Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 12

Mungacite Ciani Kuti Banja Likhale Lokondweletsa?

Mungacite Ciani Kuti Banja Likhale Lokondweletsa?

Cikondi cimafunika kuti mabanja akhale acimwemwe. Aefeso 5:33

Lamulo la Mulungu ndi lakuti cikwati ni ca mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi.

Mwamuna wacikondi amacitila cifundo mkazi wake ndipo amamumvetsetsa.

Mkazi ayenela kugwilizana ndi mwamuna wake.

Ana ayenela kumvela makolo ao.

Khalani okoma mtima ndi okhulupilika, osati ankhanza ndi osakhulupilika. Akolose 3:​5, 8-10

Mau a Mulungu amakamba kuti mwamuna ayenela kukonda mkazi wake monga thupi lake ndi kuti mkazi ayenela kulemekeza kwambili mwamuna wake.

Kugonana ndi munthu amene simunakwatilane naye ni kulakwa. Kukwatila cipali nako ni kulakwa.

Mau a Yehova amaphunzitsa mabanja mmene angakhalile okondwela.