July 13-19
EKSODO 8-9
Nyimbo 12 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Farao Wonyadayo Mosadziŵa Anathandiza kuti Cifunilo ca Mulungu Cikwanilitsidwe”: (10 min.)
Eks. 8:15—Farao anaumitsa mtima wake ndipo anakana kumvela Mose na Aroni (it-2 1040-1041)
Eks. 8:18, 19—Farao anapitilizabe kukana olo kuti ansembe ake ocita zamatsenga anavomeleza kugonjetsedwa kwawo
Eks. 9:15-17—Yehova anakweza dzina lake posungabe Farao na moyo (it-2 1181 ¶3-5)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 8:21—Kodi tuzilombo touluka toyamwa magazi tunali ciani? (it-1 878)
Eks. 8:25-27—N’cifukwa ciani Mose anakamba kuti nsembe za Aisiraeli zikanakhala “conyansa kwa Aiguputo”? (w04 3/15 25 ¶9)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 8:1-19 (th phunzilo 12)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani mafunso aya: Kodi wofalitsa wacita motani pamene mwininyumba wakana kulalikidwa? Kodi wofalitsa akanacita ciani kuti agaŵile cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu?
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 6)
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. (th phunzilo 3)
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo, ndiyeno gaŵilani cofalitsa cophunzitsila Baibo. (th phunzilo 12)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Khalani Wodzicepetsa—Pewani Kudzitamandila”: (7 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Khala Wodzicepetsa. Pambuyo pake, itanilani acicepele ngati alipo, amene munasankhilatu kuti abwele ku pulatifomu, ndiyeno afunseni mafunso pa vidiyo imeneyi.
“Khalani Wodzicepetsa Ena Akakutamandani”: (8 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khalani Okhulupilika Monga Yesu—Mukatamandidwa.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 123, na bokosi lakuti “Thukuta la Yesu Linaoneka Ngati Madontho a Magazi.”.
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 44 na Pemphelo