Onani zimene zilipo

N’cifukwa ciani atsikana samanifuna?

N’cifukwa ciani atsikana samanifuna?

MUTU 28

N’cifukwa ciani atsikana samanifuna?

Zimene nikumuuzazi zicititsa kuti afe nane mutu. Namuuza zonse, katundu amene nili naye, malo amene nayenda ndiponso anthu amene nimadziŵana nawo. Sinikukayika kuti akucita kuona kucedwa kuti nimufunsile.

Zimene akucitazi zikunikhumudwitsa. Nayesa kumuuza mwaulemu kuti sinikumufuna koma sakumva. Ndiye nimuuze bwanji mwamphamvu koma moti asakhumudwe?

TIYELEKEZE kuti ndimwe wamkulu ndithu moti mukhoza kukhala na cibwenzi. Mukulakalaka mutapeza mtsikana wooneka bwino ndiponso wofanana naye cikhulupililo. (1 Akorinto 7:39) Koma m’mbuyomu mwayesapo kuti mupeze cibwenzi koma mumangowomba khoma. Kodi vuto ni ciani? Kapena atsikana amangofuna anyamata ooneka bwino okha? Mtsikana wina, dzina lake Lisa, ananena kuti: “Nimakonda anyamata okhala ni masozi.” Komabe atsikana ambili samangokopeka ni maonekedwe. Carrie wazaka 18, ananena kuti: “Nthawi zambili anyamata ooneka bwino samakhala akhalidwe.”

Kodi atsikana amafuna “anyamata akhalidwe lotani”? Ngati mukufuna kufunsila mtsikana winawake kodi muyenela kuganizila zinthu ziti? Nanga ni mfundo ziti za m’Baibo zimene muyenela kuzikumbukila?

Zoyenela Kucita Musanayambe Cibwenzi

Musanaganize zofufuza mtsikana, pali zinthu zingapo zofunika zimene muyenela kucita ndipo zingakuthandizeni kuti muzigwilizana ni aliyense. Tiyeni tikambilane zinthu zimenezi.

Yesetsani kukhala na makhalidwe abwino. Baibo imanena kuti cikondi “sicicita zosayenela.” (1 Akorinto 13:5) Khalidwe labwino limasonyeza kuti mumalemekeza anthu ena ndiponso kuti mukukula mwauzimu ndipo mwayamba kutengela makhalidwe a Khristu. Komabe makhalidwe abwino sali ngati suti imene umangovala kuti anthu ena akuone kenako n’kukaivula ukafika kunyumba. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimasonyeza makhalidwe abwino n’kamacita zinthu na abale anga?’ Ngati simusonyeza khalidwe labwino kwa abale anu zingakhale zovuta kuti muzisonyeza khalidwe labwino pocita zinthu na anthu ena. Kumbukilani kuti mtsikana wozindikila adzafuna kuona mmene inuyo mumacitila zinthu na abale anu kuti adziŵe kuti ndimwe munthu wotani.—Aefeso 6:1, 2.

Zimene atsikana amanena: “N’makopeka na mnyamata amene amasonyeza khalidwe labwino ponicitila zinthu zing’ono-zing’ono ngati kunitsegulila citseko ndiponso zinthu zikulu-zikulu ngati kucita zinthu moniganizila komanso moganizila abale anga.”—Anatelo Tina.

“Sinisangalala ngati munthu amene nangokumana naye koyamba akunifunsa zinthu zimene munthu sungamasuke kumangouza aliyense ngati zoti ‘Kodi uli na cibwenzi?’ ndiponso ‘Kodi uli na zolinga zotani?’ N’maona kuti si ulemu, moti nimamangika kwambili munthu akamanifunsa zimenezi.”—Anatelo Kathy.

