Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Wokondedwa Mkristu mnzathu:

Monga mmene mukudziŵila, Baibulo limasimba za anthu. Ambili anali amuna ndi akazi okhulupilika amene anakumanapo ndi mavuto ngati amene timakumana nao. Iwo anali anthu “monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Ena anafookapo cifukwa ca mavuto ndi nkhawa, komanso ena anakhumudwapo ndi zimene acibale ao kapena okhulupilila anzao anawacitila. Ndipo ambili anali kudziimba mlandu cifukwa ca zolakwa zao.

Kodi anthu amenewo analekelatu kutumikila Yehova? Iyai. Ambili maganizo ao anali ngati a wamasalimo, amene anapemphela kuti: “Ndayendayenda ngati nkhosa yosocela. Ndifunefuneni ine mtumiki wanu, pakuti sindinaiŵale malamulo anu.” (Salimo 119:176) Kodi inunso mumamva conco?

Yehova saiŵala alambili ake amene anacoka m’khola lake ndi kusocela. M’malo mwake, iye nthawi zambili amawathandiza, ndipo amagwilitsila nchito Akristu anzao. Mwacitsanzo, Yehova anathandiza mtumiki wake Yobu amene anakumana ndi mavuto a za cuma, kutaikilidwa okondedwa ake, ndi matenda aakulu. Ndiponso anthu amene Yobu anayembekezela kuti am’limbikitse anam’lankhula mau opweteka. Komabe, iye sanaleke kutumikila Yehova ngakhale kuti penapake anali ndi maganizo olakwika. (Yobu 1:22; 2:10) Kodi Yehova anacita ciani kuti athandize Yobu kukhalanso wolimba?

Yehova anagwilitsila nchito Elihu, munthu woopa Mulungu, kuthandiza Yobu. Elihu anali kumvetsela pamene Yobu anali kufotokoza maganizo ake, kenako nayenso analankhulapo. Kodi Elihu anakamba ciani? Kodi anadzudzula Yobu mwa kumuimba mlandu kapena kum’cititsa manyazi? Kodi Elihu anadziona kukhala wolungama kuposa Yobu? Kutalitali! Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Elihu anati: “Kwa Mulungu woona, ine ndili ngati inu nomwe. Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.” Ndiyeno iye anatsimikizila Yobu kuti: “Mwa ine mulibe cinthu coti muope, ndipo mau anga sakulemetsani.” (Yobu 33:6, 7) Elihu sanaonjezele mavuto a Yobu iyai, m’malo mwake anapeleka uphungu ndi cilimbikitso cimene Yobu anafunika mwacikondi.

Ici ndico colinga ca kabuku kano. Coyamba, ife tinapenda bwinobwino zimene zinacitikila anthu omwe anasocela ndi kumvetsela bwinobwino maganizo ao. (Miyambo 18:13) Ndiyeno, tinapemphelela nkhani imeneyi ndi kufufuza Malemba kuti tione mmene Yehova anathandizila atumiki ake akale omwe anakumana ndi mavuto ngati amenewa. Pomalizila pake, tinatenga nkhani za m’Malemba zimenezo ndi kuzigwilizanitsa ndi zitsanzo za makono kuti tipange kabuku aka. Conco, tikukupemphani kuti mukaŵelenge bwinobwino. Ife timakukondani kwambili. Tsalani bwino.

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova