Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu

Mu Baibo muli mfundo komanso miyezo ya makhalidwe abwino, zimene zingatithandize kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova likulimbikitsa onse okonda Yehova Mulungu, kudziŵa mokhalila na umoyo wogwilizana na coonadi ca m’Mawu ake, Baibo.

MUTU 1

Cikondi ca Mulungu N’camuyaya

Pamafunika khama kuti ubwenzi wathu na Mulungu ukhalebe wolimba. Nanga tingacite bwanji zimenezo?

MUTU 2

Khalani na Cikumbumtima Cabwino kwa Mulungu

Mulungu anapatsa munthu aliyense cikumbumtima kuti cizim’tsogolela mu umoyo wake.

MUTU 3

Sankhani Mabwenzi Okonda Mulungu

Mabwenzi akhoza kutithandiza kukhala na makhalidwe abwino, kapena akhoza kutiwononga. Kodi mfundo za m’Baibo zingatithandize bwanji posankha mabwenzi?

MUTU 4

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?

Tili na cifukwa comveka colemekezela ulamulilo m’banja, mu mpingo, na m’dela limene tikhala.

MUTU 5

Kukhala Olekana Nalo Dziko

Yesu anauza ophunzila ake kuti, “Simuli mbali ya dzikoli.” Kodi “dziko” limeneli n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani Akhristu afunika kulekana nalo?

MUTU 6

Mmene Tingasankhile Zosangalatsa

Zosangalatsa m’dzikoli zili monga cipatso cimene mbali yake ina ni yabwino, koma ina ni yoola. N’ciani cingakuthandizeni kusankha zosangalatsa zabwino, na kupewa zoipa?

MUTU 7

Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela

Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zimatithandiza kupanga zosankha zabwino pa nkhani ya moyo na magazi?

MUTU 8

Yehova Amafuna Anthu Ake Kukhala Oyela

Miyezo ya Mulungu ya ciyelo simangofuna cabe kuti matupi athu, zovala zathu, komanso nyumba yathu, zikhale zoyela. Imafunanso kuti kalambilidwe kathu, khalidwe, na maganizo athu, zikhale zoyela.

MUTU 9

“Thaŵani Dama”

Kodi dama n’ciani? Nanga tingalithaŵe bwanji?

MUTU 10

Cikwati Ni Mphatso Yocokela Kwa Mulungu

Kodi m’cikwati muli mapindu anji? Mungasankhe bwanji womanga naye banja? N’ciani cingathandize kuti banja likhalitse?

MUTU 11

Pambuyo pa Tsiku la Cikwati

Cikwati ciliconse cili na mapindu komanso mavuto ake. Ngakhale n’conco, anthu amene ali na mavuto aakulu m’banja lawo, angathe kulimbitsa cikwati cawo.

MUTU 12

Muzikamba Mawu Olimbikitsa

Mawu akhoza kulimbikitsa ena koma kuwavulaza kwambili. Yehova amatiphunzitsa mmene tingaseŵenzetsele bwino mphatso imeneyi.

MUTU 13

Kodi Zikondwelelo Zonse Zimakondweletsa Mulungu?

Anthu ambili amaona kuti zikondwelelo na maholide n’zofunika kwambili mu umoyo wawo. N’ciani cingatithandize kudziŵa mmene Yehova amazionela?

MUTU 14

Khalani Oona Mtima M’zinthu Zonse

Onani mbali zinayi m’zimene kuona mtima kungakhale kovutilapo, komanso mapindu amene timapeza tikakhalabe oona mtima.

MUTU 15

Muzikondwela Nayo Nchito Yanu

Mlengi wathu amafuna kuti tizikondwela na zimene timacita. N’ciani cingatithandize kuti tikondwela nayo nchito yathu? Kodi pali nchito zina zimene Akhristu afunika kupewa?

MUTU 16

Mutsutseni Mdyelekezi

Tikukhala m’dziko loyendetsedwa na Satana. Kodi tingakhale bwanji pafupi na Mulungu, kuti atiteteze kwa mdani wake?

MUTU 17

Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu

wolemba Baibo wina analimbikitsa Akhristu kuti: “Dzilimbitseni pa cikhulupililo canu coyela kopambana.” Kodi mungacite bwanji zimenezi?

Zakumapeto

Matanthauzo a mawu ena a m’buku yakuti, ‘Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu.’