“N’imaona kuti si ulemu anyamata akamaganiza kuti akhoza kumangotiseweletsa maganizo pomacita zinthu ngati atifunsila, koma ayi. Amakhala ngati sasamala za mmene tikumvela mumtima komanso amaona ngati tonse timangoganizila za banja basi, moti timafuna kuti azitimvela cisoni.”—Anatelo Alexis.

Muzikhala aukhondo nthawi zonse. Kukhala waukhondo kumasonyeza kuti mumalemekeza anthu ena komanso mumalemekeza thupi lanu. (Mateyu 7:12) Ngati mumadzilemekeza nokha n’zosavuta kuti anthu enanso azikulemekezani. Koma ngati mulibe ukhondo, olo mutayesetsa bwanji n’zovuta kuti mtsikana akopeke nanu.

Zimene atsikana amanena: “Mnyamata wina amene anali kunifuna anali kununkha mkamwa. Fungo lake linali lamphamvu kwambili moti zinali zosatheka kulipilila.”—Anatelo Kelly.

Muzidziŵa kucezetsa. Kulankhulana bwino n’kumene kumathandiza kuti cibwenzi kapena banja likhale lolimba. Muyenela kukambilana zomwe inuyo mumakonda komanso zimene mnzanuyo amakonda. (Afilipi 2:3, 4) Muyenela kumvetsela pamene iyeyo akulankhula ndiponso muzilemekeza maganizo ake.

Zimene atsikana amanena: “N’masangalala mnyamata akamaceza nane momasuka. Ayenela kumakumbukila zinthu zimene n’namuuza komanso azifunsa mafunso amene angathandize kuti tizipitiliza kuceza.”—Anatelo Christine.

“N’maganiza kuti anyamata amakopeka na zimene amaona pamene atsikana amakopeka na zimene amamva.”—Anatelo Laura.

“Mnyamata akamakupatsa mphatso zimakhala bwino koma mnyamata yemwe ukhoza kukopeka naye mosavuta ni amene amadziŵa kucezetsa komanso amakuuza mawu olimbikitsa.”—Anatelo Amy.

“N’ikudziŵa mnyamata winawake yemwe ni waulemu komanso samakumasukila kwambili. Timatha kuceza nkhani zabwino-bwino iyeyo osakuuza zinthu ngati zoti, ‘Komatu ndiye ukununkhila bwino’ kapena ‘Lelo ndiye wachenatu.’ Amamvetsela mwacidwi nikamalankhula ndipo n’kukhulupilila kuti mtsikana aliyense angasangalale kuceza na munthu wotele.”—Anatelo Beth.

“N’khoza kulola kukhala pa cibwenzi na munthu amene amakambako tinthabwala koma osati nthawi zonse. Pena muzikambilanako zinthu za phindu koma asamakambe nkhani zimenezi mongofuna kuti akukope.”—Anatelo Kelly.

Muzisonyeza kuti ndimwe woganiza bwino. Baibo imati: “Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.” (Agalatiya 6:5) Palibe mtsikana amene angakopeke na mnyamata yemwe sacedwa kucotsedwa nchito cifukwa coti ni waulesi kapena cifukwa cakuti amangokhalila kuceza.

Zimene atsikana amanena: “Kuli bwino kuti anyamata azicita zinthu mozindikila cifukwa akapanda kutelo atsikana sangawafune.”—Anatelo Carrie.

“Anyamata ena alibe zolinga zenizeni. Akamamufuna mtsikana winawake amamufunsa zolinga zake kenako amvekele, ‘Tafanana, na zimene nanenso nikufuna n’dzacite.’ Koma zimene amacita sizigwilizana na zonena zawo.”—Anatelo Beth.

Zitsanzo zimene zili pamwambazi zikusonyeza kuti kukhala munthu wodalilika komanso woganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzigwilizana na ena. Koma kodi mungacite ciani ngati mukuona kuti ndimwe wokonzeka kuyamba cibwenzi na mtsikana winawake?

