Numeri 34:1-29

  • Malire a dziko la Kanani (1-15)

  • Amuna amene anawapatsa ntchito yogawa malo (16-29)

34  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2  “Upereke malangizo awa kwa Aisiraeli: ‘Awa ndi malire a dziko la Kanani, dziko limene ndidzakupatseni kuti likhale cholowa chanu.+ 3  Malire a dziko lanu mbali yakumʼmwera adzayambire kuchipululu cha Zini, malire ndi Edomu. Malire anu akumʼmwera, mbali yakumʼmawa, adzayambire kumene Nyanja Yamchere* yathera.+ 4  Malirewo adzakhota nʼkukadutsa kumʼmwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, nʼkukathera kumʼmwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ nʼkukafika ku Azimoni. 5  Ndiyeno kuchokera ku Azimoni, malirewo akalowere kuchigwa cha Iguputo* mpaka kukathera ku Nyanja Yaikulu.*+ 6  Malire anu a mbali yakumadzulo akakhale gombe la Nyanja Yaikulu.* Amenewa akakhale malire anu a mbali yakumadzulo.+ 7  Malire anu akumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+ 8  Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo mpaka kukafika ku Lebo-hamati,*+ ndipo malirewo akathere ku Zedadi.+ 9  Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka kukathera ku Hazara-enani.+ Malire anu a mbali yakumpoto akakhale amenewa. 10  Ndiyeno mukalembe malire anu a kumʼmawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu. 11  Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kumʼmawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akadutse pamalo otsetsereka akumʼmawa kwa Nyanja ya Kinereti.*+ 12  Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndi limene lidzakhale dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’” 13  Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti: “Limeneli ndi dziko limene ligawidwe kwa inu pogwiritsa ntchito maere kuti likhale cholowa chanu.+ Lidzagawidwa kwa inu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kuti liperekedwe kwa mafuko 9 ndi hafu. 14  Fuko la Rubeni potengera mabanja a makolo awo, fuko la Gadi potengera mabanja a makolo awo komanso hafu ya fuko la Manase, analandira kale cholowa chawo.+ 15  Mafuko awiri ndi hafuwo analandira kale cholowa chawo kudera lakumʼmawa kwa Yorodano, moyangʼanizana ndi Yeriko.”+ 16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17  “Amuna amene akakugawireni malo kuti akhale cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni. 18  Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse kuti akathandize kugawa malowo kuti akhale cholowa chanu.+ 19  Amunawo mayina awo ndi awa: pa fuko la Yuda,+ Kalebe+ mwana wa Yefune, 20  pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi, 21  pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni, 22  pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili, 23  pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi, 24  pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana, 25  pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki, 26  pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani, 27  pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi, 28  ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.” 29  Amenewa ndi amuna amene Yehova anawalamula kuti akagawe malo kwa Aisiraeli mʼdziko la Kanani.+

Mawu a M'munsi

^ Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
^ Kapena kuti, “kukhwawa la Iguputo.”
^ Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
^ Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
^ Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
^ Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti, kapena kuti Nyanja ya Galileya.