Numeri 10:1-36

  • Malipenga asiliva (1-10)

  • Anachoka ku Sinai (11-13)

  • Dongosolo la kayendedwe (14-28)

  • Hobabu anapemphedwa kuti alondolere njira Aisiraeli (29-34)

  • Pemphero limene Mose anapereka ponyamuka (35, 36)

10  Kenako Yehova anauza Mose kuti: 2  “Upange malipenga awiri+ asiliva. Uchite kusula, ndipo uziwagwiritsa ntchito poitanitsa msonkhano komanso posamutsa msasa. 3  Akaliza malipenga onse awiriwo, gulu lonse lizibwera kwa iwe pakhomo la chihema chokumanako.+ 4  Koma akaliza lipenga limodzi lokha, akuluakulu amene ndi atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, azibwera kwa iwe.+ 5  Mukaliza lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmawa+ azinyamuka. 6  Mukaliza kachiwiri lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmwera+ azinyamuka. Gulu lililonse likamanyamuka, aziliza lipenga lolira mosinthasintha. 7  Poitanitsa msonkhano wa anthu onse muziliza lipenga,+ koma osati lolira mosinthasintha. 8  Ana a Aroni, omwe ndi ansembe, ndi amene aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kuti muzigwiritsa ntchito malipengawa mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 9  Ngati mukufunika kumenya nkhondo mʼdziko lanu polimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipengawo+ posonyeza kuti mukuitanira asilikali kunkhondo. Mukatero, Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndipo adzakupulumutsani kwa adani anuwo. 10  Komanso pa nthawi ya zisangalalo+ zanu, monga pa zikondwerero+ zanu ndi kumayambiriro kwa miyezi, muziliza malipenga popereka nsembe zanu zopsereza+ ndi zamgwirizano.+ Kulira kwa malipengawo kudzachititsa kuti Mulungu akukumbukireni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”+ 11  Tsopano mʼchaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20 la mweziwo,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12  Choncho Aisiraeli ananyamuka mʼchipululu cha Sinai potsatira dongosolo lawo lonyamukira,+ ndipo mtambowo unakaima mʼchipululu cha Parana.+ 13  Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke motsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.+ 14  Choncho, gulu la mafuko atatu la ana a Yuda ndi limene linali loyamba kunyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 15  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Isakara anali Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 16  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Zebuloni anali Eliyabu,+ mwana wa Heloni. 17  Chihema chitapasulidwa,+ ana a Gerisoni+ ndi ana a Merari,+ amene ankanyamula chihemacho, ananyamuka. 18  Kenako, gulu la mafuko atatu la ana a Rubeni linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 19  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Simiyoni anali Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 20  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Gadi anali Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli. 21  Kenako Akohati, amene ankanyamula zinthu za mʼmalo opatulika+ ananyamuka, kuti akamakafika akapeze chihema chitamangidwa kale. 22  Ndiyeno gulu la mafuko atatu la ana a Efuraimu linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elisama,+ mwana wa Amihudi. 23  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Manase anali Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 24  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Benjamini anali Abidana,+ mwana wa Gidiyoni. 25  Pomaliza, gulu la mafuko atatu la ana a Dani linanyamuka potengera magulu awo.* Iwo ndi amene ankalondera kumbuyo kwa magulu onse a mafukowo. Mtsogoleri wa gululi anali Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Aseri anali Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 27  Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Nafitali anali Ahira,+ mwana wa Enani. 28  Dongosolo limene Aisiraeli ndi magulu awo* ankatsatira posamuka ndi limeneli.+ 29  Ndiyeno Mose anauza Hobabu mwana wa mpongozi wake Reueli*+ wa ku Midiyani, kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi,+ ndipo tidzakuchitirani zabwino, chifukwa Yehova analonjeza Aisiraeli zinthu zabwino.”+ 30  Koma iye anamuyankha kuti: “Ayi, sindipita nanu kumeneko. Ndibwerera kudziko lakwathu, kwa abale anga.” 31  Komabe Mose anamupempha kuti: “Chonde musatisiye, chifukwa inu mukudziwa bwino kumene tingamange msasa mʼchipululu muno, ndipo mungamatilondolere.* 32  Ngati mungapite nafe limodzi,+ madalitso amene Yehova adzatipatse inunso mudzalandira nawo.” 33  Choncho iwo ananyamuka kuphiri la Yehova,+ nʼkuyenda ulendo wa masiku atatu. Likasa+ la pangano la Yehova linali patsogolo pawo ulendo wa masiku atatu wonsewo, mpaka atapeza malo oti amangepo msasa.+ 34  Akanyamuka pamsasa masana, mtambo wa Yehova+ unkakhala pamwamba pawo. 35  Nthawi zonse Likasa likamanyamuka, Mose ankanena kuti: “Nyamukani, inu Yehova,+ adani anu abalalike. Ndipo amene amadana nanu athawe pamaso panu.” 36  Nthawi zonse likasalo likaima, iye ankanena kuti: “Bwererani inu Yehova, kwa Aisiraeli masauzande osawerengeka.”*+

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Kapena kuti, Yetero.
^ Kapena kuti, “mungakhale maso athu.”
^ Kapena kuti, “kwa Aisiraeli miyandamiyanda.”