Zinthu Zina Zimene Muyenela Kucita

Muuzeni maganizo anu. Ngati mukuona kuti mtsikana amene mumaceza naye angakhale mkazi wabwino, muuzeni kuti mukumufuna. Fotokozani maganizo anu momveka bwino komanso mosazungulila. Ni zoona kuti zimenezi sizopepuka cifukwa mungamaope kuti akukanani. Koma kulimba kwanu mtima kufotokoza maganizo anu ni umboni wakuti mwakula. Komabe dziŵani kuti mukufunsila cibwenzi osati banja. Conco, muzicita zinthu mwanzelu. Kulankhula mwaulemu kwambili kapena momangika kukhoza kucititsa mtsikanayo kukuopani m’malo moti akopeke nanu.

Zimene atsikana amanena: “Siningadziŵe zimene munthu akuganiza ndiye ngati mnyamata akunifuna, kulibwino angoniuza bwino-bwino.”—Anatelo Nina.

“N’zovuta kuti musinthe n’kuyamba kuonana ngati cibwenzi maka-maka ngati mwakhala mukungoceza kwa nthawi yaitali. Komabe ningakonde ngati mnyamatayo atangoniuza maganizo ake.”—Anatelo Helen.

Muzilemekeza maganizo a mtsikanayo. Kodi mungacite ciani ngati mtsikana yemwe mumaceza naye atakana zoti mukhale naye pa cibwenzi? Mungasonyeze kuti mumamulemekeza ngati mutakhulupilila kuti iyeyo akudziŵa zimene zili mumtima mwake ndipo ayi wake akutanthauzadi ayi. Mungasonyeze kuti ndimwe munthu wacibwana ngati mutakakamilabe kuti akuloleni. Ndipo ngati mutanyalanyaza zimene iye wanena momveka bwino kuti sakukufunani, mwinanso mpaka kumukwiyila cifukwa cakuti wakukanani, kodi zingasonyeze kuti mumamuganiziladi kapena mumangoganizila zofuna zanu?—1 Akorinto 13:11.

Zimene atsikana amanena: “Zimanikhumudwitsa kwambili n’kamukana mnyamata momveka bwino koma iyeyo n’kumakakamilabe.”—Anatelo Colleen.

“Mnyamata wina n’tamukana anali kukakamilabe kuti nim’patse nambala yanga ya foni. N’nali kufuna kumuyankha mwaulemu pozindikila kuti anasonyeza kulimba mtima kuti akwanitse kuniuza maganizo ake. Koma kenako n’naona kuti nikufunika kumuuza mwamphamvu kuti anisiye.”—Anatelo Sarah.

Zimene Simuyenela Kucita

Anyamata ena amaona ngati sizingawavute kufunsila mtsikana kapena kumukopa kuti ayambe kuwafuna. Ndipo nthawi zina amapikisana na anzawo kuti aone munthu amene akhoza kukopa atsikana ambili. Komatu mpikisano wotelo si wabwino ndipo ungakuipitsileni mbili. (Miyambo 20:11) Mukhoza kupewa zimenezi ngati mutatsatila mfundo zotsatilazi.

Musamakope atsikana. Munthu amene amakopa anzake amalankhula zinthu zacinyengo komanso amagwilitsa nchito thupi lake m’njila yoti akope anthu ena. Munthu wotele sakhala na colinga cokhala pa cibwenzi colongosoka. Kucita zimenezi kumakhala kunyalanyaza mfundo ya m’Baibo yakuti tiziona ‘akazi acitsikana . . . ngati alongo athu, ndipo pocita zimenezi tisakhale ndi maganizo alionse oipa.’ (1 Timoteyo 5:2) Munthu amene amakopa ena samakhala na anzake odalilika komanso banja lake silimayenda bwino. Atsikana anzelu amadziŵa zimenezi.

Zimene atsikana amanena: “N’kukhulupilila kuti palibe mtsikana amene angakopeke na mnyamata yemwe wamuuza mawu okopa koma n’kudziŵa kuti mnyamatayo ananenanso zomwezo kwa mtsikana wina mwezi watha.”—Anatelo Helen.

