KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Mmene Tingatsogozele Phunzilo m’Kabuku ka Uthenga Wabwino
-
Ŵelengani funso lili m’zilembo zakuda lokhala ndi nambala kuti muthandize mwininyumba kumvetsa mfundo yaikulu.
-
Ŵelengani ndime ili munsi mwa funsolo.
-
Ŵelengani malemba olembedwa mopendeketsa, ndipo funsani mafunso mwaluso kuti muthandize mwininyumba kuzindikila mmene malembawo akuyankhila funsolo.
-
Ngati pali ndime ina munsi mwa funso limenelo, tsatilaninso malangizo amene alembedwa pa 2 ndi 3 pamwambapa. Ngati pa jw.org pali vidiyo yogwilizana ndi funsolo, mungaonetse mwininyumba vidiyoyo mkati mwa phunzilo lanu.
-
Pofuna kutsimikizila kuti mwininyumba wamvetsetsa mfundo imene mwakambilana, mufunseninso funso lili m’zilembo zakuda.