UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Amateteza Anthu Ake

Yehova Amateteza Anthu Ake

Mwambo woyamba wa Pasika unali cocitika cofunika kwambili. Tsiku lina usiku, pambuyo pakuti Farao waona kuti mwana wake woyamba kubadwa waphedwa, anauza Mose kuti: “Nyamukani, cokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi ana onse a Isiraeli. Pitani, katumikileni Yehova, monga momwe mwanenela.” (Eks. 12:31) Yehova anaonetsa kuti amateteza anthu ake.

Tikaona mbili yamakono ya anthu a Yehova, n’zoonekelatu kuti Yehova wapitiliza kuwatsogolela na kuwateteza. Izi zionekela bwino mu miziyamu yathu yochedwa “Anthu Odziŵika na Dzina la Yehova,” imene ili ku likulu lathu la padziko lonse.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KUYENDELA MIZIYAMU YA KU WARWICK: “ANTHU ODZIŴIKA NA DZINA LA YEHOVA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSALIWA:

  • Kodi ni zida ziti zimene Ophunzila Baibo anayamba kuseŵenzetsa mu 1914, polimbikitsa cikhulupililo cawo pa Baibo? Nanga panali zotulukapo zotani?

  • Kodi ni zopinga zotani zimene anakumana nazo mu 1916 komanso mu 1918? Nanga panali umboni wotani woonetsa kuti Yehova anali kutsogolela gulu lake?

  • Kodi anthu a Yehova amacilimika bwanji pa cikhulupililo cawo pamene anthu ena awatsutsa?

  • Kodi ni kamvedwe katsopano kati kamene anthu a Yehova analandila mu 1935? Nanga zimenezi zinawakhudza bwanji?

  • Ngati munayendako kukaona miziyamu imeneyi, kodi n’ciani cimene munaona cimene cinalimbitsa cikhulupililo canu cakuti Yehova amatsogolela na kuteteza anthu ake?