“Pali mnyamata wina wooneka bwino yemwe anayamba kuniuza mawu okopa ndipo nthawi zambili anali kungodzicemelela. Koma kenako pamene tinalipo panabwelanso mtsikana wina ndipo iye anayambanso kunena zomwe zija kwa mtsikanayo. Kenako panabwelanso mtsikana wina ndipo anacitanso cimodzi-modzi. Zimenezi sizinanisangalatse ngakhale pang’ono.”—Anatelo Tina.

Musamangopusitsa atsikana. Musamaganize kuti mmene mumacezela na anyamata n’cimodzi-modzi na mmene mungacezela na mtsikana. N’cifukwa ciani tikutelo? Taganizilani izi: Ngati mutamuuza mnyamata mnzanu kuti akuoneka bwino na suti yatsopano imene wagula kapena ngati mumamuuza zakukhosi kwanu kaŵili-kaŵili sangaganize kuti mukumufuna. Koma ngati mutayamikila mtsikana cifukwa ca mmene akuonekela kapena ngati kaŵili-kaŵili mumamuuza zakukhosi kwanu, akhoza kuyamba kuganiza kuti mukumufuna.

Zimene atsikana amanena: “N’kukayikila ngati anyamata amadziŵa zoti sangaceze na mtsikana mofanana na mmene amacezela na anyamata anzawo.”—Anatelo Sheryl.

“Nthawi zina mnyamata akhoza kupeza nambala yanga kenako n’kunitumizila meseji. Munthu umayamba kudzifunsa kuti colinga cake ni ciani. Nthawi zina anthu amatha kuyamba kuceza kwambili cifukwa ca mameseji omwe amatumizilana n’kuyamba kufunana, koma kodi munthu anganene zambili bwanji pa foni?”—Anatelo Mallory.

“Anyamata ambili sadziŵa kuti mtsikana sacedwa kukopeka maka-maka ngati mnyamatayo akuoneka kuti amawaganizila komanso ni wocezeka. Si kuti mtsikanayo amakhala kuti watopa na umbeta. Nikuganiza kuti atsikana ambili amacita zimenezi cifukwa amafuna atakhala na cibwenzi ndipo nthawi zonse amakhala akusaka-saka mwamuna woyenelela.”—Anatelo Alison.

KUTI MUMVE ZAMBILI ŴELENGANI MUTU 3, M’BUKU LACIŴILI

M’MUTU WOTSATILA

Kodi cikondi ceniceni mungacidziŵe bwanji?

LEMBA LOFUNIKILA

‘Valani umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.’—Aefeso 4:24.

MFUNDO YOTHANDIZA

Funsani munthu wina wacikulile kuti akuuzeni khalidwe lofunika kwambili limene mnyamata ayenela kukhala nalo. Kenako onani ngati inuyo mukufunika kuyesetsa kukonza mbali imeneyi.

KODI MUKUDZIŴA . . .

Kukhala na makhalidwe abwino n’kofunika kwambili kuposa maonekedwe

ZOTI NICITE

N’kufunika kukhala waulemu pocita zinthu izi ․․․․․․

Kuti niziceza bwino na anthu ena n’zicita izi ․․․․․

Zimene nikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumadzilemekeza?

● Kodi mukamaceza na mtsikana mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza maganizo ake komanso mmene akumvela?

[Mau okopa]

Anyamata amaganiza kuti atsikana angakopeke nawo ngati amavala mwanjila inayake kapena ngati ali ooneka bwino. Ngakhale kuti atsikana ena akhoza kukopekadi na zimenezi, atsikana ambili amakopeka na mnyamata amene ali na makhalidwe abwino.’’—Anatelo Kate

[Cithunzi]

Makhalidwe abwino sali ngati suti imene umangovala kuti anthu ena akugomele kenako n’kukaivula ukafika kunyumba