Alandila mlongo amene wayambanso kubwela ku Nyumba ya Ufumu

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO April 2017

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a citsanzo oseŵenzetsa pogaŵila Galamukani! ndi mfundo yokhudza Ufumu wa Mulungu. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo pokonza ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Lolani Kuti Yehova Aumbe Maganizo na Khalidwe Lanu

Woumba Wamkulu amaumba makhalidwe athu akuuzimu, koma tifunika kucita mbali yathu.

UMOYO WACIKHRISTU

Alandileni Bwino

Aliyense amene wabwela pa misonkhano ayenela kuonetsedwa cikondi. Kodi mungacite ciani kuti pa Nyumba ya Ufumu pakhale malo acikondi ndi aubwenzi?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kodi Muli na “Mtima Wodziŵa” Yehova?

Mu Yeremiya caputa 24, Yehova Mulungu anayelekezela anthu ndi nkhuyu. N’ndani anali monga nkhuyu zabwino, ndipo tingatengele bwanji citsanzo cawo?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mukhoza Kulimbikitsa Mkhristu Wozilala

Ozilala amakhalabe amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu. Tingawathandize bwanji kubwelela mumpingo?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya

Yeremiya analosela kuti Yerusalemu adzasakazidwa. N’ciani cinam’thandiza kukhalabe wolimba mtima?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo za Ufumu Zimathandiza Kukhala Wolimba Mtima

Kuimba nyimbo za Ufumu kunalimbikitsa Akhristu pamene anali mndende ya Sachsenhausen. Nyimbo zimenezi zingatilimbikitse tikamakumana na ziyeso.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Yehova Ananenelatu za Pangano Latsopano

Kodi pangano latsopano lisiyana bwanji ndi pangano la Cilamulo, ndipo mapindu ake ni a muyaya m’njila yanji?