Alalikila mayi ndi mwana wake ku West Bengal m’dziko la India

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO September 2016

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a citsanzo osewenzetsa pogaŵila Nsanja ya Mlonda ndi pofotokozela anthu Mfundo ya coonadi ca m’Baibulo yoonetsa kuti Mulungu amatidela nkhawa. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo amenewa pokonza ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

“Muzitsatila Cilamulo ca Yehova”

Kodi kutsatila cilamulo ca Yehova kutanthauza ciani? Wolemba Salimo 119 ndi citsanzo cabwino kwa ife masiku ano.

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Mukapeza Mwana Panyumba

Zimene tingacite kuti tionetse kuti timalemekeza makolo ake.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

“Thandizo Langa Licokela kwa Yehova”

Mu Salimo 121 muli zitsanzo zoonetsa mmene Yehova amatitetezela.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Tinapangidwa Modabwitsa

Mu Salimo 139, Davide anatamanda Yehova cifukwa ca zinthu zodabwitsa zimene analenga.

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo

Kuti tifike pamtima wophunzila wathu, n’ciani cimene tifunika kupewa?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

“Yehova Ndi Wamkulu ndi Woyenela Kutamandidwa Kwambili”

Salimo 145 ionetsa mmene Davide anamvelela ponena za mmene Yehova amasamalila atumiki ake okhulupilika.

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Limbikitsani Anthu Acidwi Kupezeka pa Misonkhano

Nthawi zambili, anthu acidwi na ophunzila baibulo amapita patsogolo kwambili akayamba kupezeka pa misonkhano.