CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | 2 MBIRI 33–36

Yehova Amaona Munthu Wolapa ndi Mtima Wonse Kukhala Wamtengo Wapatali

Yehova Amaona Munthu Wolapa ndi Mtima Wonse Kukhala Wamtengo Wapatali

MANASE

Yehova analola kuti agwidwe ndi Asuri ndipo anapita naye ku Babulo m’matangadza

ULAMULILO WAKE ASANATENGEDWE KU UKAPOLO

  • Anamangila milungu yonama maguwa ansembe

  • Anapeleka ana ake nsembe

  • Anakhetsa magazi a anthu osalakwa

  • Analimbikitsa anthu onse kucita zamatsenga

ULAMULILO WAKE ATAMASULIDWA

  • Anadzicepetsa kwambili

  • Anapemphela kwa Yehova; ndipo anapeleka nsembe

  • Anacotsa maguwa a nsembe a milungu yonama

  • Analimbikitsa anthu onse kutumikila Yehova

YOSIYA

ULAMULILO WAKE WONSE

  • Anafunafuna Yehova

  • Anayeletsa Yuda ndi Yerusalemu

  • Anakonza nyumba ya Yehova; anapeza buku la Cilamulo ca Yehova