe tsoka limene limangocitika cabe; tsoka lililonse limene lacitika, limacitika cifukwa ca mphamvu ina yake yosadziŵika. Mwacitsanzo, tikambe kuti mwana wafa ndi maleliya. Amai ake angadziŵe kuti maleliya imabwela ndi udzudzu (mosikito). Koma angakhulupilile kuti munthu wina walodza mwana wao potumiza udzudzu kuti umulume.

Nthawi zina imangokhala tsoka cabe

9. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti si vuto lililonse limene Satana amacititsa?

9 Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu zocititsa mavuto ena, ndi kulakwa kukhulupilila kuti ali ndi mphamvu zocititsa vuto lina lililonse. Baibo imakamba kuti: “Anthu othamanga kwambili sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzelu sapeza cakudya, omvetsa zinthu naonso sapeza cuma, ndipo ngakhale odziŵa zinthu sakondedwa, cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onseo.” (Mlaliki 9:11) Pampikisano wothamanga, mmodzi angakhale waliwilo kwambili kuposa anzake, koma mwina sangapambane, kapena kuti kuwina, mpikisano. “Zinthu zosayembekezeleka” zingamucititse kuti asapambane. Mwina angagwe kapena kudwala kapenanso kudzipweteka mwendo. Zinthu zimenezi zingacitike kwa aliyense. Si Satana kapena mfiti imene imacititsa zimenezi; koma zimangocitika cabe.

10. Kodi anthu amakamba ciani za mfiti, nanga tidziŵa bwanji kuti zimenezi ni bodza?

10 Bodza laciŵili limene Satana amafalitsa ndi lakuti: Mfiti zimasiya matupi ao usiku ndi kupita kukakumana ndi mfiti zinzao kapena kukaononga anthu amene amazondana nao. Tsopano ganizilani izi: ‘Ngati mfiti zimacita zimenezi, ni ciani maka-maka cimene cimacoka kusiya thupi?’ Taona kale kuti palibe cimene cimacoka mwa munthu. Ndiponso mzimu ni mphamvu ya moyo imene imacititsa thupi kukhala lamoyo koma sungacite ciliconse palibe thupi.

N’zosatheka mfiti kucoka kusiya matupi awo

11. Timadziŵa bwanji kuti mfiti sizimasiya matupi ao, ndipo kodi inu mukuvomeleza zimenezi?

11 Mzimu sumacoka kusiya thupi kuti ukacite zina zake, zabwino kapena zoipa. Conco, mfiti sizimacoka kusiya matupi ao. Izo sizimacita ngakhale pang’ono zinthu zimene zimakamba kuti zimacita kapena zinthu zimene zimaganiza kuti zinacitapo.

12. Kodi Satana amacititsa bwanji anthu kukhulupilila kuti acita zinthu zimene sanacite?

12 Nanga tingakambe ciani pa zimene ena amene kale anali mfiti anaulula? Satana angacititse anthu kukhulupilila kuti anacitapo zinthu zimene io sanacite. Angagwilitsile nchito masomphenya kucititsa anthu kuganiza kuti aona zinthu zimene sanaone, kumva zinthu zimene sanamve, ndipo acita zinthu zimene sanacite. Mwa njila imenei, Satana amafuna kucotsa anthu kwa Yehova ndi kuwacititsa kuganiza kuti Baibo ni yabodza.

13. (a) Kodi kutsilika ni kwabwino? (b) Kodi Malemba amakamba ciani za matsenga?

13 Bodza lacitatu ndi lakuti: Kutsilika—kumene anthu amati kumachinjiliza munthu kuti asalodzedwe—ni kwabwino. Baibo simasiyanitsa kutsilika ndi kulodza. Imaletsa matsenga amtundu ulionse. Onani malamulo amene Yehova anapatsa mtundu wa Isiraeli otsutsa matsenga ndi anthu amene amacita zamatsenga:

  • “Musacite zamatsenga.”—Levitiko 19:26.

  • “Mwamuna kapena mkazi amene amalankhula ndi mizimu kapena amene amalosela zam’tsogolo aziphedwa ndithu.”—Levitiko 20:27.

  • “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wocita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsila kwa wolankhula ndi mizimu.”—Deuteronomo 18:10-14.

14. N’cifukwa ciani Yehova anapeleka malamulo oletsa matsenga?

14 Malamulo amenewa anafotokoza momveka bwino kuti Mulungu safuna anthu ake kucita matsenga. Yehova anapatsa anthu ake malamulo amenewa cifukwa cakuti anali kuwakonda ndipo sanafune kuti azikhala ndi mantha kapena kuti akhale akapolo a zikhulupililo zabodza. Iye sanafune kuti viŵanda viziwavutitsa.

15. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti Yehova ni wamphamvu kwambili kuposa Satana?

15 Ngakhale kuti Baibo simafotokoza zonse zimene viŵanda vingacite ndi zimene sivingacite, imaonetsa kuti Yehova Mulungu ni wamphamvu kwambili kuposa Satana ndi viŵanda vake. Yehova ndiye analamula kuti Satana athamangitsidwe kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Ndipo onani kuti Satana anacita kupempha kuti ayese Yobu ndipo anamvela pamene Mulungu anamucenjeza kuti asaphe Yobu.—Yobu 2:4-6.

16. Kodi tiyenela kuyang’ana kwa ndani kuti atichinjilize?

16 Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawila mmenemo ndipo amatetezedwa.” Conco ngati tifuna kuchinjilizidwa, tiyenela kuyang’ana kwa Yehova. Anthu a Mulungu sadalila zithumwa kapena mankhwala kuti awachinjilize ku zoipa zimene Satana ndi viŵanda vake amacita, ndipo saopa zamatsenga. Anthu a Mulungu amakhulupilila zimene Baibo imakamba kuti: “Maso a Yehova akuyenda-yenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.”—2 Mbiri 16:9.

17. Kodi lemba la Yakobo 4:7 likutilonjeza ciani, koma tiyenela kucita ciani?

17 Inunso mungakhale ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzakuchinjilizani ngati mumutumikila. Lemba la Yakobo 4:7 limakamba kuti: “Gonjelani Mulungu, koma tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthawani.” Ngati mutumikila Mulungu woona, ndi kumugonjela, dziŵani kuti Yehova adzakuchinjilizani.