Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ansembe akuloŵa pa Mtsinje wa Yorodano atanyamula Likasa

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Amatidalitsa Ngati Ticita Zinthu Zoonetsa Cikhulupililo

Yehova Amatidalitsa Ngati Ticita Zinthu Zoonetsa Cikhulupililo

Nthawi zina, malangizo a Yehova angaoneke osathandiza malinga n’kuona kwa anthu (Yos. 3:12, 13; it-2 105; onani cithunzi pacikuto)

Amuna a paudindo ayenela kukhala citsanzo cabwino pa nkhani yotsatila malangizo. (Yos. 3:14; w13 9/1 16 ¶17)

Yehova amadalitsa anthu amene amacita zinthu mosazengeleza (Yos. 3:15-17; w13 9/1 16 ¶18)

Timapatsa Yehova mpata woti atidalitse ngati timayesetsa kupeza njila yolalikilila, ngakhale kuti tili na thanzi lofooka kapena pali zovuta zina.