Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 21-22

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

“Cifunilo ca Yehova Cicitike”

21:8-14

Paulo anamva kuti mzimu woyela ukumutsogolela kupita ku Yerusalemu kumene anakumana na masautso. (Mac. 20:22, 23) Conco, pamene Akhristu a kumeneko anayamba kumucondelela kuti asapite, iye anayankha kuti: “N’cifukwa ciani mukulila ndi kunditayitsa mtima?” (Mac. 21:13) Sitifunika kufooketsa ena amene akuyesetsa kudzipeleka na mtima wonse potumikila Yehova.